19.Mary

  1. Kaf ha ya ain suad
  2. Ichi ndi chikumbutso cha chifuniro cha Ambuye wako kwa kapolo wake Zakariya
  3. Pamene Iye adamupempha Ambuye wake motsitsa mawu
  4. Iye adati, “oh Ambuye wanga! Mafupa anga ndi ofoka ndipo mutu wanga uli ndi imvi chifukwa cha ukalamba. Komabe, Ambuye, ine sindidapemphe kwa Inu mopanda phindu.”
  5. “Ndithudi ine ndili ndi mantha ndi abale anga za amene adzalowe m’malo mwanga ndiponso mkazi wanga ndi chumba. Ndipatseni mwana wamwamuna.”
  6. “Amene adzalowe m’malo mwanga ndi m’malo mwa ana a Yakobo, ndipo mpangeni, Ambuye wanga, kukhala mmodzi wa wokondedwa wanu.”
  7. “Ee iwe Zakariya! Ife tili kukuuza nkhani yabwino yakuti iwe udzapatsidwa mwana wamwamuna ndipo adzatchedwa Yohane, dzina limene silidapatsidwe kwa aliyense kumbuyoku.”
  8. Zakariya adati, “Ambuye! Kodi ine ndingakhale ndi mwana wamwamuna bwanji, pamene mkazi wanga ndi chumba ndipo ine ndine wokalamba?”
  9. Iye adati, “Chimenechi, wanena Ambuye wako! Idzakhala ntchito yopepuka kwa Ine chifukwa Ine ndidakupanga kukhala munthu pamene iwe siunali chinthu china chilichonse chodziwika.”
  10. Zakariya adati, “Ambuye, ndipatseni chizindikiro chokhudza zimene zidzachitike.” Iye adati, “Chizindikiro chako ndi chakuti siudzalankhula ndi anthu usiku utatu ngakhale ulibe chilema.”
  11. Pamene Zakariya adadza kwa anthu ake kuchokera m’kachisi, adawauza anthuwo kuti, “Lemekezani Ambuye wanu m’mawa ndi madzulo.”
  12. “Oh Yohane! Samala mawu a Mulungu kwambiri.” Ife tidamupatsa luntha pamene adali mwana
  13. Ndiponso tidamupatsa mtima wachifundo ndi woyeretsedwa ndipo adali munthu opewa zoipa
  14. Ndipo adali kulemekeza abambo ndi amayi ake. Iye sadali wodzikweza kapena wonyoza malamulo a Mulungu
  15. Mtendere udali pa iye pa tsiku limene adabadwa ndi pa tsiku limene adafa ndipo mtendere ukhale pa iye pamene aukitsidwa kwa akufa
  16. Ndipo kukumbukira nkhani ya Maria m’Buku! Pamene iye adasiya anthu ake ndi kupita kumalo a payekha kumbali ya ku m’mawa
  17. Ndipo iye adafunda nsalu kuti anthu asaone nkhope yake. Ife tidamutumizira iye Mzimu wathu umene udaoneka ngati munthu
  18. Maria adati, “Mwini chisoni anditeteze ine kwa iwe! Ngati iwe umaopa Ambuye, ndisiye ndekha, usandiyandikire ayi.”
  19. Mngelo adati, “Ine ndine Mthenga wa Ambuye wako ndipo ndadza kudzakupatsa mwana wamwamuna woyera.”
  20. Maria adati, “Kodi ine ndidzabereka mwana bwanji pamene ine ndine wosakhudzidwa ndi mwamuna ndiponso si ndine wachiwerewere ayi?”
  21. Mngelo adati, “Ndi momwemo” Ambuye wako wanena kuti, “Zimenezo, kwa Ine, ndi zopepuka. Tidzamupanga iye kukhala chizindikiro kwa anthu ndi madalitso ochoka kwa Ife. Limeneli ndilo lamulo limene lalamulidwa.”
  22. Ndipo iye adakhala ndi pakati ndipo adapita kumalo akutali
  23. Ndipo ululu wa kubereka udamubwerera pamene adali patsinde pa mtengo wa tende ndipo adalira nati, “Kalanga ine, bola ndikadangofa zisanachitike izi chifukwa ndikadakhala woiwalidwa.”
