20.Taa-Haa

  1. Ta Ha
  2. Ife sitidavumbulutse Korani ino kwa iwe ndi cholinga choti uvutike
  3. Koma kuti chikhale chilangizo kwa anthu oopa Mulungu
  4. Ndi chivumbulutso chochokera kwa Iye amene adalenga dziko lapansi ndi kumwamba kwenikweniko
  5. Mwini chisoni chosatha amene adaoneka ali pamwamba pa Mpando wa Chifumu
  6. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zonse zimene zimakhala m’menemo ndiponso zimene zili pansi pa nthaka
  7. Ngati iwe utchula mawu mokweza, ndithudi Iye amadziwa chinsinsi ndiponso chobisika
  8. Mulungu! Kulibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye yekha. Ake ndi mayina okongola
  9. Kodi udamva za mbiri ya Mose
  10. Pamene iye adaona moto adawauza abale ake kuti, “Dikirani! Ndithudi ine ndaona moto. Mwina ndikubweretserani muuni kuti ndipeze ulangizi pa motopo.”
  11. Pamene iye adafika pafupi ndi moto, adaitanidwa pomutchula dzina lake kuti, “Oh Mose!”
  12. “Ndithudi, Ine ndine Ambuye wako! Motero chotsa nsapato zako. Ndithudi iwe uli m’dambo lodalitsika la Tuwa.”
  13. “Ndipo Ine ndakusankha iwe. Kotero mvetsera chimene chikuvumbulutsidwa kwa iwe.”
  14. Ndithudi Ine ndine Mulungu. Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha motero ndipembedze Ine ndipo pitiriza mapemphero pondikumbukira Ine.”
  15. “Ndithudi ola lili nkudza ndipo cholinga changa ndi kulibisa kuti mzimu ulionse udzalipidwe malipiro molingana ndi ntchito zake.”
  16. “Ndipo usalole kuti munthu amene sakhulupirira za olali ndipo yemwe amachita zimene mtima wake umafuna kuti akusocheretse chifukwa ukhoza kuonongeka.”
  17. “Kodi ndi chiyani chimene chili m’dzanja lako la manja iwe Mose?”
  18. Iye adati, “Iyi ndi ndodo yanga, ndi iyoyi ine ndimayedzamira ndipo ndimagwetsera masamba akudya nyama zanga. Imeneyi imandithandiza pa ntchito zambiri kuonjezera pa zimenezi.”
  19. Mulungu adati, “Ndodoyo iponye pansi iwe Mose.”
  20. Mose adaiponya pansi, ndipo taonani! Iyo idasanduka njoka yoyenda mwaliwiro
  21. Mulungu adati, “Igwire ndipo usachite mantha ayi. Ife tidzaibwezera monga momwe idalili poyamba.”
  22. “Tsopano kanikiza dzanja lako m’khwapa mwako. Ilo lidzasanduka loyera lopanda matenda ngati chizindikiro china.”
  23. “Kuti tikusonyeze zizindikiro zathu zazikulu.”
  24. “Pita kwa Farawo! Ndithudi iye wadumpha malire onse.”
  25. Mose adati, “Ambuye tsekulani chifuwa changa”
  26. “Ndipo pepukitsani ntchito yanga.”
  27. “Masulani lilime langa ku chibwibwi.”
  28. “Kuti anthu azindikire zonena zanga.”
  29. “Ndipo ndisankhileni munthu wondithandiza kuchokera ku banja langa.”
  30. “Aroni m’bale wanga.”
  31. “Onjezereni mphamvu zanga ndi iye.”
  32. “Ndipo muloleni nayenso kugwira ntchito yanga.”
  33. “Kuti tizikulemekezani kwambiri.”
  34. “Ndi kukukumbukirani kwambiri.”
  35. “Ndithudi! Inu muli kutiona nthawi zonse.”
  36. Mulungu adati, “Pempho lako lalandiridwa, iwe Mose.”
  37. “Ndithudi Ife tidakuonetsa chifundo chathu nthawi ina.”
