21.The Prophets

  1. Chayandikira kwa anthu chiweruzo cha ntchito yawo ndi pamene iwo abwerera m’mbuyo monyoza
  2. Palibe chenjezo limene limadza kuchokera kwa Ambuye wawo limene iwo amalimvera kupatula pamene iwo ali kusewera
  3. Ndi mitima yotangwanika, iwo amene amachita zoipa amauzana mwamseri kuti, “Kodi uyu si munthu ngati inu? Kodi inu mukutsatira matsenga pamene muli kuona?”
  4. Iye adati: “Ambuye wanga amadziwa chilichonse chimene chimanenedwa kumwamba ndi pa dziko lapansi ndipo Iye amamva zonse ndiponso amadziwa chinthu china chilichonse.”
  5. Koma ena amati, “Ichi si china koma maloto a bodza! Iyayi! Iye walipeka. Iyayi, iye ndi mlakatuli! Ndipo mulekeni atilangize ife chizindikiro china monga momwe Atumwi akale ankachitira.”
  6. Palibe umodzi wa mizinda imene tidaononga imene idakhulupirira iwo asanadze. Kodi iwo adzakhulupirira
  7. Ndipo Ife, iwe usadabwere sitidatumize ena, koma amuna omwe timawapatsa chivumbulutso. Motero afunse anthu ozindikira ngati iwe siudziwa
  8. Ife sitidawapange iwo ndi matupi amene samadya chakudya kapena amuyaya ayi
  9. Ndipo Ife tidakwaniritsa lonjezo lathu kwa iwo, ndipo tidawapulumutsa iwo pamodzi ndi ena amene Ife tidawafuna koma tidaonongeratu anthu onse ochimwa
  10. Ndithudi tavumbulutsa Buku m’mene muli chikumbutso kwa inu. Kodi mulibe nzeru
  11. Kodi ndi mizinda ingati imene tidaononga imene idali yochita zoipa, ndipo m’malo mwawo tidaikamo anthu ena
  12. Ndipo pamene iwo adaona chilango chathu iwo adayesa kuthawa m’mizinda yawo
  13. “Musathawe koma bwererani kumene mumakhala moyo wa chisangalalo ndi ku nyumba zanu kuti mukafunsidwe.”
  14. Iwo anati, “Tsoka kwa ife! Ndithudi tinali kuchita zoipa.”
  15. Koma kulira kwawo sikunathe mpaka pamene Ife tidawaononga ndi kukhala ngati munda umene wakololedwa
  16. Sitidalengemwamasewerakumwambandidzikolapansi ndi zonse zimene zili pakati pake
  17. Ife tikadafuna kuti tisangalale tikadadzipangira tokha, ngati Ife tikadafunadi kutero
  18. Iyayi! Ife timatumiza choonadi kuti chilimbane ndi bodza ndipo chimaliononga. Taonani, ilo latha. Ndipo tsoka kwa inu chifukwa cha zimene mumanena
  19. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo onse amene ali pafupi pake sanyozera kumupembedza Iye ndipo satopa ayi
  20. Iwo amamutamanda Iye masana ndi usiku ndipo sachita ulesi
  21. Kodi iwo asankha milungu ya pa dziko lapansi imene imadzutsa anthu akufa
  22. Kukadakhala milungu ina kumeneko yoonjezera pa Mulungu weniweni, ndithudi, konse kukadaonongeka. Alemekezeke Mulungu, Mwini wa Mpando wa Chifumu, mu zimene akumunenera
  23. Iye sangafunsidwe pa ntchito zimene amachita pamene iwo adzafunsidwa
  24. Kodi kapena iwo asankha milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni? Nena, “Bweretsani umboni wanu”. Ichi ndi chikumbutso cha amene ndili nawo ndiponso iwo amakedzana. Koma ambiri a iwo sadziwa choonadi motero salabadira
  25. Ndipo Ife sitidatumize iwe usadabadwe, Mtumwi wina aliyense amene sitinamuuze kuti, “Kulibe Mulungu wina koma Ine ndekha, kotero ndi pembedzeni Ine.”
