96.The Clot

  1. Werenga! M’dzina la Ambuye wako amene analenga
  2. Yemwe adalenga munthu kuchokera ku kadontho kamagazi oundana
  3. werenga! Ndipo Ambuye wako ndiye wopereka mowoolowa manja
  4. Amene anaphunzitsa ndi cholembera
  5. Anaphunzitsa munthu chimene sanali kuchidziwa
  6. Iyayi! Ndithudi, munthu amalakwa mopyola muyeso
  7. Chifukwa amaganiza kuti iye ndi oima payekha
  8. Ndithudi! Nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu
  9. Kodi mwamuona munthu amene amaletsa
  10. Kapolo pamene akupemphera
  11. Kodi mwamuona ngati iye alikutsatira chilangizo chabwino
  12. Kapena kulamulira machitidwe abwino
  13. Ndiuze ngati iye akana choonadi ndipo salabadira
  14. Kodi iye sadziwa kuti Mulungu amaona zinthu zonse
  15. Iyayi! Ngati iye sasiya, Ife tidzamududuluza pogwira tsitsi la pa mphumi pake
  16. Mphumi yabodza ndi yochimwa
  17. Ndipo mulekeni iye aitane anzake oti amuthandize
  18. Ife tidzaitana osunga Gahena
  19. Iyayi! Usamumvere iye. Gunditsa mphumi yako pansi ndipo idza pafupi ndi Mulungu