6.The Cattle

  1. Kuyamikidwa ndi kwa Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi kukhazikitsa mdima ndi kuwala, komabe anthu osakhulupirira amakhazikitsa milungu ina kuti ndi yolingana ndi Ambuye wawo
  2. Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku dothi ndipo Iye adakhazikitsa nthawi. Ndipo Iye adakhazikitsanso nthawi ina, komabe inu mumakaika
  3. Iye ndi Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi. Iye amadziwa zonse zimene mumabisa ndi zonse zimene mumaulula. Ndipo amadziwa zimene mumachita
  4. Ndipo chizindikiro sichidza kwa iwo kuchokera ku zizindikiro za Ambuye wawo, chimene iwo amachivomereza
  5. Ndithudi iwo adakana choonadi pamene chidadza kwa iwo; koma kudzadza kwa iwo nkhani za zimene adali kuchita chipongwe
  6. Kodi iwo sadaone kuti kodi ndi mibadwo ingati, iwo asanabadwe, imene Ife tidawononga imene tidakhazikitsa pa dziko kukhala ya mphamvu kwambiri kuposa inu? Ndipo timawatumizira mvula yochuluka kuchokera kumwamba ndi kuipanga mitsinje yamadzi kuyenda pansi pawo. Komabe tidawawononga chifukwa cha machimo awo ndipo tidalenganso, pambuyo pa iwo, mibadwo ina
  7. Ngakhale Ife tikadakutumizira iwe uthenga wolembedwa kale papepala kuti alikhudze ndi manja awo, anthu osakhulupirira akadanena kuti: “Ichi si china ayi koma matsenga enieni.”
  8. Iwo adati: Kodi ndi chifukwa chiyani mngelo sadatumizidwe kwa iye? Ife tikadatumiza mngelo, nkhani ikanaweruzidwa nthawi yomweyo, ndipo sakadapatsidwa mpata
  9. Ndipo ngati Ife tikadamupanga iye kukhala mngelo, ndithudi Ife tikadamupanga iye kuti azioneka ngati munthu ndipo tikadawasokoneza ndi zimene iwo adasokonezeka nazo kale
  10. Ndipo, ndithudi, Atumwi ena adasekedwa iwe usadadze, koma amene anali kuwaseka anazungulilidwa ndi zinthu zomwe iwo anali kuseka
  11. Nena: “Yendani pa dziko lapansi ndipo muone mapeto a anthu amene anakana choonadi.”
  12. Nena: “Kodi mwini wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi ndani?” Nena: “Mwini wake ndi Mulungu” ndipo Iye adadzilamula yekha kuti azionetsa chifundo. Ndipo, ndithudi, Iye adzakusonkhanitsani nonse pa tsiku la kuuka kwa akufa, tsiku lopanda chikaiko. Iwo amene asochera sadzakhulupirira
  13. Ndipo zake ndi zonse zimene zimapezeka usiku ndi usana ndipo Iye ndi Wakumva ndi Wozindikira
  14. Nena: “Kodi ine nditenge wina aliyense osati Mulungu kuti akhale Mtetezi wanga, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi? Iye ndiye amene amadyetsa pamene Iye sadyetsedwa.” Nena: “Ndithudi ine ndalamulidwa kukhala woyamba wa anthu ogonjera kwa Mulungu.” Iwe usadzakhale mmodzi wa iwo amene amapembedza mafano
  15. Nena: “Ine ndikuopa, ngati nditanyoza Ambuye wanga, chilango cha tsiku lalikulu.”
  16. Aliyense amene adzapulumutsidwa ku mazunzo a tsiku limeneli adzakhala atalandira chifundo cha Mulungu. Kumeneko ndiko kudzakhala kupambana kwenikweni koonekeratu
  17. Ndipo ngati Mulungu akupatsa mavuto, palibe wina amene angachotse mavutowo koma Iye yekha; ndipo ngati Iye akupatsa zinthu zabwino, Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
  18. Iye ali ndi mphamvu pa akapolo ake ndipo Iye ndiye Wanzeru ndi Wodziwa zonse
  19. Nena: “Kodi ndi chiani chili chachikulu mu umboni?” Nena: “Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi inu. Buku la Korani lavumbulutsidwa kwa ine kuti ndikuchenjezeni inu ndi ena onse amene angalandire chivumbulutsochi. Kodi inu mungachitire umboni kuti pali milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni?” Nena: “Ine sindingaikire umboni pa nkhani yotere.” Nena: “Iye ndi Mulungu mmodzi yekha. Ndipo, ndithudi, ine ndili kutali ndi milungu imene inu muli kupembedza powonjezera pa Iye.”
  20. Kwa iwo amene tidawapatsa Buku amamudziwa Iye mongamomweamadziwiraanaawo. Komaiwoameneataya mizimu yawo sadzakhulupirira
  21. Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amakana chivumbulutso chake? Ndithudi anthu ochita zoipa sadzapambana ayi
  22. Ndipo patsiku limene tidzawasonkhanitsa onse pamodzi, Ife tidzati kwa anthu opembedza mafano: “Kodi ali kuti mafano anu aja munkawadalira?”
  23. Iwo sadzawiringula china chili chonse koma adzati: “Tilumbira pali Mulungu, Ambuye wathu, kuti ife sitidali kupembedza mafano pambali pa Mulungu.”
  24. Taona mmene iwo ali kudzinamiza okha! Koma bodza limene anali kupeka lidzawathawira
  25. Ndipo ena a iwo amamvetsera kwa iwe koma Ife taika tchingo m’mitima mwawo kuti asazindikire ndipo m’makutu mwawo ndi mogontha ndipo iwo akaona chizindikiro chilichonse, sadzachikhulupirira ndipo amadza kwa iwe kudzatsutsana nawe, ndipo anthu osakhulupirira amati: “Ichi sichina chilichonse koma nkhani zopeka za anthu a kale kwambiri.”