  26. Iwo amati, “Mwini chisoni chosatha wabereka mwana wamwamuna.” Iye alemekezedwe! Amenewo si ena ayi koma akapolo ake olemekezeka
  27. Iwo sayankhula pokhapokha Iye atayankhula, ndipo amachita zinthu potsatira malamulo ake
  28. Iye amadziwa zonse zimene zili patsogolo pawo ndiponso zimene zili m’mbuyo mwawo ndipo iwo sangalankhulire wina aliyense chipulumutso kupatula amene Iye wamukonda ndipo iwo amanjenjemera chifukwa cha mantha pomuona Iye
  29. Ndipo ngati wina wa iwo atanena kuti, “Ndithudi ine ndine mulungu kuonjezera pa Iye.” Oteroyo adzalangidwa ndi moto wa ku Gahena. Mmenemo ndi mmene timalipirira anthu olakwa
  30. Kodi anthu osakhulupirira sadziwa kuti kumwamba ndi dziko lapansi chidali chinthu chimodzi chogwirana chimene tidachisiyanitsa? Ndipo tidapanga, chilichonse chamoyo, kuchokera ku madzi. Kodi iwo sangakhulupirire
  31. Ndipo Ife tidakhazikitsa mapiri pa dziko lapansi molimba kuti asagwedezeke pamodzi ndi iwo ndipo tidakhazikitsa misewu pa miyala kuti mwina atsogozedwe
  32. Ndipo tidapanga kumwamba denga losungika bwino limene silingagwe. Komabe iwo amakana zizindikiro zake
  33. Iye ndiye amene adalenga usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi ndi china chilichonse chimene chimayenda mlengalenga
  34. Palibe munthu, pambuyo pako amene tidamulenga kuti sadzafa. Ngati iweyo udzafa, kodi iwo adzakhala ndi moyo mpaka kalekale
  35. Chilichonse cholengedwa chidzalawa imfa ndipo Ife tidzakuyesani ndi zinthu zoipa ndi zabwino ndipo ndi kwa Ife kumene nonse mudzabwerera
  36. Pamene anthu osakhulupirira amakuona iwe, sakuganizira zabwino koma chipongwe ndipo amati, “Kodi uyu ndiye munthu amene amayankhula zoipa za milungu yanu?” Pamene iwo amakana zonse zokhudza Mwini chisoni chosatha
  37. Munthu adalengedwa kukhala opupuluma pochita zinthu. Ine ndidzakusonyezani zizindikiro zanga. Motero musandifulumizitse
  38. Iwo amati, “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene uli kunena ndi zoona?”
  39. Akadakhala kuti anthu osakhulupirira akudziwa tsiku limene iwo sadzakhala ndi mphamvu zophimba nkhope kapena misana yawo kudziteteza ku moto ndipo iwo sangathandizike
  40. Iyayi. Ilo lidzadza kwa iwo mwadzidzidzi ndipo adzadodoma ndi kusokonezeka ndipo iwo sadzatha kulibweza ndiponso sadzapatsidwa nthawi yopuma
  41. Ndithudi Atumwi ena, adachitidwa chipongwe kale, koma anthu a chipongwe adafafanizidwa ndi chilango chimene iwo adachichitira chipongwe
  42. Nena, “Kodi ndani adzakutetezani inu nthawi ya usiku ndi nthawi ya masana ku mkwiyo wa Mwini chisoni?” Komabe iwo salabadira zokumbukira Ambuye wawo
  43. Kapena iwo ali ndi milungu ina yoti ingawateteze kwa Ife? Iyo siingathe kudziteteza yokha; ndiponso iwo sangatetezedwe kuchilango chathu
  44. Koma Ife tidapereka zokoma za m’moyo uno kwa anthuwa pamodzi ndi makolo awo mpaka pamene nthawi idawatalikira iwo. Kodi iwo saona kuti Ife timachepetsa dziko lawo kuchokera m’malire mwake? Kodi iwo ndiwo adzapambane
  45. Nena, “Ine ndili kukuchenjezani ndi chivumbulutso, koma agonthi sadzamva kuitana pamene achenjezedwa
  46. Koma ngati katsoka kakang’ono kochokera kwa Ambuye wako kagwa pa iwo, ndithudi, iwo adzalira, “Tsoka kwa ife; ndithudi tidali anthu ochita zoipa.”
