8.The Spoils of War

  1. Iwo akukufunsa iwe za katundu amene mumapeza mukamenya nkhondo. Nena: “Mwini wake wa katundu uyu ndi Mulungu ndi Mtumwi. Motero muopeni Mulungu ndipo yanjanani pakati panu ndipo mverani Mulungu ndi Mtumwi wake ngati inu ndinu okhulupirira.”
  2. Okhulupirira enieni ndi okhawo, amene ngati dzina la Mulungu litchulidwa, amachita mantha m’mitima mwawo ndipo pamene mavesi ake awerengedwa kwa iwo, iwo amaonjezera chikhulupiriro chawo ndipo amaika chikhulupiriro chawo mwa Ambuye wawo
  3. Amene amapitiriza mapemphero ndipo amapereka mwaulere gawo lina la zinthu zimene tawapatsa
  4. Iwo ndiwo amene ali okhulupirira enieni. Kwa iwo kuli maudindo olemekezeka amene ali ndi Ambuye wawo ndiponso chikhululukiro ndi mphotho yolemekezeka
  5. Monga momwe Ambuye wako adakutulutsa m’nyumba yako ndi choonadi ndipo, ndithudi, gulu lina la okhulupirira sadakondwe ndi icho
  6. Kutsutsana ndi iwe pa choonadi chimene chinadza ngati kuti iwo anali kuperekedwa ku imfa pamene iwo anali kuona
  7. Ndi pamene Mulungu adalonjeza gulu lina pakati pa magulu awiri, ilo ndi lanu ndipo inu mudakonda kuti mukhale ndi gulu lija lopanda zida koma Mulungu adafuna kukwaniritsa chilungamo ndi mawu ake ndi kudula maziko ya anthu osakhulupirira
  8. Kuti choonadi chikhoza kupambana ndi kuthetsa bodza ngakhale kuti anthu osakhulupirira anali kudana nazo
  9. Ndi pamene inu mudapempha thandizo la Ambuye wanu ndipo Iye adakuyankhani: “Ine ndikuthandizani ndi angelo chikwi chimodzi m’magulumagulu otsatana.”
  10. Mulungu anafuna kukusangalatsani chabe kuti mitima yanu ikhazikike. Ndipo palibe kupambana kupatula kochokera kwa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi Wamphamvu ndi Wanzeru
  11. Pamene adakubweretsani inu tulo ngati mtendere kuchokera kwa Iye ndipo adakutumizirani mvula kuchokera kumwamba kuti ikutsukeni ndi kukuyeretsani ku uve wa Satana ndi kulimbikitsa mitima yanu ndi mapazi anu
  12. Pamene Mulungu ananena ndi angelo kuti: Ndithudi Ine ndili ndi inu ndipo limbikitsani anthu amene akhulupirira. Ine ndidzakhazikitsa mantha m’mitima ya anthu osakhulupirira, motero amenyeni m’makosi mwawo ndipo konkhonthani zala zawo za kumanja ndi za kumapazi
  13. Ichi ndi chifukwa chakuti iwo sanamvere Mulungu ndi Mtumwiwake. Ndipoaliyenseamenesamvera Mulungundi Mtumwi wake, ndithudi, Mulungu ndi wolanga kwambiri
  14. Ichi ndi chilango motero chilaweni ndipo, ndithudi, anthu osakhulupirira chawo ndi chilango chakumoto
  15. oh inu anthu okhulupirira! Pamene mukumana ndi magulu a nkhondo a anthu osakhulupirira musathawe
  16. Ndipo aliyense amene adzathawe patsiku limeneli kupatula ngati kuli kukonzekera nkhondo kapena kubwerera ku gulu lake, iye adzaputa mkwiyo wa Mulungu. Ndipo Gahena idzakhala mudzi wake ndipo malowa ndi oipa kukhalako