  26. Ndipo iwo amaletsa anthu kumvetsera ndipo iwo amadzitalikitsa okha kwa Iye. Koma iwo sali kuwononga wina aliyense koma akudziononga okha. Koma iwo sazindikira
  27. Koma iwe ukadawaona pamene iwo adzaimitsidwe moyandikira moto! Iwo adzati: “Zikadakhala kuti tinabwezedwa! Ife sitikadakana chivumbulutso cha Ambuye wathu ndipo tikadakakhala anthu okhulupirira.”
  28. Koma zonse zimene adali kuzibisa kale zidzaonekera poyera kwa iwo. Komabe akadabwezedwa, iwo akadakabwerera ku zinthu zimene adaletsedwa. Ndithudi iwo ndi anthu a bodza
  29. Iwo adanenetsa kuti: “Kulibenso moyo wina uliwonse kupatula moyo wathu wadziko lapansi ndiponso ife sitidzaukitsidwa kwa akufa.”
  30. Ndipo iwe ukadawaona pamene ali kusonkhanitsidwa kuima pamaso pa Ambuye wawo! Iye adzati: “Kodi izi sizoona?” Iwo adzayankha: “Ndi zoona pali Ambuye wathu.” Ndipo Iye adzati: “Motero lawani chilango chifukwa inu simunali okhulupilira.”
  31. Ndithudi iwo ndi olephera kwambiri amene amakana kuti adzakumana ndi Ambuye wawo mpaka pamene ola loopsa lidza pa iwo mwadzidzidzi ndipo iwo adzafuula kuti: “Kalanga ife tidali kunyalanyaza kwambiri!” Iwo adzanyamula katundu wawo pa misana yawo ndipo zoipa kwambirizimeneadzasenza
  32. Ndipomoyowapadzikolino lapansi siuli kanthu konse koma masewera ndi nthabwala. Koma yabwino kwambiri ndi nyumba m’moyo umene uli nkudza kwa amene amaopa. Kodi simungazindikire
  33. Ife tili kudziwa kuti zonse zimene ali kunena zili kukukhumudwitsa. Sindiwe amene iwo ali kukana koma ndi chivumbulutso cha Mulungu chimene anthu ochita zoipa ali kukana
  34. Ndithudi Atumwi ena adakanidwa iwe usanadze koma iwo adapilira pa zimene adali kuwanena ndipo anazunzidwa mpaka pamene thandizo lathu lidadza kwa iwo ndipo palibe amene angasinthe chilamulo cha Mulungu. Ndithudi iwe udamva nkhani zaAtumwi
  35. Ngati uona kuti kukana kwawo kwanyanya ndipo kuti sungathe kupirira, peza ngati ungathe, njira yapansi pa nthaka kapena makwerero oti ukwere kumwamba, kuti ukhoza kuwabweretsera chizindikiro. Ngati Mulungu akadafuna, Iye akadawasonkhanitsa onse ku chilangizo choona ndipo iwe usakhale mmodzi wa mbuli
  36. Ndi okhawo amene amamva, amene adzapindula koma anthu akufa Mulungu adzawadzutsa kwa akufa ndipo kwa Iye adzabwerera
  37. Iwo amafunsa: “Kodi ndi chifukwa chiyani chizindikiro sichinadze kwa iye kuchokera kwa Ambuye wake?” Nena: “Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu zotumiza chizindikiro koma ambiri a iwo sazindikira.”
  38. Palibe chinthu cha moyo padziko lapansi kapena mbalame imene imauluka ndi mapiko ake awiri imene ndi zosiyana ndi inu. Ife sitidasiye china chilichonse m’Buku ndipo kwa Ambuye wawo iwo adzasonkhanitsidwa
  39. Koma iwo amene amakana zizindikiro zathu, ndi agonthi m’khutu ndi abububu mu mdima. Mulungu amasocheza aliyense amene Iye wamufuna ndipo amatsogolera, kunjira yoyenera, aliyense amene Iye wamufuna
  40. Nena: “Ndiuzeni, ngati chilango cha Mulungu chitadza pa inu kapena ola loopsa lidza pa inu, kodi inu mudzapempha wina amene sali Mulungu kuti akuthandizeni inu? Yankhani ngati mukunena zoona.”
  41. Iyayi! Ndi kwa Iye yekha kumene inu mumapempha ndipo ngati Iye atafuna akhoza kukuchotserani zovuta zanu, ndipo inu pa nthawi imeneyi mudzaiwala mafano anu
  42. Ndithudi Ife tidatumiza, iwe usanadze, Atumwi ku mitundu ina. Ndipo tidawagwetsera umphawi, matenda ndi matsoka ochuluka kuti akhoza kukhulupilira modzichepetsa
  43. Nanga ndi chifukwa chiyani iwo sadadzichepetse pamene mazunzo athu adadza pa iwo? Koma mitima yawo inalimba ndipo Satana adawakongoletsera zochita zawo zoipa zimene adali kuchita
  44. Ndipo pamene iwo adaiwala zimene adachenjezedwa, Ife tidawatsegulira makomo a zinthu zonse zabwino mpaka pamene adasangalala ndi zimene adapatsidwa, mwadzidzidzi Ife tidawalanga ndipo ah! Iwo adalowa m’chionongeko wokhumudwa ndi a chisoni
  45. Motero maziko a anthu ochimwa adaonongedwa. Ndipo kutamandidwa konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengezedwa zonse
  46. Nena: “Tandiuzani! Ngati Mulungu akadakulandani kumva kwanu, kuona kwanu ndi kutseka mitima yanu, kodi pali mulungu wina, woonjezera pa Mulungu weniweni, amene angakubwezereni zimenezi?” Taonani mmene tifotokozera chivumbulutso chathu ndi mmene iwo sakhulupilira
  47. Nena: “Ndiuzeni, ngati chilango cha Mulungu chitadza mwadzidzidzi kapena moonekera, kodi ndani angaonongeke kupatula anthu ochita zoipa?”
