23.The Believers

  1. Anthu okhulupirira ndiwo opambana
  2. Iwo amene amadzichepetsa akamapemphera
  3. Ndi iwo amene amalewa nkhani zabodza
  4. Ndipo amapereka zaulere kwa anthu osauka
  5. Ndi iwo amene amadziteteza ku chiwerewere
  6. Kupatula kwa akazi awo kapena akapolo awo akazi, chifukwa iwo sangadzudzulidwe
  7. Koma amene angafune zina pamwamba pa zimene tawaloleza anthu otere ndi ochimwa
  8. Amene amakwaniritsa malonjezo ndi mapangano awo
  9. Ndi iwo amene amasunga mapemphero awo
  10. Amenewa ndithudi ndiwo amene adzalowa
  11. Iwo adzalowa ku Paradiso ya pamwamba ndipo adzakhalamo mpaka kalekale
  12. Ndithudi Ife tidapanga munthu kuchokera ku dothi labwino
  13. Titatero tidamukonza iye kukhala dontho la umuna m’malo otetezedwa mu msana
  14. dontho la umunali tidalipanga kukhala dontho la magazi ndipo dontho lamagazili tidalipanga kukhala m’bulu wa mnofu. Ndipo mnofu umenewu tidaukonza kukhala mafupa ndipo tidakuta mafupa ndi mnofu. Kotero tidamupanga iye kukhala chilengedwe china. odalitsa akhale Mulungu, Namalenga wabwino kwambiri mwa onse
  15. Ndipo pambuyo pake inu nonse mudzafa
  16. Ndipo mudzapatsidwanso moyo patsiku la kuuka kwa akufa
  17. Ife tidalenga miyamba isanu ndi iwiri pamwamba panu ndipo kwa zolengedwa zathu. Ndipo Ife sitikhala osalabadira ayi
  18. Ife timatumiza madzi kuchokera kumwamba m’muyeso wokwana ndipo timawalowetsa pansi pa nthaka. Ndipo Ife tili ndi mphamvu yowachotsa madziwo
  19. Ndipo Ife timakutulutsirani mmenemo minda ya tende ndi mphesa, m’mene muli zipatso zanu zambiri zimene zina mwa izo mumadya
  20. Mtengo umene umamera pa phiri la Sinai, umapereka mafuta ndiponso ndiwo kwa anthu
  21. M’nyama namonso muli chizindikiro choonetsa mphamvu zathu. Inu timakumwetsani zimene zili m’mimba mwake ndipo mumadya nyama yake ndiponso mumapeza phindu lambiri
  22. Ndipo pa izo ndi m’zombo zimene zimayenda pa nyanja, inu mumanyamulidwa
  23. Tidamutumiza Nowa kwa anthu ake ndipo iye adati, “Tumikirani Mulungu anthu anga chifukwa mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Iye?”
  24. Akuluakulu osakhulupirira a anthu ake adati, “Munthu uyu ndi wolingana ndi inu, iye ali kungodziyenereza kuti ndi wopambana pakati panu.” Mulungu akadafuna, akadatumiza angelo. Ndiponso zinthu za mtundu uwu sitidamvepo kuchokera kwa makolo athu akalekale
  25. Ndithudi ameneyu ndi wopenga, ndipo mumuyang’anire pa kanthawi.”
  26. Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kundikana.”
  27. Ife tidavumbulutsa chifuniro chathu kwa iye ponena kuti, “Khoma chombo chimene Ife tidzayang’anira molingana ndi chilangizo chathu. Pamene chiweruzo chathu chidza ndipo madzi asefukira kuchokera ku ng’anjo, utenge zolengedwa ziwiriziwiri, zazimuna ndi zazikazi ndiponso kuchokera kwa iwo a m’nyumba mwako kupatula okhawo amene adanenedwa kuti adzaonongeka. Usandipemphe kuti ndipulumutse iwo amene adachita zoipa chifukwa iwo adzamizidwa.”
  28. Ndipo pamene iwe ndi iwo amene akutsata iwe mulowa m’chombo, nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu amene watipulumutsa ife kuchoka ku mtundu wa anthu oipa.”
  29. Ndipo nena: “Ambuye wanga! Ndithandizeni kuti ndikafike pamalo podalitsika chifukwa Inu ndinu wabwino wa onse amene amafikitsa pamalo okocheza.”