  38. “Pamene tidawauza Amayi ako mawu athu.”
  39. Ponena kuti, “Ika mwana wako m’bokosi ndipo umuponye mu mtsinje ndipo mtsinje udzamulavula iye pa mtunda ndipo adzatoledwa ndi mdani wanga ndiponso ndi mdani wake. Ndipo Ine ndidaonetsa chikondi changa pa iwe kuti uleredwa moyang’aniridwa ndi Ine.”
  40. “Ndipo pamene mlongo wako adapita kwa iwo ndi kunena kuti, Kodi ndikusonyezeni Mayi amene akhoza kumusamala iye? M’menemo ndi mmene tidakubwezera kwa Amayi ako kuti mtima wawo ukhoza kukhazikika ndipo kuti asakhumudwe. Ndipo pamene iwe udapha munthu, Ife tidakupulumutsa ku mavuto ako, ndipo tidakuyesa ndi mayeso ena. Iwe udakhala pakati pa anthu a ku Midiyani zaka zambiri ndipo pomaliza, iwe Mose, udabwera kuno monga momwe zidakonzedwera.”
  41. “Ine ndakusankha iwe kuti unditumikire Ine.”
  42. “Pita iwe ndi m’bale wako ndi zizindikiro zanga ndipo musatope pondikumbukira Ine.”
  43. “Pitani, nonsenu, kwa Farawo yemwe wadumpha malire.”
  44. “Ndipo mukayankhule naye ndi mawu oleza kuti mwina akhoza kumva chenjezo kapena kuopa Mulungu.”
  45. Iwo adati, “Ambuye wathu! Ndithudi! Ife tiopa kuti abweretsa chilango chake msanga kapena achita zoipa zambiri kwa ife.”
  46. Iye adati, “Musaope! Ndithudi! Ine ndili pamodzi ndi inu. Ine ndimamva zonse ndipo ndimaona.”
  47. “Motero pitani nonse kwa iye ndipo mukati, ‘Ndithudi ife ndife Atumwi Ambuye wako motero aleke ana a Israyeli kuti apite ndi ife ndipo usawazunzenso ayi. Ndithudi ife takubweretsera zizindikiro zochokera kwa Ambuye wako! Ndipo mtendere udzakhala kwa iye amene atsatira langizo.”
  48. “Ndithudi zavumbulutsidwa kwa ife kuti chilango chake chidzagwa pa iye amene amakana zizindikiro zake ndipo sazimvera ayi.”
  49. Farawo adati, “Kodi Mose, Ambuye wanu ndani?”
  50. Iye adati, “Ambuye wathu ndiye amene adapereka maonekedwe osiyanasiyana ku zolengedwa zake ndipo adazilangiza bwinobwino.”
  51. Farawo adati, “Nanga zinali bwanji ndi anthu a masiku akale?”
  52. Iye adati, “Ambuye wanga yekha ndiye amene adziwa zimenezo ndipo zidalembedwa mu Buku lake. Iye salakwa ndiponso saiwala.”
  53. Amene adakupangirani dziko lapansi kukhala ngati kama ndipo adakhazikitsa njira zoti inu muziyendamo ndipo watumiza mvula kuchokera kumwamba. Ndipo ameretsa ndi iyo mitundu yosiyanasiyana ya mbewu
  54. Idyani ndiponso dyetsani ziweto zanu. Ndithudi muzimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira
  55. Kuchokera ku dothi tidakulengani inu ndipo ndi ku nthaka kumene tidzakubwezerani ndipo kuchoka ku iyo tidzakuutsani kuti mukhalenso ndi moyo kachiwiri
  56. Ndithudi tidamulangiza Farawo zizindikiro ndi umboni wathu koma iye adazikana zonse ndipo sadamvere ayi
  57. Iye adati, “Kodi iwe Mose wadza kudzatichotsa m’dziko lathu ndi matsenga ako?”
  58. “Ndithudi ife tikhoza kukubweretsera matsenga olingana ndi ako. Motero sankha tsiku limene ife kapena iwe siudzalephera kusunga loti tidzakumane iwe ndi ife, pa bwalo pamene tonse tidzakhala ndi mwai wofanana.”