  48. Ndipo Ife sititumiza Aneneri koma kuti azikawauza anthu nkhani yabwino ndi kuwachenjeza. Motero aliyense amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, iye sadzakhala ndi nkhawa kapena kudandaula
  49. Koma iwo amene akana chivumbulutso chathu, chilango chidzawapeza chifukwa cha kusakhulupilira kwawo
  50. Nena: “Ine sindili kukuuzani kuti ndili ndi chuma cha Mulungu kapena kuti ndimadziwa zinthu zobisika kapena kuti ine ndine mngelo. Ine sinditsatira china chilichonse kupatula zokhazo zimene zavumbulutsidwa kwa ine.” Nena: “Kodi munthu wakhungu ndi munthu openya angafanane? Kodi inu simungaganize?”
  51. Ndipo achenjeze iwo amene amaopa kuti adzasonkhanitsidwa kupita kwa Ambuye wawo, amene alibe wowasamalira kapena mkhalapakati woonjezera pa Mulungu, kuti akhoza kumalewa zoipa
  52. Ndipo usawathamangitse iwo amene amapembedza Ambuye wawo m’mawa ndi madzulo pofuna chisangalalo chake. Iwe siudzaimbidwa mlandu pa zochita zawo ndipo nawonso sadzaimbidwa mlandu pa zochita zako ndipo ngati iwe uwathamangitsa udzakhala mugulu la anthu opanda chilungamo
  53. Motero ife tinawayesa ena a iwo kupyolera mwa anzawo kuti akhoza kunena, “Kodi awa ndiwo amene Mulungu wawadalitsa pakati pathu?” Kodi Mulungu sazindikira anthu othokoza
  54. Ngati atadza kwa iwe anthu amene amakhulupirira chivumbulutso chathu. Nena, “Mtendere ukhale pa inu.” Ambuye wanu adadzilamulira yekha kuti azionetsa chisoni kuti ngati wina wa inu achita choipa chifukwa chosadziwa ndipo alapa pambuyo pake ndipo achita ntchito zabwino, ndithudi Iye ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
  55. Motero Ife timafotokoza chivulumbutso chathu poyera kuti njira ya anthu ochita zoipa ionekere poyera
  56. Nena, “Ine ndaletsedwa kupembedza milungu imene inumumaipembedzapowonjezerapa Mulungu.” Nena,“Ine sindidzatsatira zilakolako zanu zachabe. Ngati nditatero ndiye kuti ndasochera ndipo ine sindikhala mugulu la anthu otsogozedwa bwino.”
  57. Nena, “Ine ndalandira umboni wokwana kuchokera kwa Ambuye wanga komabe inu muli kuukana. Ine ndilibe mphamvu yobweretsa msangamsanga chilango chimene mufuna. Chiweruzo chili m’manja mwa Mulungu yekha, Iye amanena zoona ndipo ndi yekhayo amene ali wabwino poweruza.”
  58. Nena, “Ine ndikadakhala nacho chimene mufuna mwamsanga msanga, mkangano wa pakati pa inu ndi ine ukadaweruzidwa kalekale koma Mulungu amadziwa anthu onse ochita zoipa.”
  59. Iye ali ndi makiyi a zinthu zonse zobisika, palibe wina amene azidziwa koma Iye yekha. Iye amadziwa zonse zimene zili m’nthaka ndiponso m’nyanja; ndipo lisadagwe tsamba Iye amalidziwa. Palibe mbewu mu mdima wa nthaka kapena china chilichonse cha chiwisi kapena chouma koma zonsezo zidalembedwa mu Buku looneka bwino
  60. Iye ndiye amene amachotsa mizimu yanu nthawi yausiku ndipo amadziwa zonse zimene mwachita masana ndipo amakudzutsani kuti mukwaniritse nthawi imene idaperekedwa pa moyo wanu ndipo pambuyo pake nonse mudzabwerera kwa Iye. Ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene mumachita
  61. Iye ndi wamphamvu pa akapolo ake ndipo amatumiza atetezi amene amakuyang’anirani inu mpaka pamene mmodzi wa inu imufikira imfa; Atumiki athu amachotsa moyo wake ndipo iwo sanyoza zimene alamulidwa
  62. Ndipo iwo amabwerera kwa Mulungu, Ambuye wawo woona. Ndithudi Iye ndiye muweruzi ndipo Iye ndi wachangu powerengera zochita zanu
  63. Nena, “Kodi ndani amakupulumutsani m’mavuto a pa mtunda ndi a pa nyanja ndi pamene inu mumamupempha Iye modzichepetsa ndi mwamseri, ponena kuti: ‘Ngati Iye atipulumutsa ife pa mavuto awa, ndithudi, ife tidzakhala othokoza.”
  64. Nena, “Mulungu amakupulumutsani inu ku zovuta izi ndi kumavuto ena onse, komabe inu mumapembedzabe mafano mowonjezera pa Iye.”
  65. Nena, “Iye ali ndi mphamvu yotumiza chilango chake pa inu kuchokerapamutupanukapenapansipamapazianukapena kukugawani inu kukhala m’magulu a anthu osagwirizana ndi kukulawitsani mazunzo ochokera kwa anzanu. Taonani mmene timaonetsera poyera chivumbulutso chathu kuti akhale ozindikira.”
