95.The Fig

  1. Pali mtengo wa mkuyu ndi mtengo wa azitona
  2. Ndi pali phiri la Sinai
  3. Ndi pali Mzinda uwu wa mtendere
  4. Ndithudi Ife tidamulenga munthu m’chikombole chabwino
  5. Ndipo tinamutsitsa kukhala wapansi zedi
  6. Kupatula amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, iwo adzalandira mphotho yosatha
  7. Kodi ndi chiyani, chimene chili kukupangitsani kukana tsiku la chiweruzo
  8. Kodi Mulungu si woweruza wabwino kuposa oweruza onse