93.The Morning Hours

  1. Pali usana
  2. Ndi pali usiku pamene ulipo
  3. Ambuye wako sadakutaye iwe ndiponso sakudana nawe ayi
  4. Ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa moyo uno
  5. Ndithudi Ambuye wako adzakupatsa, ndipo iwe chidzakukondweretsa
  6. Kodi sadakupeze iwe uli wa masiye ndipo adakupatsa malo okhala
  7. Kodi sadakupeze uli wosochera ndipo Iye adakutsogolera
  8. Kodi sadakupeze iwe waumphawi ndipo adakulemeretsa
  9. Motero iwe usapondereze pansi mwana wa masiye
  10. Ndipo usapirikitse munthu wopempha
  11. Koma lengeza chisomo cha a Ambuye wako