18.The Cave

  1. Kuyamikidwa konse kukhale kwa Mulungu amene wavumbulutsa kwa kapolo wake Buku ndipo sanaike mu ilo zokayikitsa zina zili zonse
  2. Lolungama kuti lichenjeze za chilango chowawa chochokera kwa Iye ndi kuwauza anthu okhulupirira amene amachita ntchito zabwino kuti adzalandira mphotho yabwino
  3. M’menemo adzakhalamo mpaka kalekale
  4. Ndi kuchenjeza iwo amene amanena kuti, “Mulungu wabereka mwana wamwamuna.”
  5. Pa izi iwo sadziwa china chilichonse, ngakhale makolo awo. Loopsa ndi liwu lalikulu limene likutuluka m’kamwa mwawo. Iwo sanena china koma bodza
  6. Mwina iwe ukhoza kudzipha ndi chisoni chifukwa chakuti iwo sakhulupirira chivumbulutsochi
  7. Ndithudi! Ife tazipanga zimene zili m’dziko lapansi kukhala zokongola ndi cholinga chakuti tiwayese kuti ndani mwa iwo ali wochita zabwino
  8. Ndithudi! Ife tidzapanga zonse zimene zili pa dziko kukhala nthaka youma
  9. Kodi iwe ukuganiza kuti anthu a ku phanga ndi malembo a pa gome ndi zozizwitsa pakati pa zizindikiro zathu
  10. Pamene anyamata adathawa ndipo adalowa ndi cholinga chopeza malo kuphanga ndipo adati, “Ambuye wathu! Tionetseni chisoni chochokera kwa Inu ndipo tikonzereni zinthu zathu munjira zoyenera.”
  11. Motero Ife tidawatseka makutu awo pamene anali kuphanga zaka zingapo
  12. Ndipo Ife tidawadzutsa kuti tidziwe ndani mwa magulu awiriwa amene adasunga bwino nthawi imene iwo adakhala kuphanga
  13. Ife tili kukuuza nkhani zawo zonse mwachoonadi. Ndithudi! Iwo anali anyamata amene adakhulupirira mwa Ambuye wawo, ndipo Ife tidawaonjezera malangizo
  14. Ndipo Ife tidalimbitsa mitima yawo, pamene adaima ndi kunena kuti, “Ambuye wathu ndiye Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi. Ife sitidzapembedza mulungu wina kupatula Iye yekha. Ngati tikatero ndiye kuti tayankhula bodza lopyola muyeso.”
  15. Awa anthu athu amatumikira milungu ina yoonjezera pa Iye. Kodi ndi chifukwa chiyani iwo sawabweretsera umboni woonekera weniweni? Kodi wochimwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu
  16. Pamene inu muwapewa iwo pamodzi ndi zimene iwo akupembedza osati Mulungu, thawirani kuphanga kuti mukapeze mpumulo. Ambuye wanu adzakutambasulirani chisoni chake ndi kukukonzerani njira yoti zinthu zikupepukireni
  17. Mwina iwe udaona dzuwa pamene linali kutuluka kupita ku mbali ya manja kwa phanga lawo ndipo pamene linali kulowa lilikudutsa ku mbali ya manzere, iwo adagona m’kati mwake. Chimenecho ndi chimodzi cha zizindikiro za Mulungu. Yense amene Mulungu amutsogolera ndi wotsogozedwa bwino koma iye amene Iye amusocheza, iwe siungam’pezere bwenzi woti amutsogolere
  18. Ndipo inu mukadaganiza kuti iwo adali maso pamene iwo adali mtulo. Ndipo Ife tinali kuwatembenuza kuchoka ku mbali ya manja kupita ku mbali ya manzere ndipo galu wawo adali chigonere ndi miyendo yake iwiri ya m’tsogolo ili yotambasula pa khomo la phanga. Iwe ukadaona iwo ukadachita mantha ndipo ukadathawa. Ndithudi iwe ukadadzadzidwa ndi mantha chifukwa cha iwo
  19. Chomwecho Ife tidawadzutsa kuti afunsane wina ndi mnzake. Wina wa iwo adafunsa nati, “Kodi inu mwakhala nthawi yotani? Iwo adayankha kuti: ‘Ife takhala tsiku limodzi kapena theka la tsiku.’ Iwo adati: “Ambuye wanu ndiye amene adziwa bwino za nthawi imene mwakhala kuno. Mtumizeni mmodzi wa inu ku mzinda ndi ndalama zanu za siliva kuti akagule chakudya chabwino kuti akubweretsereni. Koma akasamale ndipo asakauze aliyense za inu.”
  20. “Chifukwa ngati iwo adzadziwa za inu, adzakuponyani miyala kapena adzakubwezerani ku chipembedzo chawo. Ndipo zitatero inu simudzapambana ayi.”