  47. Ndipo Ife tidzakhazikitsa miyeso yoyenera pa tsiku la kuuka kwa akufa ndipo aliyense sadzaponderezedwa pa china chilichonse. Ngakhale patakhala ntchito zazing’ono zolingana ngati kanthangala kakang’ono tidzazitulutsa kuti ziyesedwe. Ndipo Ife ndife okwana kuwerengera ntchito zonse
  48. Ndithudi Ife tidamupatsa Mose ndi Aroni muyeso ndi muuni wowala ndi chikumbutso kwa anthu angwiro
  49. Iwo amene amaopa Ambuye kuchokera m’maganizo a pansi penipeni pa mtima ndipo amaopa tsiku louka kwa akufa
  50. Ndipo ichi ndi chivumbulutso chodalitsika chimene tatumiza. Kodi mudzachikana
  51. Ndithudi Ife tidamupatsa kale chilangizo Abrahamu ndipo tinali kumudziwa bwino
  52. Pamene Iye adawauza abambo ake ndiponso anthu ake kuti, “Kodi mafano amene muli kuwapembedzawa ndi chiyani?”
  53. Iwo adati, “Ife tidapeza makolo athu ali kuwapembedza.”
  54. Iye adati, “Ndithudi inu ndiponso makolo anu mwakhala muli kuchimwa kwambiri.”
  55. Iwo adati, “Kodi ndi zoona zimene wadza nazo kwa ife kapena ndi nthabwala chabe?”
  56. Iye adati, “Iyayi. Ambuye wanu ndi amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo muzimenezo ine ndichitira umboni.”
  57. “Ndilumbira pali Mulungu kuti ine ndidzachita chiwembu pa mafano anu inu mukangochoka.”
  58. Motero iye adaziphwanya zonse kukhala tizidutswa kupatula fano lalikulu kuti akhoza kudzalifunsa
  59. Iwo adati: “Kodi ndani amene wachita izi kwa milungu yathu? Ndithudi iye ali oipitsitsa.”
  60. Iwo adati, “Ife tinamva mnyamata wotchedwa Abrahamu akunena za milunguyo.”
  61. Iwo adati, “Mubweretseni pamaso pa anthu onse kuti achitire umboni.”
  62. Iwo adati, “Kodi iwe ndi amene wachita izi ku milungu yathu? Oh Abrahamu!”
  63. Iye adati, “Iyayi. Ndi uyu, wamkulu kuposa zonse amene waziphwanya. Afunseni, ngati angayankhule”
  64. Pamenepo iwo adayang’anizana okha nati, “Ndithudi inu ndinu anthu ochimwa kwambiri.”
  65. Ndipo adayang’anizananso nati, “Ndithudi iwe uli kudziwa kuti milungu iyi siiyankhula.”
  66. Abrahamu adati, “Kodi inu mumapembedza mowonjezera pa Mulungu zinthu zimene sizingathe kukuthandizani chilichonse kapena kukuonongani?”
  67. “Tsoka likhale pa inu ndi pa mafano anu amene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu! Kodi mulibe nzeru?”