  66. Koma anthu ako alikana ili ngakhale lili choonadi chenicheni. Nena: “Ine sindine Msungi wanu ayi.”
  67. Nkhani iliyonse ili ndi nthawi yake ndipo posachedwapa mudzazindikira
  68. Ndipo pamene iwe uwaona iwo amene amanyoza chivumbulutso chathu, usakhale nawo pamodzi mpaka pokhapokha akamba nkhani ina. Ngati satana akuiwalitsa, ndipo pambuyo pake ukumbukira usakhale mgulu la anthu ochita zoipa
  69. Iwo amene amaopa Mulungu alibe udindo pa iwo koma kungowakumbutsa kuti apewe kunyoza
  70. Apewe iwo amene amasandutsa chipembedzo chawo kukhala masewera kapena nthabwala ndipo asokonezeka ndi zokoma za moyo wa dziko lapansi. Koma achenjeze ndi ilo kuti ungadzaonongeke mzimu wawo chifukwa cha zimene udachita pamene siudzakhala ndi wousamalira kapena kuwuteteza kupatula Mulungu, ndipo ngakhale iwo apereka chuma chopepesera, sichidzalandiridwa konse. Otere ndiwo amene aonongedwa chifukwa cha zimene anachita. Iwo adzalandira zakumwa zowira ndi chilango chowawa chifukwa cha zinthu zimene sadakhulupirire
  71. Nena, “Kodi ife tizipembedza ena powonjezera pa Mulungu amene sangathe kutithandiza kapena kutiwononga ndipo kodi ife tibwerere m’mbuyo pamene Mulungu watitsogolera? Monga ngati munthu amene alodzedwa ndi Satana, kumangoyenda uku ndi uku ngakhale kuti abwenzi ake ali kumuitana kuti atsatire njira yoyenera, ponena: Bwerani kuno?” Nena, “Ndithudi utsogoleri wa Mulungu ndiwo utsogoleri weniweni ndipo Ife talamulidwa kugonjera Mulungu Ambuye wa zolengedwa zonse.”
  72. Ndi kuti muzipemphera moyenera, kumvera Mulungu ndi kumuopa Iye ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzasonkhanitsidwa
  73. Iye ndiye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi ndipo patsikuli Iye adzati: “Khala” ndipo chidzakhala. Liwu lake ndi loonadi. Wake udzakhala Ufumu pa tsiku limene lipenga lidzaombedwa. Iye amadziwa zonse zosaoneka ndi zooneka. Iye ndi wanzeru ndi wodziwa zinthu zonse
  74. Ndi pamene Abrahamu adati kwa abambo ake a Uzar: “Kodi inu muzipembedza mafano ngati milungu yanu? Ndithudi ine ndili kuona kuti inu pamodzi ndi anthu anu mwasochera moonekera.”
  75. Motero tidamuonetsa Abrahamu Ufumu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi kuti akhale mmodzi wa wokhulupirira kweniweni
  76. Ndipo pamene usiku udamukuta ndi mdima, iye adaona nyenyezi. Iye adati: “Iyo ndiyo Ambuye wanga.” Koma pamene iyo idalowa, iye adati: “Ine sindikonda zimene zimalowa.”
  77. Ndipo pamene iye adaona mwezi uli kutuluka, iye adati: “Uwo ndiwo Ambuye wanga.” Koma pamene iwo unalowa, Iye adati: “Ngati Ambuye wanga sanditsogolera ine, ndithudi, ine ndidzakhala m’gulu la anthu osochera.”
  78. Ndipo pamene adaona dzuwa lili kutuluka, iye adati: “Ili ndilo Ambuye wanga. Ndipo ilo ndi lalikulu koposa.” Koma pamene ilo lidalowa, iye adati: “oh inu anthu anga! Ine ndatalikirana ndi zimene inu mukusakaniza popembedza Mulungu.”
  79. Ndithudi ine ndayang’anitsa nkhope yanga kwa Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Ine sindine mmodzi wa iwo opembedza mafano
  80. Anthu ake adatsutsana naye ndipo iye adati: “Kodi inu mukutsutsana ndi ine za Mulungu pamene Iye wanditsogolera? Ndipo ine sindiopa mafano anu kupatula ngati Ambuye wanga atafuna chilichonse. Ambuye wanga amadziwa bwino chilichonse. Kodi inu simungakumbukire
  81. Ndipo kodi ine ndingaope bwanji milungu yanu yabodza pamene inuyo mulibe mantha pomapembedza mafano amene Mulungu sadakupatseniumboniwake? Kodindaniwamaguluawiriwa amene afuna chitetezo ngati inu mumadziwa?”
  82. Ndiwo amene ali okhulupirira ndipo sasakaniza chikhulupiriro chawo pochita ntchito zoipa, kwa iwo kuli mtendere ndipo ndi otsogozedwa
  83. Chimenechi chinali chizindikiro chathu chimene tidamupatsa Abrahamu kuti agonjetsere anthu ake. Ife timakweza wina aliyense amene tamufuna. Ndithudi Ambuye wako ndi wanzeru ndi wodziwa zinthu zonse
  84. Ndipo tidamupatsa iye Isake ndi Yakobo, aliyense tidamutsogolera ndipo iye asanadze, tidatsogolera Nowa ndipo pakati pa adzukulu wake Davide, Solomoni, Yobu, Yosefe, Mose ndi Aroni. Motero ndi mmene timalipirira anthu ochita abwino
  85. Ndi Zakariya, Yohane, Yesu, ndi Eliya, aliyense adali wangwiro
  86. Ndi Ishimayeli, Elisa, Yona ndi Loti, onsewa tidawalemekeza pakati pa zolengedwa zonse
  87. Ndiponso makolo awo, ana awo, ndi abale awo Ife tidawasankha ndi kuwatsogolera ku njira yoyenera
  88. Ichi ndi chilangizo cha Mulungu chimene amalangiza nacho aliyense amene wamufuna wa akapolo ake. Koma iwo akadatumikira milungu ina yoonjezera pa Mulungu m’modzi, ntchito zawo zonse zikadakhala zopanda phindu
  89. Awa ndi amene tidawapatsa Buku, chiweruzo ndi Utumwi. Koma ngati awa sakhulupirira mwa ilo, ndithudi Ife tawapatsa iwo amene akhulupilira mwa ilo
  90. Amenewa ndi anthu amene Mulungu adawatsogolera. Choncho tsatira chilangizo chawo. Nena, “Ine sindili kufuna malipiro chifukwa cha ntchito iyi ayi. Ili ndi chenjezo kwa zolengedwa zonse.”