  30. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro zooneka. Ndithudi Ife timawaika anthu m’mayesero
  31. Potero Ife tidapanga mtundu wa anthu a tsopano pambuyo pawo
  32. Ndipo tidatumiza kwa iwo Mtumwi wa mtundu wawo amene adati, “Tumikirani Mulungu chifukwa inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Mulungu?”
  33. Koma akuluakulu a anthu osakhulupirira a anthu ake, amene adakana za moyo umene uli nkudza ndi amene tidawapatsa zinthu zabwino za m’moyo uno adati, “Munthu uyu ndi munthu monga inu nomwe amene akudya zimene mumadya inu ndi kumwa zimene inu mumamwa.”
  34. “Ngati inu mumvera munthu wonga inu nomwe, ndithudi, inu mudzatayika.”
  35. “Kodi iye ali kukuopsezani kuti pamene inu mutafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa mudzadzuka ndi kukhalanso ndi moyo?”
  36. “Zimene inu muli kuopsezedwa nazo zili kutali.”
  37. “Kulibenso moyo wina koma moyo wathu wapadziko lapansi basi. Ife timafa ndi kukhala ndi moyo ndipo ife sitidzadzukanso ayi.”
  38. “Munthu uyu ndi odziyenereza amene ali kunena za Mulungu zimene sizili zoona ayi. Ife sitidzamukhulupirira.”
  39. Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kunditsutsa.”
  40. Iye adati, “Posachedwapa iwo adzanong’oneza bombono.”
  41. Chilango chathu chidawapeza mwachilungamo ndipo tidawafafaniza monga zinyalala. Chionongeko kwa anthu onse ochimwa
  42. Atapita awa tidalenganso mitundu ina ya anthu
  43. Palibeanthuameneangafulumizitsekapenakuchedwetsa chionongeko chawo
  44. Ndipo Ife tidatumiza Atumwi ena motsagana ndipo nthawi iliyonse Mtumwi amadza kwa iwo ndipo amamukana nati ndi wabodza. Ndipo Ife tidawaononga ena pambuyo pawo ndipo tidawapanga iwo kukhala chitsanzo cha mbiri ya anthu olakwa. Ichi chidali chionongeko cha anthu osakhulupirira
  45. Ndipo Ife tidamutumiza Mose pamodzi ndi m’bale wake Aroni ndi zizindikiro ndiponso ulamuliro wathu
  46. Kwa Farawo ndi nduna zake ndipo iwo adawalandira mwamwano chifukwa iwo adali anthu a chipongwe
  47. Ndipo iwo adati, “Kodi ife tikhulupirire anthu awiri olingana ndi ife amene anthu awo ndi akapolo athu?”
  48. Iwo adawakana iwo kotero iwo adalandira chionongeko
  49. Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku la Chipangano Chakale kuti anthu ake akhoza kutsogozedwa bwino
  50. Ife tidamupanga mwana wamwamuna wa Maria pamodzi ndi amayi ake kukhala chizindikiro kwa anthu onse ndipo tidawapatsa mnthunzi pa malo okwera ndi malo a mtendere amene anali kuthiriridwa ndi madzi a pa kasupe
  51. Oh Atumwi! Idyani zinthu zabwino ndipo muzichita ntchito zabwino. Ndithudi Ine ndimadziwa zonse zimene mumachita
  52. Ndithudi chipembedzo chanu ndi chimodzi ndipo Ine ndine Ambuye wanu. Kotero ndiopeni Ine
  53. Koma anthu adagawanika m’magulu osiyanasiyana, gulu lililonse limasangalala ndi ziphunzitso zawo
  54. Alekeni ayambe achimwa mpaka pamene imfa iwapeza
  55. Kodi iwo amaganiza kuti popeza tawapatsa chuma ndi ana
  56. Ndiye kuti Ife tili kuwafunira zabwino? Iyayi. Iwo sadziwa kanthu ayi
  57. Ndithudi iwo ndi anthu amene amaopa Ambuye wawo
  58. Amene amakhulupirira zizindikiro za Ambuye wawo
  59. Amene sapembedza wina aliyense poonjezera pa Ambuye wawo
