Iwo amene sakhulupirira a m’gulu la anthu a m’Buku ndi anthu opembedza mafano, sadzasiya kusakhulupilira mpaka pamene zizindikiro zooneka zitaperekedwa kwa iwo
Mtumwi wochokera kwa Mulungu amene ali kuwerenga kuchokera pa Masamba oyera
Amene ali ndi malamulo angwiro ndi omveka bwino ochokera kwa Mulungu
Ndipo anthu okhulupirira Buku sanayambe kugawikana pakati pawo mpaka pamene zizindikiro zooneka zidaperekedwa kwa iwo
Ndipo Al-Zalzala 659 iwo sadalamulidwe koma kuti azipembedza Mulungu ndipo kuti asapembedze wina aliyense koma Iye yekha ndipo kuti adzipemphera pa nthawi yake ndi kupereka msonkho wothandiza anthu osauka. Ndipo chimenechi ndicho chipembedzo chabwino
Ndithudi iwo amene sakhulupirira amene ali pakati pa anthu a m’Buku, ndi anthu opembedza mafano, adzakhala ku moto wa ku Gahena. Iwo ndiwo oipa zedi pa zolengedwa zonse
Mphotho yawo imene ili ndi Ambuye wawo ndi kuwaika m’minda imene imathiriridwa ndi madzi ya m’mitsinje pansi pake, kumene adzakhalako nthawi zonse. Mulungu ndi wosangalala ndi iwo ndipo nawonso ndi osangalala ndi Iye. M’menemo ndi m’mene munthu oopa Mulungu adzalandirire mphotho yake