  59. Mose adati, “Tsiku lokumana lidzakhale tsiku la chisangalalo ndipo anthu adzasonkhanitsidwe nthawi ya ku m’mawa dzuwa litakwera pang’ono.”
  60. Farawo adachokapo ndipo adasonkhanitsa a matsenga ake ndipo adadza nawo kwa Mose
  61. Mose adati kwa iwo, “Tsoka kwa inu! Musapeke mabodza okhudza Mulungu chifukwa akhoza kukuonongani ndi chilango. Ndipo, ndithudi, aliyense amene apeka bodza adzalephera mochititsa manyazi
  62. Anthu a matsenga adakambirana wina ndi mnzake pa zimene angachite ndipo adasunga zokambirana zawo
  63. Iwo adati, “Anthu awiriwa ndi anthu a matsenga amene afuna kuti akuchotseni m’dziko lanu pogwiritsa ntchito matsenga awo ndikugonjetsa mafumu ndi anthu anu aulemu wawo.”
  64. “Motero konzekani ndipo muime mu mzere. Iwo amene apambane lero, ndithudi, adzakhala opambanadi.”
  65. Iwo adati, “Iwe Mose! Kodi udzayamba ndiwe kuponya ndodo yako kapena tiyambe ndife kuponya ndodo zathu?”
  66. Iye adati, “Iyayi. Ponyani zanu poyamba.” Ndipo taona ndi mphamvu ya matsenga awo, zingwe ndi ndodo zawo zidaoneka, m’maso mwa Mose, kuti zinali kuyenda mofulumira
  67. Motero Mose adachita mantha mu mtima mwake
  68. Koma Ife tidamuuza kuti, “Usaope! Ndithudi iwe udzapambana.”
  69. “Ndipo ponya chimene chili m’dzanja lako la manja. Icho chidzameza zinthu zimene iwo akonza chimene ndi chinyengo cha matsenga ndipo munthu wa matsenga sadzapambana ngakhale atakhala odziwa chotani.”
  70. Anthu a matsenga adagwa pansi kulambira nati, “Ife takhulupirira mwa Ambuye wa Aroni ndi Mose.”
  71. Farawo adati, “Kodi inu mukumukhulupirira iye wopanda chilolezo changa? Ndithudi munthu uyu ayenera kukhala mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi miyendo yanu mosiyanitsa ndipo, ndithudi, ine ndidzakupachikani pa thunthu la mtengo wa mgwalangwa. Ndipo, ndithudi, inu mudzadziwa kuti ndani mwa ife amene akhoza kupereka chilango chowawa kwambiri ndiponso chosatha.”
  72. Iwo adati, “Ife sitifuna iwe kuposa zizindikiro zimene zadza kwa ife ndi Iye amene adatilenga ife. Kotero iwe chita chimene ufuna kuchita chifukwa iwe ukhoza kulamulira za m’moyo uno zokha.”
  73. “Ndithudi ife taika chikhulupiriro chathumwaAmbuyewathukutiatikhululukireifemachimo athu ndiponso pa matsenga amene udatikakamiza kuti tichite ndipo malipiro a Mulungu ndi abwino ndiponso osatha pofanizira ndi malipiro ako.”
  74. Ndithudi! Aliyense amene adza pamaso pa Ambuye wake ali wamachimo, ndithudi, iye adzaponyedwa ku Gahena kumene sadzakhala ndi moyo kapena imfa
  75. Koma iye amene adza kwa Iye ndi chikhulupiriro choonadi ndiponso ntchito zabwino, adzakhala ndi ulemerero wapamwamba zedi
  76. Minda yamuyaya yomwe pansi pake pamayenda mitsinje m’menemo iwo adzakhalamo nthawi zonse. Amenewa ndiwo malipiro a iwo amene amadziyeretsa
  77. Ndithudi Ife tidamuuza Mose kuti, “Nyamuka nthawi yausiku pamodzi ndi akapolo anga ndipo uwatsekulire njira pakati pa nyanja ndipo usaope kuti akupeza, kapena kumira m’nyanja.”