  17. Inu simunawaphe ai koma Mulungu ndiye amene anawapha. Iwe siudaponye pamene udaponya koma Mulungu ndi amene adaponya kuti akhoza kuyesa okhulupirira ndi mayesero oyenera ochokera kwa Iye. Ndithudi Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa chili chonse
  18. Ichi, ndipo ndithudi, Mulungu amafoketsa ziwembu za anthu osakhulupirira
  19. Ngati inu mufunsa chiweruzo, tsopano chiweruzo chadza kwa inu ndipo ngati inu musiya kuchita zoipa zidzakhala bwino kwa inu ndipo ngati inu mubwerera, Ifenso tidzabwerera ndipo magulu anu a nkhondo, ngakhale kuti ndi ochuluka, sadzakuthandizani china chilichonse ndipo, ndithudi, Mulungu ali kumbali ya anthu okhulupirira
  20. Oh inu anthu okhulupirira! Mverani Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo musamutaye ayi pamene inu muli kumva
  21. Ndipo musakhale ngati iwo amene amati: “Tamva”; pamene iwo sanamve
  22. Ndithudi! Zolengedwa za moyo zimene zili zoipa kwambiri pamaso pa Mulungu ndizo zimene zili zosamva, zosalankhula ndi izo zimene sizizindikira
  23. Ngakhale Mulungu akadadziwa ubwino umene uli mwa iwo, ndithudi, Iye akadawapanga kumva koma ngakhale Iye akadawapanga kuti azimva, iwo akadabwerera m’mbuyo ndi kukana choonadi
  24. oh inu anthu okhulupirira! Yankhani Mulungu ndi Mtumwi wake pamene akukuitanani ku chimene chikupatsani inu moyo ndipo dziwani kuti Mulungu amaima pakati pa munthu ndi mtima wake. Ndipo, ndithudi, nonse mudzasonkhanitsidwa kudza kwa Iye
  25. Ndipo opani mayesero amene sabwera kwa anthu oipa okha koma kwa inu nonse ndipo dziwani kuti Mulungu ndi wokhwimitsa chilango chake
  26. Ndipo kumbukirani pamene inu mudali ochepa ndipo mumaganizidwa kuti munali opanda mphamvu m’dziko ndipo mudali kuopa kuti mwina anthu akulandani. Koma Iye adakupatsani malo otetezedwa okhala ndi kukulimbikitsani ndi chithandizo chake ndipo adakupatsani zinthu zabwino kuti muzimuyamika
  27. oh inu anthu okhulupirira! Musamunyenge Mulungu ndi Mtumwi ndipo musachite chinyengo pamene muli nkudziwa pophwanya malonjezo anu
  28. Ndipo dziwani kuti chuma chanu ndi ana anu ndi mayesero ndipo kuti, ndithudi, kwa Mulungu kuli mphotho yaikulu
  29. Oh inu anthu okhulupirira! Ngati inu mumvera ndi kuopa Mulungu, Iye adzakupatsani nzeru zodziwira chabwino ndi choipa ndipo adzakukhululukirani machimo anu ndipo Mulungu ndiye Mwini chuma chochuluka
  30. Ndi mmene anthu osakhulupirira adakupangira chiwembu choti akugwire kuti ukhale mndende kapena kukupha kapena kukuchotsa m’dziko lako. Iwo amachita chiwembu koma Mulungu, nayenso amakonza chiwembu chake, ndipo Mulungu ndi wopambana pokonza chiwembu
  31. Ndipo pamene chivumbulutso chathu chilakatulidwa kwa iwo, iwo amati: “Ife tamva kale ndipo ngati ife tikanafuna, tikhoza kunena cholingana nacho. Izi si zina koma nkhani zopanda pake za anthu akale.”
  32. Ndi pamene iwo adanena kuti, “oh Ambuye! Ngati ichi ndi chivumbulutso choonadi chochokera kwa Inu, gwetsani pamwamba pathu miyala kuchokera kumwamba kapena tipatseni chilango chowawa.”
