99.The Earthquake

  1. Pamene dziko lidzagwedezeka ndi chivomerezi chomaliza
  2. Ndipo pamene nthaka idzatulutsa katundu amene ali m’kati mwake
  3. Ndipo munthu adzafunsa: “Kodi yatani?”
  4. Pa tsikuli nthaka idzaulula zonse
  5. Chifukwa Ambuye wako wayiuza kuti itero
  6. Pa tsikuli mtundu wa anthu udzadza m’magulu osiyana siyana kudzalangizidwa ntchito zawo
  7. Motero aliyense amene amachita chabwino cholemera ngati njere ya mpiru, adzachiona
  8. Ndipo aliyense amene amachita choipa cholemera ngati njere ya mpiru, adzachiona