  78. Ndipo Farawo adawatsatira ndi asirikali ake koma madzi adawamiza onse
  79. Farawo adasocheretsa anthu ake ndipo sadawatsogolere ayi
  80. oh Inu ana a Israyeli! Ife tidakupulumutsani inu kwa adani anu ndipo tidachita lonjezo ndi inu pambali yakumanja kwa Phiri ndipo tidakutsitsirani manna ndi mbalame zokoma
  81. Idyani zinthu zabwino zimene tidakupatsani ndipo musaswe malamulo chifukwa mkwiyo wanga ungagwe pa inu. Ndipo yense amene umpeza mkwiyo wanga ndithudi watha
  82. Ndipo, ndithudi, Ine ndimakhululukira aliyense amene alapa, akhulupirira ndipo achita ntchito zabwino ndiponso apitiriza kuzichita
  83. “Kodi Mose chakufulumizitsa kubwera kuno ndi kusiya anthu ako ndi chiyani?”
  84. Mose adati, “Iwo ali kumbuyo kwangaku akunditsatira. Ndadza mofulumira kwa Inu, Ambuye, kuti musangalale.”
  85. Mulungu adati, “Ndithudi! Ife tawayesa mayeso anthu ako popembedza ng’ombe pamene iwe unachoka ndipo Msamiri wawasocheretsa.”
  86. Mose adabwerera kwa anthu ake ndi mkwiyo ndiponso mwachisoni. Iye adati, “Anthu anga! Kodi Ambuye wanu sadakulonjezeni lonjezo labwino? Kodi munaona nthawi ya lonjezo kutalika? Kapena chinali cholinga chanu kuti mkwiyo wa Ambuye wanu udze pa inu ndipo inu muphwanye lonjezo lanu kwa ine?”
  87. Iwo adati, “Ife sitinaphwanye lonjezo lako pa chifukwa chathu ayi. Koma ife anatinyamulitsa katundu wa anthu, ndolo, ndipo tinaziponya pa moto. Zimenezo ndizo zimene Msamiri anatiuza.”
  88. Ndipo iye adawatulutsira iwo chifanizo cha thupi la ng’ombe chimene chidali ndi mawu. Iwo adati, “Uyu ndi mulungu wanu ndi mulungu wa Mose yemwe adamuiwala.”
  89. Kodi iwo sanaone kuti sichidawayankhe china chilichonse ndipo kuti chinalibe mphamvu yowapweteka kapena kuwathandiza iwo
  90. Ndithudi Aroni adawauza iwo poyamba kuti, “Oh Anthu anga! Inu muli kungoyesedwa nacho ichi koma, ndithudi, Ambuye wanu ndiye Mwini chisoni chosatha motero tsatireni ine ndipo mverani malamulo anga.”
  91. Iwo adati, “Ife sitidzasiya kuchipembedza ichi mpaka pamene Mose adza kwa ife.”
  92. Mose adati, “oh Aroni! Kodi chidakuletsa ndi chiyani kuwatsutsa iwo pamene udaona kuti ali kusochera?”
  93. “Kuti siunanditsatire ine. Kodi waswa lamulo langa?”
  94. Aroni adati, “Mwana wa Amayi anga! Usandikoke ndevu zanga kapena tsitsi langa! Ndithudi! Ine ndidali ndi mantha kuti mwina iwe ukhoza kudzanena kuti, iwe wabzala mpatuko pakati pa ana a Israyeli ndipo siunalemekeze mau anga.”