  68. Onse adati, “Mutentheni kuti muteteze milungu yanu ngati mufuna kuchita china chilichonse.”
  69. Ife tidati, “Iwe moto khala wozizira ndi wamtendere kwa Abrahamu.”
  70. Ndipo iwo adafuna kumuononga Iye koma Ife tidawapanga iwo kukhala olephera
  71. Koma Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi Loti ndipo tidawaika ku dziko limene tidalidalitsa kuti zolengedwa zonse zikhalemo
  72. Ndipo Ife tidamupatsa Isake ndi Yakobo ngati chidzukulu chake ndipo tidawapanga onse kukhala anthu angwiro
  73. Ndipo Ife tidawasankha iwo kukhala atsogoleri olangiza anthu ku ulamuliro wathu ndipo tidawalamulira kuti azigwira ntchito zabwino ndipo, azipitiriza kupemphera ndi kupereka zothandizira osauka. Ndipo iwo anali kutitumikira Ife nthawi zonse
  74. Ndi Loti tidamupatsa luntha, utumiki ndi nzeru za chipembedzo ndipo tidamupulumutsa ku mzinda umene anthu ake anali kuchita zoipa. Ndithudi, iwo anali anthu ochita zoipa ndipo anali osamvera Mulungu
  75. Ndipo Ife tidamulowetsa m’chisomo chathu, ndithudi, iye adali mmodzi wa anthu olungama
  76. Ndi pamene Nowa adatipempha poyamba, Ife tidamva pempho lake ndipo tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake ku chilango choopsa
  77. Ndiponso Ife tidamupulumutsa ku gulu la anthu amene adakana chivumbulutso chathu. Ndithudi iwo anali anthu oipa ndipo onse tidawamiza m’madzi
  78. Pamene Davide ndi Solomoni adaweruza mulandu wa munda umene nkhosa zosochera za anthu ena zidadya nthawiyausiku. Ndipo Ifetidalimbonipachiweruzochawo
  79. Ife tidapatsa Solomoni nzeru zoweruzira nkhaniyi ndipo aliyense wa iwo tidamupatsa luntha, utumwi ndi nzeru. Tinalamula mapiri ndi mbalame kuti zikhale pamodzi ndi Davide pomutamanda Mulungu. Ndife amene tidachita zonsezi
  80. Ndipo tidamuphunzitsa luso lopanga zovala za nkhondo kuti zizikutetezani pa nthawi ya nkhondo, Kodi ndinu othokoza
  81. Ndi Solomoni, Ife tidampeputsira mphamvu ya mphepo. Iyo inali kuomba potsatira malamulo ake kupita kudziko limene Ife tidalidalitsa. Ndipo Ife timadziwa zinthu zonse
  82. Ndipo pakati pa a Satana padali ena omwe amaimira m’malo mwa iye ndipo amachitanso ntchito zina. Kuonjezera apa ndipo ndife amene timawayang’anira iwo
  83. Ndi Yobu pamene adaitana Ambuye wake nati, “Ine, ndithudi, mavuto andikuta ndipo Inu ndinu wachisoni kuposa achisoni onse.”
  84. Motero Ife timamuyankha pempho lake ndipo tidamuchotsera mavuto ake ndipo tidamubwezeranso banja lake ndi zinthu zambiri zimene tidamupatsa ngati chisomo chochokera kwa Ife ndi chikumbutso kwa onse amene amatipembedza Ife
  85. Ndipo Ishimayeli, Idris ndi dhulkifl, onse adali anthu opirira
  86. Ndipo Ife tidawalowetsa m’chisomo chathu. Ndithudi iwo adali anthu olungama
  87. Ndi dhan-Nun pamene adachoka mokwiya kwambiri chifukwa iye adali kuganiza kuti Ife sitingamulenge iye. Koma mu mdima iye adaitana, “Kulibe Mulungu wina koma Inu nokha. Ulemerero ukhale kwa Inu! Ndithudi ine ndidali mmodzi mwa anthu olakwa!”
  88. Motero Ife tidayankha pempho lake ndipo tidamupulumutsa ku mavuto ake. Motero ndimo mmene timapulumutsira anthu okhulupirira
  89. Ndi Zakariya pamene anaitana Ambuye wake nati, “Ambuye wanga! Musandileke ndekha. Ndipo Inu ndinu wabwinomwaokhalitsaonse.”