  60. Amene amapereka chaulere mitima ili yoopa Ambuye wawo chifukwa chakuti adzabwerera kwa Iye
  61. Awa ndiwo amene amapikisana wina ndi mnzake pochita zabwino ndipo amakhala oyamba pozindikira
  62. Ife sitinyamulitsa mzimu wina uliwonse katundu amene iwo sangathe kunyamula. M’buku lathu mudalembedwa zoona zokhazokha. Ndipo palibe munthu amene adzaponderezedwa
  63. Koma mitima ya anthu osakhulupirira siyizidziwa zimenezi ayi. Iwo ali ndi ntchito zina zoipa kupatula zimene iwo amachita
  64. Koma pamene chilango chathu chidza pa iwo amene amakhala mu mtendere, iwo adzafuula kufuna chithandizo
  65. Musalire tsiku la lero chifukwa inu simudzalandira chithandizo china chilichonse kuchokera kwa Ife
  66. Chivumbulutso changa chinali kulakatulidwa kwa inu nthawi zambiri koma inu munali kuthawa ndi kuchikana mwamwano
  67. Inu mumachinyoza usana ndi usiku uliwonse
  68. Kodi iwo sangathe kulingalira mozama pa mawu a Mulungu kapena pali china chake chimene chidavumbulutsidwa kwa iwo chimene sichidavumbulutsidwe kwa makolo awo
  69. Kapena iwo sadziwa kuti akukana Mtumwi wawo
  70. Kapena iwo akuti Iye ndi wopenga? Koma iye wawabweretsera iwo onse zoonadi. Koma ambiri amakana choonadi
  71. Kukadakhala kuti choonadi chimatsatira zofuna zawo, ndithudi, kumwamba, dziko lapansi ndi onse okhala m’menemo akadaonongeka. Ife tawapatsa chikumbutso komabe iwo safuna kumvera chikumbutsocho
  72. Kapena iwe uli kuwapemphera mphotho? Chithandizo cha Ambuye wawo ndicho chabwino. Ndipo Iye ndiye wopereka moolowa manja kuposa onse amene amapereka
  73. Ndithudi iwe uli kuwaitana kuti adze kunjira yoyenera
  74. Ndithudi iwo amene amakana moyo umene uli nkudza adzakhala ali kusochera ku njira yoyenerayi
  75. Ngati Ife tikadawalangiza chisoni chathu ndi kuwachotsera mavuto, iwo akadakhala ali kulakwabe m’njira zawo zoipa ndi kusokonezeka ndi zoipazo
  76. Ndithudi tidawalanga kale koma iwo sadafunefune Ambuye wawo kapena kukhala odzichepetsa pamaso pake
  77. Mpaka pamene tidzawatsekulira khomo la chilango chowawa, iwo adzakhala okhumudwa
  78. Iye ndiye amene adakupatsani makutu, maso ndi mitima. Komabe inu simuthokoza mokwanira
  79. Iye ndiye amene adakulengani ndi kukuchulukitsani padziko lapansi ndipo nonsenu mudzasonkhanitsidwa kudza pamaso pake
  80. Iye ndiye amene amapereka moyo ndiponso imfa ndipo ndi Iyenso amene amasithanitsa usiku ndi usana. Kodi simungazindikire
  81. Iwo amanena zimene anthu akale ankanena
  82. Iwo amati, “Pamene ife tafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa, kodi tidzadzukanso ndi kukhala ndi moyo?”
  83. Ndithudi ife tidalonjedzedwa zimenezi kale pamodzi ndi makolo athu. Izi si zina ayi koma nkhani zabodza za anthu a makedzana
  84. Nena, “Kodi Mwini wake wa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo ndani? Ndiuzeni ngati mumudziwa.”
  85. Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Kodi inu simungachenjezedwe?”
  86. Nena, “Kodi Ambuye wa miyamba isanu ndi iwiri ndiponso Mwini Ufumu ndani?”
  87. Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Nanga kodi simungasiye kuchita zoipa?”
  88. Nena, “Kodi ulamuliro wa zinthu zonse zili m’manja mwa yani? Kodi ndani amene amaziteteza zonse pamene Iye safuna chitetezo cha wina aliyense ngati inu mukudziwa?”