  33. Ndipo Mulungu sakadawalanga iwo pamene iwe unali pakati pawo ndipo Iye sadzawalanga pamene iwo ali kupempha chikhululukiro chake
  34. Kodi Mulungu asawalange iwo pamene iwo akhala ali kuletsa ena kuti alowe mu Mzikiti Wolemekezeka ngakhale kuti iwo alibe udindo woteteza Mzikitiwo? Palibe outeteza kupatula okhawo amene amaopa Mulungu, koma ambiri a iwo sadziwa
  35. Mapemphero awo mu Mzikiti wolemekezeka sadali china chili chonse koma miluzu ndi kuomba m’manja basi, motero lawani chilango chifukwa inu simunali kukhulupirira
  36. Ndithudi iwo amene sakhulupirira, amaononga chuma chawo ndi cholinga choletsa anthu kutsatira njira ya Mulungu. Motero iwo adzapitirira kumwaza chuma chawo; koma pomaliza iwo adzanong’oneza bombono. Ndipo adzagonjetsedwa. Ndipo iwo amene sakhulupirira adzasonkhanitsidwaku Gahena
  37. Kuti Mulunguasiyanitse pakati pa anthu oipa ndi abwino ndi kuwaika anthu oipa wina pamwamba pa mnzake, ndipo adzawaunjika onse pamodzi ndi kuwaponya ku Gahena. Awa! Ndiwo amene ali olephera
  38. Nena kwa anthu osakhulupirira kuti ngati iwo asintha njira yawo, zochimwa zawo zonse zakale zidzakhululukidwa. Koma ngati iwo apitirirabe kuchimwa, zitsanzo za anthu akale, amene Mulungu adawaononga, zikhale phunziro lawo
  39. Menyanani nawo mpaka pamene kusakhulupirira ndi kupembedza mafano kutha ndipo chipembedzo cha Mulungu chikhazikitsidwa ponseponse koma ngati iwo asiya, ndithudi Mulungu akuona zochita zawo zonse
  40. Koma ngati iwo sakumvera, dziwa kuti Mulungu ndi Mtetezi wako. Iye ndi Mtetezi wabwino ndi Mthandizi wabwino
  41. Ndipo dziwani kuti pa katundu yense amene mupeza pa nkhondo, ndithudi gawo limodzi pa magawo asanu ndi la Mulungu ndi Mtumwi ndi abale ake ndi ana a masiye, anthu osauka ndi a paulendo, ngati inu mukhulupirira mwa Mulungu ndi m’chivumbulutso chathu chimene tidatumiza kwa kapolo wathu ndi tsiku lamayeso, tsiku limene magulu awiri a nkhondo adakumana. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse
  42. Ndi pamene inu mudali tsidya lino la dambo ndi pamene anthu osakhulupirira adali tsidya ilo ndi magareta mmunsi mwanu. Ngakhale inu mukadagwirizana za malo okumana, inu mukadalephera kukwaniritsa chipanganocho koma Mulungu adafunitsitsa kuti akwaniritse zonse zimene adalamulira kuti aliyense amene adalembedwa kuti adzaonongeka, aonongeke pamene atalandira malangizo ooneka ndipo kuti iwo amene adalembedwa kuti asafe akhale ndi moyo atalandira malangizo ooneka. Ndithudi Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa
  43. Pamene Mulungu adakuonetsam’malotoakongatigululaling’ono.Akadakhala kuti adakuonetsa iwe kuti ndi gulu lalikulu, ndithudi iwe ukadagwa mphwayi ndipo ukadavutika popereka malamulo. Koma Mulungu adakupulumutsa. Ndithudi Iye amadziwa zinthu zonse zimene zili m’maganizo mwanu
  44. Ndipamenemudakumananawo,Mulunguadakuonetsani ngati ochepa m’maso mwanu ndipo anakuonetsani iwo inu ngati ochepa m’maso mwawo kuti Mulungu akwaniritse lamulo lake, limene anakhazikitsa kale, ndipo ndi kwa Mulungu kumene zinthu zonse zimabwerera
  45. oh inu anthu okhulupirira! Ngati mukumana ndi gulu la nkhondo limbikani ndipo kumbukirani dzina la Mulungu kwambiri kuti mupambane
  46. Ndipo mverani Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo musatsutsane wina ndi mnzake chifukwa mudzakhumudwa ndi kuchita ulesi, ndipo pirirani. Ndithudi Mulungu ali pamodzi ndi anthu opirira
  47. Ndipo musakhale ngati iwo amene amachoka m’nyumba mwawo modzitukumula ndi kudzionetsera kwa anthu ndi kuwaletsa anthu kutsatira njira ya Mulungu, ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene iwo amachita
  48. Ndi pamene Satana adakometsa ntchito zawo zopusa nati, “Palibe munthu wina aliyense amene adzakugonjetsani inu lero, ndithudi ine ndidzakhala pafupi kukuthandizani inu.” Koma pamene magulu awiri a nkhondo adakumana, iye adathawa ndipo anati: “Ndithudi ine ndilibe nanu ntchito. Ndithudi ine ndaona zimene inu simungathe kuziona. Ndithudi ine ndiopa Mulungu chifukwa chilango chake ndi choopsya.”