  91. Iwo sadapereke ulemu woyenera Mulungu pamene adati: “Mulungu sadavumbulutse china chilichonse kwa munthu.” Nena, “Kodi ndani yemwe adavumbulutsa Buku limene Mose anabwera nalo, muuni ndi chilangizo kwa anthu onse; amene mwalemba pa mipukutu ya mapepala, kuulula zina ndi kubisa zambiri? Ndipo mudaphunzitsidwa zimene inu ndiponso makolo anu sadazidziwe ndi kale lomwe.” Nena: “Ndi Mulungu.” Ndipo asiye okha kuti abadzisangalatsa ndi nkhani zopusa
  92. Ndipo ili ndi Buku lodalitsika limene tavumbulutsa, kuchitira umboni zimene zinadza ilo lisadadze kuti uchenjeze Mzinda wa Makka ndi iwo amene amakhala mouzungulira. Iwo amene ali ndi chikhulupiriro mu zamoyo umene uli nkudza amakhulupirira ilo ndipo amasamala kwambiri m’mapemphero awo
  93. Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa iye amene amapeka bodza lonamizira Mulungu kapena amati: “Ine ndalandira chibvumbulutso pamene sichidavumbulutsidwe kwa iye chilichonse?” Kapena munthu amene amati: “Ine ndikhoza kuvumbulutsa zinthu zofanana ndi zimene Mulungu wavumbulutsa?” Ndipo iwe ukadangoona anthu ochimwa pamene ali kufa ndi pamene angelo ali kutambasula manja awo akuti: “Perekani mizimu yanu. Inu mudzalipidwa mphotho yochititsa manyazi lero chifukwa cha zimene munali kunena zabodza zokhudza Mulungu. Ndiponso inu munali kukana chivumbulutso chake mwa mwano.”
  94. “Ndipo, ndithudi, mwadza kwa Ife, nokha, monga momwe tidakulengerani inu poyamba. Inu mwasiya zonse zimene tidakupatsani kumbuyo kwanu. Ndiponso Ife sitili kuona pamodzi ndi inu zimene mumazipembedza, zija mumati ndi zofanana ndi Mulungu. Tsopano ubale wonse umene umakugwirizitsani waduka ndipo zonse zimene mumaziganizira kuti zingakuthandizeni zakuthawirani.”
  95. Ndithudi! Ndi Mulungu amene amasiyanitsa mbewu ndi khoko lake kuti imere. Iye amatulutsa chamoyo kuchokera mu chakufa ndipo ndiye amatulutsa chakufa kuchokera ku chamoyo. Ameneyo ndiye Mulungu, nanga ndi chifukwa chiyani mukusokera kusiya choonadi
  96. Iye amadzetsa kuwala kwa m’mawa. Ndipo Iye waika usiku kuti ikhale nthawi yopumula, dzuwa ndi mwezi kuti zikhale zothandiza kuwerengera; umenewo ndiwo muyeso wa Mwini mphamvu zonse ndi wodziwa chilichonse
  97. Iye ndiye amene adakulengerani nyenyezi kuti zizikutsogolerani mu mdima wa pa mtunda ndi pa nyanja. Ife tafotokoza chivumbulutso kwa anthu odziwa kwambiri
  98. Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo adakupatsani malo okhalamo ndi osungidwa. Ife ndithudi tafotokoza chivumbulutso chathu kwa anthu omvetsa
  99. Iye ndiye amene amatumiza mvula kuchokera kumwamba ndipo ndi iyo, Ife timameretsa mbewu zosiyana siyana ndipo kuchokera ku izo timatulutsa mphesi za ziwisi zimene zimabereka mbeu mothinana. Ndipo kuchokera ku mitengo ya tende kumadza zipatso za tende zotsika pansi, minda ya mphesa ndi mitengo ya mafuta ya azitona, chimanga cha chizungu, zipatso zofanana koma zosiyanasiyana. Taonani zipatso zake pamene zili kubereka, kukhwima ndi kumapsya. Ndithudi! Mu izi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira
  100. Komabe iwo amasankha majini kukhala milungu kuonjezera pa Mulungu weniweni ngakhale kuti Iye ndiye amene anawalenga ndipo amamunamizira Mulungu kuti ali ndi ana amuna ndi akazi. Ulemerero ukhale kwa Iye! Alemekezeke Iye koposa zonse zimene akunena
  101. Iye ndi Namalenga wa kumwamba ndi dziko lapansi. Kodi Iye angakhale ndi ana bwanji pamene Iye alibe mkazi? Iye adalenga zinthu zonse ndipo amadziwa chilichonse
  102. Ameneyo ndiye Mulungu, Ambuye wanu. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha, Namalenga wa zinthu zonse. Motero mpembedzeni Iye yekha. Iye ndiye wosamalira zinthu zonse
  103. Palibe amene angamuone Iye koma Iye amaona chili chonse. Iye ndiye wachifundo ndipo amadziwa zonse
  104. Ndithudi zizindikiro zonse zadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu ndipo aliyense amene aona zidzampindulira iye koma aliyense amene ali wakhungu adzalephera yekha ndipo ine sindine wokuyang’anirani
  105. Motero Ife timafotokoza chivumbulutso chathu, kuti iwo anene kuti: “Iwe waphunzira” ndi kuti tifotokoze momveka kwa anthu ozindikira
  106. Choncho tsatira zonse zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha ndipo alewe anthu osakhulupirira
  107. Ngati Mulungu akadafuna, iwo sakanapembedza mafano. Ndipo Ife sitikadakusankha iwe kukhala owayang’anira ayi ndiponso iwe sindiwe wowasamalira wawo
  108. Ndipo musatukwane iwo amene amapembedza mafano poonjezera pa Mulungu weniweni kuti mwina iwo angathe kutukwana Mulungu molakwa ndi mwa umbuli. Motero tazipanga zochita zawo kukhala zosangalatsa ndipo ndi kwa Ambuye wawo kumene onse adzabwerera ndipo Iye adzawauza iwo zonse zimene anali kuchita
  109. Ndipo iwo amalumbira pali Mulungu motsindika kuti ngati chizindikiro chitaperekedwa kwa iwo, iwo adzachikhulupirira. Nena, “Ndithudi zizindikiro zonse zili ndi Mulungu ndipo kodi inu mungadziwe bwanji ngati chidza kwa iwo kuti iwo sadzachikhulupirira?”