  95. Mose adati, “Iwe Msamiri, kodi chifukwa chiyani udachita izi?”
  96. Iye adati, “Ine ndidaona zimene iwo sanali kuona. Motero ine ndidatenga dothi lodzala m’manja kuchokera ku fumbi lochokera ku phazi la Mtumwi ndi kulitaya. Kotero mzimu wanga udandikakamiza.”
  97. Mose adati, “Choka! Ndithudi chilango chako m’moyo uno ndi chakuti udzanena kuti, ‘Musandikhudze.’ Ndithudi iwe uli ndi lonjezo limene siliphwanyidwa ayi. Taona mulungu wako amene wamutumikira ndi mtima wako wonse. Ife tidzaliotcha m’moto ndipo tidzamwaza phulusa lake pa nyanja.”
  98. Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi yekha. Iye amadziwa chilichonse
  99. Kotero Ife tili kukufotokozerani mbiri ya zinthu zimene zidachitika kale. Ndithudi takupatsa chikumbutso
  100. Iwo amene adzachikana ndithudi adzanyamula katundu wolemera wamachimo pa tsiku la kuuka kwa akufa
  101. Iwo adzakhala m’menemo mpaka kalekale ndipo zidzakhala zoipa kwambiri kwa iwo osenza katundu wotereyu tsiku la kuuka kwa kufa
  102. Tsiku limene lipenga lidzaimbidwa, patsiku limene Ife tidzasonkhanitsa anthu onse ochimwa, maso awo adzakhala obiriwira ndi nkhope zakuda
  103. Monong’onezana adzakhala ali nkuyankhulana nati, “Inu simunakhale padziko lapansi kupatula masiku khumi okha.”
  104. Ife tili kudziwa kwambiri zimene adzayankhula, pamene anthu awo angwiro ndi anzeru adzati, “Inu simunakhale padziko kupatula tsiku limodzi lokha.”
  105. “Ndipo iwo ali kukufunsa za mapiri. Nena, “Ambuye wanga adzawachotsa iwo ndi kuwamwaza ngati fumbi la dothi.”
  106. “Ndipo iye adzawasiya kukhala ngati bwalo lasesese.”
  107. “M’menemo sudzaona malo otsika kapena okwera.”
  108. Pa tsiku limeneli, anthu adzatsatira woitana wa Mulungu, mopanda chinyengo. Ndipo mawu onse adzachepetsedwa chifukwa cha Mwini chisoni ndipo iwe siudzamva china kupatula mgugu wochepa wa mapazi awo
  109. Patsiku limeneli, palibe wina amene adzakhala ndi mphamvu yoyankhula m’malo mwawo kupatula yekhayo amene adzalandire chilolezo cha Mwini chisoni ndiponso amene mawu ake ngolandiridwa kwa Iye
  110. Amadziwa zonse zimene zili kutsogolo kwawo ndiponso zimene zili kumbuyo kwawo ndi zimene zili nkudza pamene iwo sadziwa china chilichonse cha Iye
  111. Ndipo nkhope zonse zidzachepetsedwa pamaso pa Mwini moyo wa nthawi zonse amene amateteza china chilichonse. Ndipo yense amene analakwa, ndithudi, ndi olephera
  112. Ndipo iye amene achita ntchito zabwino ndipo ndi munthu wokhulupirira, iye sadzaopa kuponderezedwa kapena kumanidwa malipiro
  113. Motero Ife tidatumiza Korani mu Chiarabu ndipo tafotokoza m’menemo mowirikiza machenjezo kuti iwo akhale oopa Mulungu kapena kuti Koraniyo iwapatse chiphunzitso kuchokera mu ilo
  114. Wolemekezeka ndi Mulungu, Mfumu ya choonadi! Ndipo usafulumire kulakatula Korani, chivumbulutso chake chisanathe koma uyenera kunena kuti, “Ambuye ndionjezereni nzeru.”