  21. Motero Ifetidawadziwitsaanthuzaiwokutiiwoakhoza kudziwa kuti pangano la Mulungu ndi loona, ndipo kuti ola la chionongeko, ndithudi, lidzadza popanda chikayiko. Nthawi imene amakangana pa nkhani zawo za kuphanga iwo adati; ‘Amangireni nyumba pakhomo la phanga lawo. Ambuye wawo yekha ndiye amene adziwa za iwo.’ Ndipo iwo amene adapambana pa zochita zawo anati: “Ndithudi Ife tidzamanga malo opembedzerapo pamalopo.”
  22. Ena a iwo adati, Adali atatu ndipo galu wawo adali wachinayi, pamene ena akuti adali asanu ndipo galu wawo adali wachisanu ndi chimodzi. Moganizira zinthu zobisika, ena akuti adalipo asanu ndi awiri ndipo galu wawo adali wachisanu ndi chitatu. Nena, “Ambuye wanga ndi wodziwa kwambiri chiwerengero chawo, palibe amene akuwadziwa kupatula ochepa okha.” Usakangane nawo za iwo kupatula mkangano womveka. Ndipo usamufunse wina aliyense wa anthu zokhudza anthu a kuphanga
  23. Ndipo usanene za china chilichonse kuti, “Ine ndidzachita ichi mawa.”
  24. Opanda kuonjezera mawu oti, “Ngati Mulungu afuna.” Ndipo kumbukira Ambuye wako ngati uiwala ndipo unene kuti, “Ngati ndikotheka Mulungu anditsogolere ine ndi kundibweretsa kufupi ndi choonadi m’malo mwa ichi.”
  25. Iwo adakhala m’phanga lawo zaka mazana atatu ndi kuonjeza mphambu zisanu ndi zinayi
  26. Nena, “Mulungu amadziwa kwambiri mmene adakhalira. Kudziwa zinsinsi zonse za kumwamba ndi za dziko lapansi ndi kwake. Oh! Iye amapenyetsetsa ndipo amamvetsetsa. Iwo alibe wina woti awasamale oposa Mulungu. Ndipo Iye samuphatikiza wina aliyense mu ulamuliro wake.”
  27. Werenga zimene zavumbulitsidwa kwa iwe m’Buku la Ambuye wako. Palibe munthu amene angasinthe mawu ake. Iwe siudzapeza kothawira kupatula kwa Iye
  28. Pirira pamodzi ndi iwo amene akupembedza Ambuye wawo m’mawa ndi madzulo kufuna chisangalalo chake. Maso ako asayang’ane kutali kuwasiya iwo ndi cholinga chakuti upeze zinthu zabwino m’moyo uno ndipo usamumvere iye amene mtima wake tauiwalitsa kuti asamatikumbukire; ndipo watsatira zofuna za mtima wake, ndipo ntchito zake zonse ndi zoonongeka
  29. Nena, “Choonadi chimachokera kwa Ambuye wanu. Amene afuna akhulupirire ndipo amene safuna akane. Ndithudi anthu oipa tawakonzera moto umene mphanda zake zidzawazungulira.” Pamene iwo adzapempha madzi akumwa adzapatsidwa madzi otentha ngati mkuwa wosungunuka amene adzaotcha nkhope zawo. Kuipa kwa chakumwa ndi kuipa kwa malo okhala ndi kumeneku
  30. Kwa iwo amene akhulupirira nachita zabwino, ndithudi, Ife sitidzaononga mphotho ya anthu ochita zabwino
  31. Iwo adzakhala m’minda yamuyaya ndipo mitsinje izidzayenda pansi pawo. Iwo adzavekedwa zibangiri za golide ndipo adzavala nsalu za sirika wobiriwira, wopepuka ndi wochindikala ndipo adzatsamira pa masofa ndipo malipiro abwino ndi malo abwino ofikira
  32. Auze za fanizo la anthu awiri. Mmodzi wa iwo adali ndi minda iwiri ya mphesa imene tidazunguliza m’mbali mwake ndi mitengo ya tende ndipo tidaika pakati pake mbewu zina
  33. Munda uliwonse umapereka zipatso zake, ndipo siupunguza chilichonse ndipo Ife tidatumphutsa mitsinje m’kati mwa mindayo
  34. Ndipo Iye adali ndi zipatso zambiri ndipo adanena kwa mnzake pamene anali kutsutsana naye nati, “Ine ndili ndi chuma chambiri kuposa iwe ndiponso ndili ndi anthu a ntchito amphamvu kwambiri.”