  110. Ndipo Ife tidzatembenuza mitima yawo ndi maso awo monga mmene adakana kukhulupirira nthawi yoyamba ndipo Ife tidzawasiya mukusochera kwawo akusowa chochita
  111. Ngakhale Ife tikadawatumizira iwo angelo ndi kupangaanthuakufakutialankhulenawondikusonkhanitsa zinthu zonse pamaso pawo, iwo sakadakhulupirirabe pokhapokha ngati Mulungu afuna koma ambiri a iwo ndi anthu osadziwa
  112. Kotero Ife tidakhazikitsa mdani kwa Mtumwi aliyense. A satana amene ali pakati pa anthu ndi majini, amene amauzana wina ndi mnzake mawu okoma ndiponso a chinyengo. Koma Ambuye wako akadafuna, iwo sakadachita zotero ayi motero asiyeni okha ndi zimene akupeka
  113. Kuti mitima ya anthu amene sakhulupirira m’moyo umene uli nkudza ipendekere kuzolankhula zawo ndipo kuti azitsatira zimene apeka okha ndi kumasangalala kuti mwina akhoza kuchita zimene ali nkuchita
  114. “Kodi ine ndifune wina woweruza oposa Mulungu pamene ndiye amene adavumbulutsa Korani kwa inu ndi malamulo ofotokozedwa bwino?” Iwo amene tidawapatsa Mau athu amadziwa kuti lidavumbulutsidwa kuchokera kwa Ambuye wako mwa choonadi. Motero usakhale mmodzi wa anthu okaika
  115. Ndipo Mau a Ambuye wako akwaniritsidwa moona ndi mwachilungamo. Palibe wina amene angasinthe Mau ake. Iye amamva ndipo ndi wozindikira chili chonse
  116. Ndipo ngati iwe umvera zonena za anthu ambiri apa dziko lapansi iwo adzakusocheza ku njira ya Mulungu. Iwo satsatira chilichonse koma nkhani zongoganiza chabe ndipo sachita china chilichonse koma kunama
  117. Ndithudi Ambuye wako! Ndiye amene amadziwa anthu onse amene amasochera ku njira yake ndiponso Iye amadziwa iwo amene atsogozedwa bwino bwino
  118. Motero idyani nyama yokhayo imene yaphedwa m’dzina la Mulungu ngati inu mukhulupiriradi mu chivumbulutso chake
  119. Kodi inu simungadye bwanji nyama imene yaphedwa m’dzina la Mulungu pamene Iye adaulula poyera zimene adakuletsani pokhapokha ngati mwasimidwa? Ndithudi ambiri amasochera potsatira zilako lako zawo mwa umbuli. Ndithudi Ambuye wako amadziwa onse oswa malamulo
  120. Pewa machimo oonekera kapena obisika. Ndithudi iwo amene amachita zoipa adzalangidwa chifukwa cha zoipa zawo
  121. Musadye nyama iliyonse imene sidaphedwe m’dzina la Mulungu chifukwa kutero ndi kulakwa. Ndithudi a Satana amaphunzitsa anthu awo kuti azikangana ndi inu ndipo ngati inu muwamvera, ndithudi, nanunso mudzakhala opembedza mafano
  122. Kodi munthu amene adafa, ndipo tamuukitsa kwa akufa ndipo wapatsidwa kuwala kumene kukhoza kumutsogolera pakati pa anthu, angafanizidwe ndi iye amene ali kusochera mumdima umene sadzatulukamo? Chomwecho zimakongoletsedwa kwa anthu osakhulupirira zimene adali kuchita
  123. Motero Ife tidakhazikitsa mu Mzinda uliwonse atsogoleri a anthu olakwa kwambiri amene amakonza njira zoswera malamulo m’kati mwa Mzindawo. Koma iwo amakonza njira zoti zibweretse chiwonongeko pa iwo eni ndipo iwo sadziwa
  124. Ndipo pamene zizindikiro ziwafikira iwo amati: “Ife sitidzakhulupirira mu ichi pokhapokha ngati tipatsidwa chimene Atumwi a Mulungu adapatsidwa.” Mulungu amadziwa bwino ndani amene akhoza kumupatsa uthenga wake. Kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi kochokera kwa Mulungu ndiponso chilango chowawa chidzadza pa anthu oipa chifukwa cha zimene anali kuchita
  125. Ndipo aliyense amene Mulungu afuna kumutsogolera, Iye amatsegula mtima wake kuti akhale Msilamu ndipo aliyense amene Iye afuna kumusocheretsa, Iye amachititsa mtima wake kukhala opapatizika ndi ovutika ngati kuti akukwera kumwamba. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaikira mkwiyo pa anthu osakhulupirira
  126. Iyi ndi njira ya Ambuye wako, yoyenera. Ife tafotokoza chivumbulutso kwa anthu oganizira
  127. Kwa iwo kudzakhala nyumba ya mtendere imene ili ndi Ambuye wawo. Iye adzakhala Mtetezi wawo chifukwa cha zimene anali kuchita
  128. Ndipo patsiku limene adzawasonkhanitsa onse, ndi kuti: “oh inu gulu la majini! Inu mudali kusokeletsa anthu mu unyinji wawo.” Ndipo anzawo ochokera m’gulu la anthu adzati: “Ambuye ife tidapindula kuchokera kwa wina ndi mnzake, koma tsopano tafika pa mapeto ya nthawi yathu imene mudatikhazikitsira ife.” Mulungu adzati: “Kumoto ndiko kumalo kwanu ndipo kumeneko mukakhala mpaka kalekale kufikira pamene Mulungu adzafuna.” Ndithudi Ambuye wako ndi Wanzeru ndi Wozindikira
  129. Ndipo motero ndi mmene timapangira anthu olakwa kuthandizana wina ndi mzake chifukwa cha zimene anali kuchita
  130. Inu gulu la majini ndi anthu! “Kodi sikudadze kwa inu Atumwi a mtundu wanu amene adali kukuuzani za zizindikiro zanga ndi kuchenjeza za kukumana kwa tsiku lanuli?” Iwo adzayankha, “Ife tidzichitira umboni wodzitsutsa tokha.” Ndi moyo wa dziko lino lapansi umene udawanyenga. Ndipo iwo adzadzichitira umboni okha kuti iwo adali osakhulupirira
  131. Ichi ndi chifukwa chakuti Ambuye wako samaononga Mizinda chifukwa cha zochita zawo, pamene anthu ake sadali kudziwa
  132. Kwa aliyense kudzaperekedwa gawo molingana ndi zimene adachita. Sikuti Ambuye wako sadziwa zimene iwo achita
  133. Ambuye wako ndi wolemera ndiponso ndi wachisoni ndipo ngati Iye afuna, akhoza kukuonongani ndi kuika m’malo mwanu ena amene Iye wafuna monga momwe Iye adakulengerani inu kuchokera ku mbeu ya anthu ena
  134. Ndithudi chimene inu mukulonjezedwa chidzachitika ndipo inu simungachizembe ayi
  135. Nena, “oh anthu anga! Chitani chimene mungachite, ndithudi, nanenso ndili kuchita chimene ndimachita ndipo inu mudzadziwa kuti ndani wa ife amene adzakhala ndi mapeto abwino m’moyo umene uli nkudza. Ndithudi anthu olakwa sadzapambana.”