  89. Iwo adzati, “M’manja mwa Mulungu.” Nena, “Nanga ndi chifukwa chiyani inu mwanyengedwa?”
  90. Iyayi, Ife tawavumbulutsira choonadi. Koma onsewa ndi anthu abodza
  91. Palibe nthawi imene Mulungu adabala mwana ndipo kulibe Mulungu wina woonjezera pa Iye. Ngati izi zikadakhala choncho, bwezi Mulungu aliyense akumatenga zolengedwa zake zokha ndi kumaziika pamwamba pa zolengedwa za Mulungu wina. Ulemerero ukhale kwa Mulungu woposa zina zilizonse
  92. Iye amadziwa zonse zooneka ndiponso zobisika. Mulungu akhale wopambana milungu ina imene iwo amaitumikira
  93. Nena, “Ambuye wanga! Ngati Inu mukadandionetsa chilango chimene muli kuwopseza
  94. Ambuye wanga! Pulumutsani ndipo musandisiye ine pakati pa mtundu wa anthu oipawu.”
  95. Ndithudi, Ife tili ndi mphamvu zoti ukhoza kuona chilango chimene tawaopseza
  96. Dzitetezeni ndi chabwino pothamangitsa choipa. Ife tili kudziwa zonse zimene ali kukunamizirani
  97. Ndipo iwe unene kuti, “Ambuye wanga, Ine ndili kufuna chitetezo chanu pothawa zoipa za Satana.”
  98. “Ambuye! Ine ndili kupempha chitetezo chanu kuti asabwere kumene ndili ine.”
  99. Mpaka pamene imfa idza kwa munthu wolakwa iye adzati, “Ambuye wanga! Bwezeni.”
  100. “Kuti ndikachite ntchitozabwinozimenendidalepherakuchita.” Kosatheka! Amenewa ndiwo mawu chabe amene akungolankhula. Kumbuyo kwawo kudzakhala chipupa mpaka pa tsiku la kuuka kwa akufa
  101. Ndipo pamene lipenga lidzaombedwa, pa tsiku limeneli, ubale wawo wonse udzathera pomwepo ndiponso sadzafunsana chithandizo chochokera kwa wina ndi mnzake
  102. Aliyense amene muyeso wake udzakhala wolemera, adzapambana
  103. Koma aliyense amene muyeso wake udzakhala wopepuka adzataya moyo wake ndipo adzakhala ku Gahena nthawi zonse
  104. Moto udzatentha nkhope zawo ndipo izo zidzakwinyikakwinyika chifukwa chaululu
  105. “Kodi chivumbulutso chathu sichidalakatulidwe kwa inu? Kodi simudachikane?”
  106. Iwo adzati, “Ambuye wathu! Zilakolako zathu zidatigonjetsa ife ndipo tidali anthu osochera.”
  107. “Ambuye wathu! tipulumutseni ife ku ichi. Ngati ife tidzabwereranso ku zoipa, ndithudi, ife tidzakhala anthu oipa kwambiri.”
  108. Iye adzati, “Khalani mu icho mwamanyazi ndipo musandiyankhulitse Ine ayi.”
  109. Ndithudi padali gulu la Atumiki anga amene adati, “Ambuye wathu! Ife timakhulupirira mwa inu. Tikhululukireni ndipo mutichitire chisoni. Inu ndinu wabwino pochita chisoni kuposa a chisoni onse.”
  110. Koma inu munali kuwanyogodola mpaka pamene inu mudandiiwala Ine ndipo inu munali kuwaseka iwo
  111. Ndithudi lero Ine ndawalipira chifukwa cha kupirira kwawo ndipo iwo ndi amene apambana
  112. Ndipo Iye adzafunsa kuti, “Kodi inu munakhala padziko lapansi zaka zingati?”
  113. Iwo adzayankha kuti, “Takhala tsiku limodzi kapena mphindi zochepa zokha. Afunseni iwo amene amasunga chiwerengero.”
  114. Iye adzawayankha kuti, “Inu mukadadziwa ndi nthawi yochepa kwambiri imene inu munakhala.”
  115. “Kodi inu mumaganiza kuti tidangokulengani inu opanda cholinga ndipo kuti simudzabwerera kwa Ife?”
  116. Motero alemekezeke Mulungu, Mfumu ya chilungamo. Palibe Mulungu wina koma Iye yekha, Ambuye wa Mpando wolemekezeka ndi Wachifumu
  117. Aliyense amene apembedza mulungu wina woonjezera pa Mulungu, pamene Iye alibe umboni wa chimenecho, Ambuye wake adzamufunsa. Ndithudi anthu osakhulupirira sadzapambana ayi
  118. Nena, “Ambuye wanga! Ndikhululukireni machimo anga ndipo mundichitire chisoni chifukwa Inu ndinu wachisoni choposa a chisoni onse.”