  35. Ndipo iye adalowa m’munda mwake modzitukumula yekha nati, “Ine sindiganiza kuti izi zidzatha ayi.”
  36. “Ndipo ine sindikhulupirira kuti ola la chionongeko lidzadza. Ndipo ngakhale nditabwezedwa kwa Ambuye wanga, ine ndikapeza malo abwino oposa awa.”
  37. Mnzake uja adati kwa iye, “Kodi iwe wam’kana Iye amene adakulenga iwe kuchokera ku dothi ndi kuchokera ku dontho la umuna ndipo adakuumba kukhala munthu?”
  38. Akakhala ine, Mulungu ndiye Ambuye wanga. Ine sindidzamufanizira Iye ndi china chilichonse
  39. Bwanji pamene iwe umalowa m’munda mwako, siudanene kuti, “Izi ndi zimene Mulungu wafuna ndipo kulibe mphamvu kwina kulikonse kupatula kwa Mulungu? Ngakhale iwe ukundiona ine kuti ndine wochepekedwa kwambiri m’chuma ndi ana.”
  40. “Mwina Ambuye wanga akhoza kundipatsa munda wabwino oposa wako ndi kutumiza ziphaliwali kuchokera kumwamba ndi kusandutsa nthaka kukhala yosabereka.”
  41. “Kapena kuzamitsa madzi ake kuti iwe usawapeze.”
  42. Ndipo zipatso zake zidaonongeka. Ndipo iye adayamba kufikisa zikhato zake mwachisoni chifukwa cha zonse zimene adaononga pa mindayi chifukwa zonse zidaonongeka. Ndipo iye adati: “Kalanga ine! Ndikanadziwa, sindikanaphatikiza milungu ina ndi Ambuye wanga!”
  43. Ndipo iye adalibe gulu lomuthandiza polimbana ndi Mulungu ndiponso adalibe mphamvu zoti adzitetezere kapena kudzipulumutsira
  44. Kumeneko chitetezo chidzakhala chochokera kwa Mulungu, Mwini choonadi. Iye ndiye ali ndi malipiro ndiponso mapeto abwino
  45. Uwapatse chitsanzo cha moyo wa padziko lapansi. Moyowu uli ngati madzi amene timatsitsa kumwamba ndi mbeu za padziko la pansi zimene zimasakanizana ndi iwo ndipo zimakhala zanthete ndi zobiliwira. Koma pambuyo pake zimauma ndi kufumbutuka ndipo mphepo imazimwaza. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse
  46. Chuma ndi ana ndi zinthu zokongola za umoyo wadziko lapansi. Koma ntchito zabwino zokhalitsa ndi zomwe zili ndi malipiro abwino kwa Ambuye wako ndi chiyembekezo chabwino
  47. Ndi tsiku limene tidzagudubuza mapiri ndipo mudzaona nthaka ili kukhala poyera popanda chilichonse ndipo Ife tidzasonkhanitsa anthu onse. Palibe aliyense amene tidzamusiye mwa iwo
  48. Ndipo iwo adzaonetsedwa kwa Ambuye wako ataimikidwa m’mizere ndipo tidzanena kuti, “Ndithudi inu mwabwera kwa Ife monga momwe tidakulengerani poyamba. Koma inu munali kuganiza kuti lonjezo lathu silidzakwaniritsidwa ayi.”
  49. Ndipo Buku lidzaikidwa m’manja mwa aliyense ndipo iwe udzaona anthu ochita zoipa ali ndi mantha poona zonse zimene zidalembedwa mu Bukulo. Iwo adzati, “Tsoka kwa ife! Kodi Buku ili ndi lotani limene silisiya kanthu kakang’ono kapena kakakulu ndipo zonse lidasunga?” Ndipo iwo adzapeza ntchito zawo zonse zitalembedwa momwemo ndipo Ambuye wako sadzapondereza wina aliyense
  50. Pamene Ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Motero onse anamugwadira Iye kupatula Satana amene adali mmodzi wa ziwanda ndipo adanyoza lamulo la Ambuye wake. Kodi mudzasankha iyeyo pamodzi ndi ana ake kukhala okutetezani ndi kukuthandizani m’malo mwa Ine, pamene iwo ndi adani? Kodi ndi choipa chotani chimene anthu ochita zoipa asankha
  51. Ine sindidawaonetse kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi kapena kalengedwe kawo komwe ndiponso Ine sindidawasankhe, osocheretsa anthu, kukhala ondithandiza anga
  52. Ndi tsiku limene Iye adzati kwa iwo, “Itanani onse amene mumandifanizira aja, amene munkadzinamiza aja.” Ndipo iwo adzalira kwa iwo koma sadzawayankha ndipo Ife tidzabzala chidani pakati pawo