  24. Kudabwera mawu kuchokera pansi oti: “Usadandaule ayi. Ambuye wako wakukonzera ka mtsinje kamene kalikuyenda ku mapazi ako.”
  25. “Ndipo gwedeza mtengo watendewu, iwo udzagwetsa zipatso za tende zaziwisi ndi zakupsa.”
  26. “Idya ndi umwe, kotero sangalala.” Ndipo ukakumana ndi munthu wina aliyense muuze kuti, “Ine ndalumbira kwa Mwini chisoni kusala chakudya ndipo sindidzayankhula ndi munthu wina aliyense lero.”
  27. Ndipo iye adatenga mwana wake nanka naye kwa anthu ake amene adati kwa iye’ “Iwe Maria! Ndithudi iwe wabweretsa chinthu cha chilendo.”
  28. “Iwe mlongo wake wa Aroni! Atate wako sanali munthu wochita zoipa ndiponso Amayi ako sadali a chiwerewere.”
  29. Maria adamuloza iye. Koma iwo adati, “Kodi ife tingayankhule ndi mwana wam’chikuta bwanji?”
  30. Mwanayo adati, “Ine ndine kapolo wa Mulungu. Iye wandipatsa ine Buku labwino ndipo wandisankha kukhala Mtumwi.”
  31. “Madalitso ake ali pa ine kulikonse kumene ndingapite ndipo wandilamulira kuti ndikhale wopemphera ndi kupereka chaulere kwa anthu osauka nthawi yonse ya moyo wanga.”
  32. “Iye wandilamula kuti ndizilemekeza amayi anga ndipo sadandipange kukhala wamwano ndi woipa.”
  33. Ndipo mtendere ukhale kwa ine patsiku limene ndidabadwa, ndi patsiku limene ndidzafa ndiponso pa tsiku limene ndidzaukitsidwa kwa akufa
  34. Ameneyo ndiye Yesu, mwana wa Maria. Liwu loonadi limene iwo ali kukayika
  35. Sizili zoyenera kuti Mulungu akhale ndi mwana wamwamuna! Iye ayeretsedwe ku zimenezo. Ngati Iye afuna chinthu, Iye amangonena kuti, “Chikhale” ndipo chimakhaladi
  36. Ndithudi Mulungu ndi Ambuye wanga ndiponso Ambuye wanu. Kotero mpembedzeni Iye yekha. Imeneyo ndiyo njira
  37. Koma magulu a Akhirisitu adasemphana maganizo pakati pawo. Koma pamene tsiku loopsa lidza, tsoka kwa anthu osakhulupirira
  38. Kodi iwo adzaona ndi kumva momveka bwanji pa tsiku limene adzaonekera pa maso pathu! Koma anthu ochita zoipa lero ali mu chisokonezo choonekeratu
  39. Achenjeze za tsiku limene adzanong’oneza bombono, pamene malamulo athu adzakwaniritsidwa ndipo pamene iwo ali nkuiwala ndi kusakhulupirira
  40. Ndithudi Ife tidzatenga dziko lapansi ndi onse amene amakhala m’menemo. Ndi kwa Ife kumene onse adzabwezedwa
  41. Ndipo kumbukira nkhani ya Abrahamu imene ili m’Buku. Iye adali Mtumwi ndi munthu wangwiro
  42. Pamene iye adawauza bambo wake kuti, “Oh Abambo! Kodi inu mungalambire bwanji chinthu chimene sichingathe kumva, kuona kapena kukuthandizani pa chilichonse?”
  43. “Ohabambo! Choonadichavumbulutsidwa kwa ine chimene sichinakufikireni inu. Kotero nditsatireni ine kuti ndikutsogolereni ku njira yoyenera.”
  44. “oh abambo! Musamapembedze Satana. Ndithudi Satana adanyoza Ambuye wachisoni chosatha.”
  45. “oh abambo! Ine ndili kuopa kuti chilango cha Mulungu chidzadza pa inu ndipo mudzakhala bwenzi la Satana.”
  46. Abambo ake adati, “Kodi ukudana ndi milungu yanga iwe Abrahamu? Ukapanda kusiya ndidzakuponya miyala ndipo unditalikire pa kanthawi kochepa.”
  47. Abrahamu adati, “Mtendere ukhale kwa inu. Ine ndidzapempha Ambuye wanga kuti akukhululukireni popeza, Mulungu, kwa ine, ndi wokoma mtima.”