  115. Ndithudi IfetidachitalonjezondiAdamukalekomaiye adaiwala ndipo sitinapeze chipiriro kwa iye
  116. Pamenepo Ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Ndipo onse adamugwadira koma Satana adakana
  117. Ife tidati, “oh iwe Adamu! Ndithudi uyu ndi mdani wako ndiponso mdani wa mkazi wako. Musalole kuti akutulutseni ku Paradiso ndi kukukhazikani m’mavuto.”
  118. Ndithudi muli ndi lonjezo lathu kuti kumeneko inu simudzamva njala kapena kukhala wamaliseche
  119. Ndiponso inu simudzamva ludzu m’menemo kapena kutentha kwa dzuwa
  120. Koma Satana adamunong’oneza nati, “Oh iwe Adamu! Kodi ndingakulangize mtengo wa moyo wosatha ndiponso ufumu wosatha?”
  121. Ndipo onse adadya chipatso cha mumtengo uja kotero udaonekera umaliseche wawo ndipo adayamba kudziveka masamba a m’munda muja. Kotero Adamu adanyoza lamulo la Ambuye wake ndipo adasochera
  122. Ndipo Ambuye wake adamusankha iye ndipo adamukhululukira ndi kumutsogolera kunjira yoyenera
  123. Mulungu adati, “Chokani inu m’menemo, nonse awiri, ndipo inu mudzakhala adani a wina ndi mnzake. Pamene ulangizi wanga udzavumbulutsidwa kwa inu, iye amene adzautsatira sadzasochera kapena kuona mavuto.”
  124. “Koma iye amene safuna kumvera machenjezo anga, ndithudi, adzakhala movutika ndipo tidzamuukitsa ali wakhungu pa tsiku louka kwa akufa.”
  125. Iye adzati, “Ambuye wanga! Bwanji mwandiukitsa wakhungu, pamene ine ndidali wopenya?”
  126. Mulungu adzati, “Chifukwa chakuti pamene chivumbulutso chathu chinadza kwa iwe udachiiwala. Chimodzimodzi tsiku lino nawenso waiwalidwa.”
  127. Mmenemundimmenetimalipiriramunthu oswa malamulo amene sakhulupirira chivumbulutso cha Ambuye wake. Koma chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi choopsa ndiponso chosatha
  128. Kodi iwo saona mibadwo ya anthu imene tidaiononga iwo asanadze? Iwo amayenda pakati pa nyumba zimene iwo anali kukhalamo. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu a nzeru
  129. Akadakhala kuti Ambuye wako sadalonjeze ndi kukhazikitsa nthawi, chilango chawo chikanadza kale
  130. Motero pirira pa zimene ali kunena ndipo lemekeza ndi kutamanda Ambuye wako dzuwa lisanatuluke ndiponso lisanalowe. Ndipo muyamike Iye nthawi yausiku ndi yausana kuti iwe udzasangalale
  131. Usasirire zinthu zimene tawapatsa anthu chifukwa zimenezi ndi zosangalatsa za m’moyo uno. Ife tingofuna kuwayesa nazo. Koma mphotho ya Ambuye wako ndi yabwino ndipo ndi yosatha
  132. Ndipo lamulira banja lako kupemphera ndipo ukhale wopirira pokwaniritsa mapemphero. Ife sitipempha zinthu kwa iwe koma Ife timakupatsa zofuna zako. Ndipo mapeto abwino ndi a anthu oopa Mulungu
  133. Iwo adati, “Bwanji iye satipatsa ife chizindikiro chochokera kwa Ambuye wake?” Kodi iwo sadapatsidwe zizindikiro zambiri zimene zili m’mabuku a kale a Mulungu
  134. Ngati Ife tikadawaononga iwo ndi chilango tisadawatumizire ichi, iwo akadati, “Ambuye wathu! Inu mukadatitumizira Mtumwi, ndithudi, ife tikadatsatira chivumbulutso chanu tisadanyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi.”
  135. Nena, “onse ali kudikira. Nanunso dikirani ndipo inu mudzadziwa kuti ndani amene adatsatira njira yoyenera ndiponso amene ali otsogozedwa.”