  49. Pamene anthu a chinyengo pamodzi ndi anthu amene m’mitima mwawo mudali matenda adati: “Anthu awa ali kunyengedwa ndi chipembedzo chawo.” Koma aliyense amene aika chikhulupiriro chake mwa Mulungu, ndithudi, Mulungu ndi Wamphamvu ndi Wanzeru
  50. Iwe ukadawaona angelo pamene amachotsa mizimu ya anthu osakhulupirira! Iwo amamenya pa nkhope ndi pa misana yawo nati: “Lawani ululu wa moto wa ku Gahena.”
  51. “Ichi ndi chifukwa cha zimene manja anu adatsogoza. Ndipo ndithudi, Mulungu sapondereza akapolo ake.”
  52. Monga anthu a Farao ndi iwo amene adalipo kale, iwo adakana zizindikiro za Mulungu, ndipo Mulungu adawalanga chifukwa cha kulakwa kwawo. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu ndipo amakhwimitsa chilango
  53. Ichi ndi chifukwa chakuti Mulungu sasintha madalitso amene amapereka kwa anthu mpaka pamene iwo asintha makhalidwe awo, ndipo ndithudi, Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa
  54. Monga anthu a Farawo ndi iwo amene adalipo kale, iwo sadakhulupirire uthenga wa Ambuye wawo kotero Ife tidawaononga chifukwa cha zolakwa zawo ndipo Ife tidamiza anthu a Farawo chifukwa onse adali osalungama
  55. Ndithudi zolengedwa za moyo zimene ndi zoipitsitsa pamaso pa Mulungu ndi anthu osakhulupirira ndipo iwo sadzakhulupirira
  56. Iwo ndiwo amene iwe umapanga nawo mapangano koma iwo amaphwanya mapangano awo nthawi zonse ndipo iwo saopa Mulungu
  57. Ngati iwe uwapambana pomenyana nawo nkhondo, alange kwambiri kuti ukhoza kuthamangitsa iwo amene ali kumbuyo kwawo kuti akhoza kuphunzira
  58. Ngati iwe uopa chinyengo chochokera kwa anthu, nawenso abwezere mwawubwino machitidwe omwewo. Ndithudi Mulungu sakonda anthu aupandu
  59. Ndipo anthu osakhulupirira asaganize kuti akhoza kuthawa chilango. Ndithudi iwo sadzatha kudzipulumutsa
  60. Ndipo akonzekereni iwo mwamphamvu, mmene mungathere, kuopseza adani a Mulungu ndi adani anu ndiponso ena amene inu simuli kuwadziwa koma Mulungu amawadziwa. Ndipo chili chonse chimene mudzaononga mu njira ya Mulungu chidzabwezedwa kwa inu ndipo inu simudzaponderezedwa
  61. Koma ngati iwo afuna kukhazikitsa mtendere, nanunso khazikitsani mtendere ndipo khulupirirani mwa Mulungu. Ndithudi Iye ndi wakumva ndi wodziwa
  62. Ndipo ngati iwo afuna kukunyenga ndithudi Mulungu ndi wokwanira kwa iwe. Iye ndiye amene adakulimbikitsa pokupatsa chithandizo chake ndi anthu okhulupirira
  63. Ndipo Iye wayanjanitsa mitima yawo. Ngati iwe ukadawononga zinthu zonse za padziko lapansi iwe siukadatha kuyanjanitsa mitima yawo ayi koma Mulungu waiyanjanitsa. Ndithudi Iye ndi Wamphamvu ndi Wanzeru
  64. oh iwe Mtumwi! Mulungu ndi wokwanira kwa iwe ndi kwa anthu okhulupirira amene amakutsatira iwe