  90. Motero Ifetidamuyankha pempho lake ndipo tidamupatsa Yohane ndipo tidathetsa uchumba wa mkazi wake. Ndithudi iwo adali ofulumira pochita ntchito zabwino ndipo amatipempha Ife ndi chikhulupiriro ndi mantha ndiponso amadzichepetsa kwa Ife
  91. Adali mkazi amene adasunga unamwali wake. Ife tidauzira mwa iye ndipo tidamupanga iye pamodzi ndi mwana wake wa mwamuna kukhala chizindikiro kwa zolengedwa zonse
  92. Ndithudi! Ichi ndi chipembedzo chanu ndipo ndi chipembedzo chimodzi, ndipo Ine ndine Ambuye wanu motero ndipembedzeni Ine ndekha
  93. Ndipo iwo adapatukana ndi kugawa chipembedzo chawo pakati pawo ndipo ndi kwa Ife kumene adzabwerera
  94. Motero aliyense amene achita ntchito zabwino ndipo ndi wokhulupirira moona ntchito zake sizidzakanidwa ayi. Ndithudi Ife timazilemba zonse m’Buku la chiwerengero
  95. Ndipo ndi koletsedwa kuti mudzi umene tidawuwononga kuti ubwererenso
  96. Mpaka pamene anthu a Ya-juj ndi Majuj adzamasulidwa ndipo iwo adzakhala akutsika kuchokera kumalo aliwonse wokwera
  97. Ndipo pamene lonjezo loona lidzafika, maso a anthu onse osakhulupirira adzapenyetsetsa mwamantha nati “Tsoka kwa ife! Ndithudi ife tidali osalabadira zimenezi. Zoonadi ife tidali ochita zoipa.”
  98. Ndithudi! Inu pamodzi ndi zimene mukupembedza kuonjezera pa Mulungu, mudzakhala nkhuni za ku Gahena! Kumeneko nonse mudzalowako
  99. Iyo ikadakhala milungu, siikadalowa kumeneko ndipo onse adzakhala kumeneko
  100. Kumeneko iwo adzalira ndipo adzakhala osamva
  101. Ndithudi iwo amene tawaonetsera chifundo chathu, iwo adzakhala kutali ndi moto
  102. Iwo sadzamva mkokomo wake pamene iwo ali kumene mitima yawo imafuna mpaka kalekale
  103. Zoopsa sizidzawadandaulitsa ayi ndipo Angelo adzawalandira iwo nati,“Ili ndi tsiku lanu limene inu mudalonjezedwa.”
  104. Tsiku limene tidzapinde thambo monga momwe timapindira tsamba la Buku. Monga momwe tidayamba chilengedwe choyamba momwemonso tidzachibwezeranso. Ili, ndithudi, ndi lonjezo kwa Ife. Ndithudi, Ife, tidzachita motero
  105. Ndipo, ndithudi, Ife tidalemba m’Buku la Masalimo, motsatira chikumbutso kuti akapolo anga angwiro adzakhala ku dziko lapansi
  106. Ndithudi mu ili muli Uthenga womveka kwa anthu amene amapembedza Mulungu
  107. Ndipo sitidakutumize iwe pa chifukwa china koma ngati madalitso kwa zolengedwa zonse
  108. Nena, “Zavumbulutsidwa kwa ine kuti Mulungu wanu ndi mmodzi yekha. Kodi inu mudzadzipereka kwa Iye?”
  109. Koma ngati iwo safuna kumvera nena, “Ine ndili kukuchenjezani kuti tonse tidziwe. Ine sindidziwa kuti chimene mwalonjezedwa chidza msanga kapena chikadali patali.”
  110. Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mumayankhula mokweza ndipo amadziwanso zimene mubisa
  111. Ndipo ine sindidziwa ngati awa ndi mayeso kwa inu ndi chisangalalo cha kanthawi kochepa
  112. Iye anati, “Ambuye wanga! Weruzani mwachilungamo! Ambuye wathu ndi Mwini chisoni chosatha amene chithandizo chake chimafunika pa zimene inu muonjezera.”