  136. Ndipo iwo amaika pa mbali gawo la mbewu ndi gawo la ziweto kuti ndi za Mulungu ndipo amati: “Izi ndi za Mulungu pamene izi ndi za mafano athu.” Koma gawo limene amati ndi la mafano awo silifika kwa Mulungu ayi pamene gawo la Mulungu limafika lonse kwa mafano awo! Chiweruzo chawo ndi choipa kwambiri
  137. Motero kwa anthu opembedza mafano, mafano awo adapangitsa kupha ana awo kukhala chinthu chokondweretsa ndi cholinga chakuti awawononge iwo ndi kuwasokonezera chipembedzo chawo. Koma ngati Mulungu akadafuna, iwo sakadachita choncho. Motero asiyeni okha ndi zimene akupeka
  138. Potsatira zofuna zawo, iwo amati: “Nyama izi ndiponso mbewu izi ndi zoletsedwa ndipo palibe munthu amene adye kupatula okhawo amene tawaloleza.” Ndipo pali nyama zina zimene amaletsa anthu kuti asakwere kapena kugwira ntchito, ndi zina zimene satchulapo dzina la Mulungu komwe ndi kumunamizira Iye. Mulungu adzawalipira chifukwa cha mabodza awo amene amapeka
  139. Ndipo iwo amati: “Zam’kati zanyamazi ndi zololedwa kudyedwa ndi anthu athu amuna okha ndipo ndi zoletsedwa kwa anthu a akazi koma ngati izo zibadwa zakufa onse amagawana. Mulungu adzawalanga chifukwa cha zonse zimene amamunamizira Iye. Ndithudi Iye ndi Wanzeru ndi Wodziwa.”
  140. Ndithudi olephera ndi amene, adapha ana awo mwaumbuli ndipo adaletsa zinthu zimene Mulungu adawapatsa iwo ndi kupeka bodza lokhudza Mulungu. Ndithudi iwo asokera ndipo siotsogozedwa
  141. Iye ndiye amene amapanga minda ya mbewu za mitundumitundu; zoyanga ndi zosayanga, mitengo ya tende ndi mbeu zosiyanasiyana kukoma kwake, azitona ndi chimanga cha chizungu zofanana ndi zosiyana. Idyani zipatso zake pamene zibereka ndipo perekani chaulere chake nthawi yake. Koma musawononge ayi. Ndithudi Mulungu sakonda anthu owononga
  142. Ndipo pakati pa nyama, pali zina zonyamula katundu ndi zina zosanyamula katundu. Idyani zimene Mulungu wakupatsani ndipo musatsatire mapazi a Satana ayi. Ndithudi iye ndi mdani wooneka
  143. Tengani ng’ombe zisanu ndi zitatu, ndi nkhosa ziwiri, ndi mbuzi ziwiri. Nena, “Kodi Iye adaletsa zazimuna ziwiri kapena zazikazi ziwiri kapena ana amene ali m’mimba? Ndiyankheni mozindikira ngati mukunena zoona.”
  144. Ndipo kuchokera ku ngamira, ziwiri ndi ng’ombe ziwiri. Nena, “Kodi Iye adaletsa zazimuna ziwiri kapena zazikazi ziwiri kapena ana amene ali m’mimba mwawo? Kodi mudalipo pamene Mulungu adakupatsani malamulo awa? Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ndi kusocheretsa anthu popanda kuzindikira? Ndithudi Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa.”
  145. Nena, “Ine sindipeza china chilichonse mu zimene zavumbulutsidwa kwa ine choletsa aliyense kudya chakudya china chilichonse kupatula nyama yofa yokha kapena liwende kapena nyama ya nkhumba, chifukwa zimenezo ndi zauve ndi zodetsedwa kapena nyama ina iliyonse imene yaphedwa osati mu dzina la Mulungu. Koma aliyense amene waumirizidwa kudya chilichonse cha izi, osati mokondweretsedwa kapena ndi cholinga chofuna kuswa malamulo, ndithudi, Ambuye wako ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha.”
  146. Ife tidawaletsa Ayuda kudya nyama zonse zosabsyukula ndipo tinawaletsa mafuta a ng’ombe ndi a nkhosa kupatula amene ali pa msana ndi m’matumbo kapena amene adasakanizika ndi mafupa. Motero tidawapatsa chilango chifukwa cha kulakwa kwawo. Ndithudi Ife tili kunena zoonadi
  147. Ngati iwo akukunamizani, nena, “Ambuye wanu ndi Mwini chifundo chosatha koma mkwiyo wake siungachotsedwe pa anthu ochita zoipa.”