  48. “Ine ndikuchokerani ndi zimene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu. Ine ndidzapempha kwa Ambuye wanga ndipo ndikhulupirira kuti popembedza Ambuye wanga ndisadzakhale watsoka
  49. Ndipo pamene Abrahamu adasiya anthu ake ndi mafano amene iwo anali kupembedza kuonjezera pa Mulungu, tidamupatsa Isake ndi Yakobo. Aliyense wa iwo tidamupanga kukhala Mtumwi
  50. Ndipo tidawapatsa onse mituka kuchokera m’chifundo chathu ndipo tidawapanga iwo kukhala otchulidwa mwaulemu
  51. Ndipo kumbukira nkhani ya Mose imene ili m’Buku, amene adali wosankhidwa ndiponso Mtumwi ndi Mneneri
  52. Ife tidamuitana kuchokera kumbali ya dzanja la manja la phiri la Sinai ndipo tinamuyandikitsa kukhala pafupi ndi Ife kuti tiyankhule naye mwamseri
  53. Tidamupatsa, mwachisoni chathu, m’bale wake Aroni kuti akhale Mtumwi
  54. Ndipo kumbukira nkhani ya Ishimayeli imene ili m’Buku. Iye adali wosunga pangano ndipo adali Mtumwi ndi Mneneri
  55. Iye anali kulamula anthu ake kuchita mapemphero ndi kupereka chothandiza nacho anthu osauka ndipo adali, kwa Ambuye wake, wokondedwa
  56. Ndipo kumbukira za Idrissa. Iye adali munthu wonena zoona ndi Mtumwi
  57. Ife tidamukweza kukhala malo a pamwamba
  58. Awa ndi anthu amene Mulungu adawaonetsera chisomo chake. Atumwi ochokera ku m’badwo wa Adamu ndi iwo amene tidawatenga pamodzi m’chombo ndi Nowa. Ana a Abrahamu, a Israyeli ndi iwo amene Ife tawatsogolera ndi kuwasankha. Pamene zivumbulutso za Mwini chisoni chosatha zinali kulakatulidwa kwa iwo, iwo adali kugwa nkhope zawo pansi ndi kumalira
  59. Koma mibadwo ya anthu imene inadza iwo atachoka idanyoza mapemphero ndi kutsatira zilakolako zawo. Ndithudi awa adzakumana ndi mavuto
  60. Kupatula amene alapa machimo ndi kukhulupirira choonadi ndi kumachita ntchito zabwino. Iwo adzalowa ku Paradiso ndipo sadzaponderezedwa m’chilichonse
  61. Iwo adzakhala m’minda ya Edeni mpaka muyaya, imene Mwini chisoni chosatha adalonjeza akapolo ake ngakhale kuti iwo sadaione. Ndithudi lonjezo lake lidzakwaniritsidwa
  62. Kumeneko iwo sadzamva zinthu zopanda pake koma mawu a mtendere okha, ndipo chakudya chidzapatsidwa kwa iwo m’mawa ndi madzulo
  63. Imeneyo ndiyo Paradiso imene tidzawapatsa akapolo athu omwe anali kuopa Mulungu
  64. Ife sititsika kuchoka kumwamba pokhapokha ngati taloledwa ndi Ambuye wako. Iye ndiye mwini wa zinthu zonse zimene zili pamaso pathu, kumbuyo kwathu ndi zonse zimene zili pakati pa zimenezi. Ndipo Ambuye wako saiwala
  65. Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo. Kotero m’pembedze Iye yekha ndipo khala wopirira pamapemphero ake. Kodi ukudziwa wina amene ali ndi dzina ngati la Iye
  66. Munthu amati, “Pamene ine nditafa kodi ndidzaukitsidwa ndi kukhalanso ndi moyo?”
  67. Kodi munthu sakumbukira kuti tidamulenga iye pamene poyamba sadali chinthu china chilichonse
  68. Motero pali Ambuye wako; ndithudi Tidzawasonkhanitsa pamodzi ndi a Satana ndipo onse tidzawabweretsa m’mphepete mwa Gahena atagwada
  69. Ndipo mwachoonadi tidzachotsa mugulu lililonse onse amene adanyoza Mulungu kwambiri
  70. Ndithudi Ife tilikuwadziwa kwambiri amene ali oyenera kuotchedwa
  71. Palibe wina wa inu amene sadzapita kumbali ya Moto. Limeneli ndilo lamulo la mphamvu la Ambuye wanu
  72. Ndipo Ife tidzapulumutsa onse amene amaopa ndi kuwasiya ochita zoipa, atagwada, kuti amve ululu wake
  73. Pamene zivumbulutso zathu zilakatulidwa momveka kwa iwo, anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ndi gulu liti pa magulu awiriwa limene lili ndi malo abwino okhala ndi anthu apamwamba?”