  65. oh iwe Mtumwi! Alimbikitse anthu okhulupirira kuti amenye nkhondo. Ngati pali anthu makumi awiri opilira pakati panu, iwo adzagonjetsa anthu mazana awiri; ndipo ngati pali anthu zana limodzi, iwo adzagonjetsa anthu chikwi chimodzi cha anthu osakhulupirira chifukwa iwo ndi anthu amene sazindikira
  66. Mulungu tsopano wachepetsa vuto lanu chifukwa Iye adziwa kuti pakati panu pali anthu ofoka. Motero ngati pali anthu zana limodzi opilira pakati panu iwo adzagonjetsa anthu mazana awiri, ndipo ngati pali anthu chikwi chimodzi, iwo adzagonjetsa anthu zikwi ziwiri mwachifuniro cha Mulungu. Ndipo Mulungu ali pamodzi ndi anthu opirira
  67. Sikoyenera kuti Mtumwi akhale ndi akapolo a nkhondo mpaka iye atamenya nkhondo ndi kupambana m’dziko. Inu mufuna kupeza zinthu zabwino za m’dziko lino koma Mulungu akukufunirani za m’dziko limene lili nkudza. Mulungu ndi wamphamvu ndi wanzeru
  68. Pakadakhala kuti padalibe lamulo lakale lochokera kwa Mulungu, inu mukadalangidwa kwambiri chifukwa cha zinthu zimene mwatenga
  69. Ndipo idyani zinthu zabwino zololedwa zimene mwazipeza pa nkhondo ndipo opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amakhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha
  70. o Iwe Mtumwi! Nena kwa iwo amene mwawagwira ukapolo, “Ngati Mulungu adziwa ubwino m’mitima mwanu, Iye adzakupatsani zinthu zabwino kuposa zimene mwalandidwa ndipo adzakukhululukirani machimo anu. Mulungu amakhululukira ndipo ndi Wachisoni chosatha.”
  71. Koma ngati iwo afuna kukunyenga iwe, iwo adamunyenga kale Mulungu. Motero wakupatsa iwe mphamvu kuti uwapambane iwo. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi waluntha
  72. Ndithudi iwo amene adakhulupirira ndi kusamuka ndipoanapilirandikumenyankhondondichumachawondi iwoenim’njiraya Mulungundipondiiwoameneadawasunga ndi kuwathandiza, amenewa adzakhala a bwenzi a wina ndi mnzake. Iwo amene akhulupirira koma sadasamuke mwa njira iliyonse iwe ulibe udindo pa iwo pokhapokha ngati iwo asamuka. Koma ngati iwo afuna chithandizo cha chipembedzo ndi udindo wako kuwathandiza kupatula anthu amene ali ndi pangano logwirizana pakati pa inu ndi iwo ndipo Mulungu amaona ntchito zanu zonse
  73. Ndipo anthu osakhulupirira ndi abwenzi wina ndi mnzake. Ndipo ngati inu simuchita chimodzimodzi mudzakhala chisokonezo ndi kuponderezana m’dziko ndiponso chionongeko chachikulu
  74. Ndipo iwo amene adakhulupirira ndipo adasamuka ndipo adamenya nkhondo molimbika mu njira ya Mulungu, ndi iwo amene adawasunga ndi kuwathandiza amenewo ndiwo okhulupirira enieni ndipo iwo adzalandira chikhululukiro ndi zabwino zambiri
  75. Ndipo iwo amene adakhulupirira pambuyo pake kale ndipo adasamuka ndi kumenya nkhondo pamodzi ndi iwe, iwo ndi abale ako. Koma ubale wa magazi amodzi umakhala woganiziridwa polandira katundu malinga ndi malamulo a Mulungu amene adaperekedwa. Ndithudi Mulungu amadziwa zinthu zonse