  148. Anthu opembedza mafano adzati: “Mulungu akadafuna, ife kapena makolo athu, sitikadatumikira milungu ina yoonjezera pa Iye ndipo ife sitikadaletsa china chilichonse.” Mmenemu ndi mmene anthu amene adalipo kale adanamira mpaka pamene analawa mkwiyo wathu. Nena, “Kodi inu muli ndi umboni uliwonse umene mungatisonyeze Ife?” Ndithudi inu simutsatira china koma zinthu zongoganiza ndiponso simuchita china chilichonse koma bodza basi
  149. Nena, “Ndi Mulungu yekha amene ali ndi umboni weniweni ndipo Iye akadafuna akadakutsogolerani nonse.”
  150. Nena, “Bweretsani mboni zanu zonse zimene zikhoza kuchitira umboni kuti Mulungu adakuletsani izi. Ngati iwo apereka umboni, iwe usapereke umboni wako. Ndipo usatsatire zilakolako za iwo amene amati chivumbulutso chathu ndi chabodza, amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza ndipo amapanga milungu ina kukhala yofanana ndi Ambuye wawo.”
  151. Nena, “Bwerani! Ine ndikuwerengerani zimene Ambuye wanu wakulamulani inu kuti musachite. Musapembedze milungu ina yowonjezera pa Iye; Muzionetsa chifundo kwa makolo anu; musaphe ana anu chifukwa chaumphawi, Ife timakudyetsani inu pamodzi ndi iwo; musayandikire zinthu zoipa zimene zili zoonekera kapena zili zobisika ndipo musaphe munthu amene Mulungu waletsa pokhapokha ngati pali chifukwa choyenera.” Ichi wakulamulani inu kuti muzindikire
  152. “Ndipo musayandikire chuma cha ana a masiye kupatula m’njira yabwino yowakonzera tsogolo lawo mpaka pamene iwo akula msinkhu. Kwaniritsani muyeso woyenera ndipo muyese mwachilungamo. Ife sitinyamulitsa munthu wina aliyense katundu wolemera amene iye sangathe kunyamula. Ndipo mukamalankhula, muzilankhula mwachilungamo ngakhale kuti nkhanizo zikhudza abale anu ndipo kwaniritsani malonjezo a Mulungu. Ichi wakulamurani inu kuti mudzikumbukira.”
  153. Ndithu iyi ndi njira yanga yoyenera motero itsatireni ndipo musatsatire njira zina zake chifukwa izo zidzakusocheretsani inu ku njira yake. Ichi Iye wakulamulani kuti mukhale angwiro
  154. Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku, kumaliza ubwino wathu kwa aliyense wochita zabwino ndiponso lofotokoza chinthu chilichonse, ulangizi ndi chisomo kuti akhulupirire mukukumana kwawo ndi Ambuye wawo
  155. Ili ndi Buku lodalitsika limene talivumbulutsa, motero opani Mulungu kuti mulandire chisomo
  156. Kuti inu musadzanene kuti: “Buku lidangovumbulutsidwa ku magulu awiri pambuyo pathu, ndipo ife sitidadziwe zimene adali kuwerenga.”
  157. Kapena mukhoza kudzanena kuti: “Buku la Mulungu likanavumbulutsidwa kwa ife, ndithudi, tikadalangizidwa bwino kuposa iwo.” Ndithudi chizindikiro chosakaikitsa chadza tsopano kuchokera kwa a Ambuye wanu; chilangizo ndi madalitso. Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene akana chivumbulutso cha Mulungu ndipo safuna kuchitsatira? Ife tidzawalipira onse amene amakana zizindikiro zathu ndi chilango chowawa chifukwa chokana kwawo
  158. Kodi iwo ali kudikira wina kupatula angelo kuti adze kwa iwo kapena kuti Ambuye wako adze kapena zina mwa zizindikiro za Ambuye wako zidze? Tsiku limene zina mwa zizindikiro za Ambuye wako zidzadza, chikhulupiriro sichidzathandiza mzimu umene unalibe chikhulupiriro kale kapena umene siudagwiritse ntchito bwino chikhulupiriro. Nena, “Dikirani! Nafenso tili kudikira.”
  159. Ndithudi iwo amene apatukana m’chipembedzo ndi kupanga mipingo yosiyanasiyana, iwe sizikukhudza zimenezo. Nkhani yawo adzathetsa ndi Mulungu ndipo Iye adzawauza zomwe amachita
  160. Aliyense amene amachita ntchito yabwino adzalipidwa magawo khumi olingana ndi iyo ndipo aliyense amene amachita zoipa adzalandira choipa chomwecho ndipo iwo sadzaponderezedwa ayi
  161. Nena, “Ndithudi Ambuye wanga wanditsogolera ine ku njira yoyenera, ku chipembedzo changwiro, chikhulupiriro cha Abrahamu wangwiro chifukwa Abrahamu sadali mmodzi wa anthu opembedza mafano.”
  162. Nena, “Ndithudi mapemphero anga, nsembe yanga, moyo wanga ndi imfa yanga zonse zili m’manja mwa Mulungu Ambuye wazolengedwa zonse.”
  163. Iye alibe wothandizana naye. Pa izi ine ndalamulidwa ndipo ine ndine woyamba wa iwo ogonjera malamulo a Mulungu
  164. Nena, “Kodi ine ndifune Ambuye wina osati Mulungu pamene Iye ndi Ambuye wa zinthu zonse? Munthu aliyense adzakolola zipatso za ntchito yake ndipo palibe mzimu umene udzanyamula katundu wa wina wake. Pomaliza nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu; ndipo Iye adzakuuzani zomwe munali kutsutsana.”
  165. Ndipo ndiye amene anakulengani kukhala mibadwo yodza pambuyo pa mibadwo yina, kulowa m’malo mwa uzake padziko lapansi. Ndipo anakukwezani m’maudindo, ena kuposa anzawo kuti akhoza kukuyesani ndi zimene wakupatsani. Ndithudi Ambuye wanu ndi wachangu polanga koma ndithudi Iye amakhululuka, Mwini chisoni chosatha