  74. Kodi ndi mibadwo ingati yakale imene tidaononga iwo asanadze, mibadwo imene idali ndi zinthu zabwino ndiponso zokongola
  75. Nena, “Aliyense amene alakwa, Mwini chisoni chosatha adzawaonjezera nthawi, mpaka pamene adzaone zomwe adalonjezedwa. Kaya ndi chilango kapena ola lomaliza, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndani amene ali mwini wa malo oipa ndi gulu lankhondo lofoka.”
  76. Mulungu amapitiriza kutsogolera iwo amene atsatira njira yoyenera. Ntchito zabwino zimene zili ndi malipiro osatha zili ndi mphotho yabwino pamaso pa Ambuye wako ndiponso zotsatira zake ndi zabwino
  77. Kodi mwamuona munthu amene akana zivumbulutso zathu ndipo amanena kuti, “Ine, ndithudi, ndidzapatsidwa chuma ndi ana?”
  78. Kodi iye waziona zinthu zosaoneka kapena Mwini chisoni chosatha wamupatsa lonjezo lotere
  79. Osatheka! Ife tidzalemba zimene akunena ndi kuchipanga chilango chake kukhala chachitali
  80. Zonse zimene azilankhula iye zidzabwerera kwa Ife ndipo adzadza pamaso pathu yekha
  81. Anthu osakhulupirira adadzisankhira milungu ina kuti iwapatse mphamvu ndi ulemerero
  82. Ayi. Koma milunguyo idzakana kupembedza kwawo ndipo idzakhala adani awo
  83. Kodi siudaone kuti timatumiza kwa anthu osakhulupirira a Satana amene amawaonetsa zinthu zoti achimwe nazo
  84. Kotero musafulumize kuwapemphera chionongeko, ndithudi, tikuwawerengera masiku awo
  85. Tsiku limenetidzasonkhanitsaanthuolungamam’magulu kufika pamaso pa Ambuye wachisoni kudzalandira ulemu
  86. Ndipo tidzawakusa anthu oipa kupita ku moto wa ku Gahena ali ndi ludzu lodetsa nkhawa
  87. Palibe amene adzakhala ndi mphamvu zodandaula kupatula yekhayo amene walandira chilolezo cha Mwini chisoni chosatha
  88. Iwo amati, “Mwini chisoni chosatha wabala mwana wamwamuna.”
  89. Ndithudi mwanena chinthu choipitsitsa
  90. Pafupifupi kumwamba kumafuna kung’ambika chifukwa cha mawu amenewa ndipo nthaka imafuna kugawikana ndi mapiri kugudubuzika ndi kuonongeka
  91. Chifukwa chonena Mwini Chisoni Chosatha ali ndi mwana wamwamuna
  92. Si zoyenera kwa Mwini chisoni chosatha kuti akhale ndi mwana
  93. Palibe china chilichonse chimene chili kumwamba kapena pa dziko lapansi chimene chimabwera kwa Mwini chisoni chosatha kupatula ngati kapolo
  94. Iye wasunga chiwerengero cha zolengedwa zake zonse
  95. Ndipo onse, mmodzimmodzi, adzabwerera kwa Iye pa tsiku la kuuka kwa akufa
  96. Ndithudi amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, Mwini chisoni chosatha adzawakonda
  97. Motero Ife tapanga iyo kukhala yosavuta ya m’chiyankhulo chako kuti upeleke nkhani yabwino kwa anthu oopa ndi kuchenjeza ndi ilo anthu otsutsa
  98. Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaononga kale iwo asanadze? Kodi uli kumuona mmodzi aliyense wa iwo kapena kumva manong’onong’o ochokera kwa iwo