  53. Ndipo anthu ochimwa adzaona moto wa ku Gahena ndipo adzatsimikiza kuti iwo aulowa. Ndipo iwo sadzapeza njira yothawirako
  54. Ndithudi Ife tawakhazikitsira anthu chitsanzo chilichonse mu Korani ino. Koma munthu ndi wotsutsa muzinthu zambiri
  55. Palibe chimene chimawaletsa anthu kukhulupirira ndi kupempha chikhululukiro kwa Ambuye wawo pamene chilangizo chidza kwa iwo kupatula kuti ali kudikira njira za anthu a zaka zakale kuti ziwapeze iwo kapena kuti akumane ndi mazunzo maso ndi maso
  56. Ndipo Ife sitimangotumiza Atumwi kupatula kuti akalalikire nkhani yabwino ndi kupereka chenjezo. Koma anthu osakhulupirira amatsutsa mwabodza kuti agonjetse choonadi ndi bodza lawo. Ndipo iwo amasandutsa mawu anga ndi zonse zomwe achenjezedwa ngati nthabwala kapenachoseketsa
  57. Kodiwolakwakwambirindanikuposa munthu amene akakumbutsidwa mavesi a Ambuye wake iye amawakana ndi kuiwala zimene manja ake atsogoza? Ife taika zophimba mitima yawo kuti asazindikire ndipo tatseka m’makutu mwawo. Ndipo ngati iwe utawaitana iwo kuti atsatire njira yoyenera, iwo sadzatsogozedwa
  58. Ndipo Ambuye wako ndi wokhululukira kwambiri ndi Mwini chisoni. Iye akadafuna kuwalanga chifukwa cha machimo amene achita, ndithudi, Iye akadawafulumizitsira chilango chawo. Koma iwo ali ndi nthawi yawo ndipo sadzapeza kothawirako
  59. Ndi Mizinda, imene tidaiononga pamene eni ake adachita zoipa tidaika nthawi yachionongeko chawo
  60. Ndipo pamenepo Mose adamuuza mnyamata wake kuti, “Ine ndidzapitirirabe kuyenda mpaka pamene ndidzafika pamalo pamene nyanja ziwiri zikumana kapena ndidzapitirira kuyenda zaka ndi zaka.”
  61. Koma pamene iwo adafika pamalo pamene nyanja ziwiri zidakumana, iwo adaiwala nsomba yawo ndipo iyo idatenga njira yake yodutsa kupita m’madzi
  62. Ndipo iwo atapitiriza ulendo wawo, Mose adati kwa mnyamata wake, “Bweretsa chakudya chathu. Ndithudi tapeza, mu ulendo wathu, zotopetsa.”
  63. Iye adati, “Kodi iwe siudaone pathanthwe pamene tidapuma paja, kuti ine ndidaiwala nsomba ndipo palibe china chimene chidandiiwalitsa kuti ndiikumbukire koma Satana yemwe adandiiwalitsa. Ndipo iyo idalowa m’madzi mozizwitsa.”
  64. Mose adati, “Pamenepo ndi pamene timafuna.” Iwo adabwerera kulondola kumene adachokera
  65. Ndipo iwo adam’peza mmodzi wa akapolo wathu amene tidamupatsa chifundo chochokera kwa Ife ndiponso tidamuphunzitsa nzeru zochokera kwa Ife
  66. Mose adati kwa iye, “Kodi ndingakutsateni kuti mwina mundiphunzitse zabwino zina za zimene mudaphunzitsidwa?”
  67. Iye adati, “Ndithudi! Iwe siudzatha kupirira ndi ine.”
  68. Kodi iwe ungapirire bwanji pa zinthu zimene suli kuzidziwa
  69. Mose adati, “Ngati Mulungu afuna, udzandipeza ine ndili wopirira ndipo ine sindidzakunyoza iwe ayi.”
  70. Iye adati, “Ngati iwe unganditsatire, usandifunse china chilichonse chimene ungawone mpaka pamene ine nditakuuza za chinthucho.”
  71. Motero iwo adanyamuka ndipo pamene iwo adakwera m’chombo, mnzake wa Mose adaboola chombocho. Mose adati, “Kodi waboola dzenje pa chombochi ndi cholinga chofuna kumiza eni ake? Ndithudi ichi ndi chinthu choipa kwambiri chimene wachita!”
  72. Iye adati, “Kodi sindidakuuze kuti iwe siudzatha kupirira ndi ine?”
  73. Mose adati, “Musandidzudzule chifukwa cha zimene ndaiwala ndipo musandisenzetse katundu wolemera chifukwa cha zochita zanga.”
  74. Ndipo onse adapitirizabe ulendo wawo mpaka pamene adakumana ndi mnyamata wina amene iye adamupha. Ndipo Mose adati, “Kodi iwe wapha munthu wosalakwa amene sadaphepo wina aliyense? Ndithudi iwe wachita chinthu choipa kwambiri.”
  75. Iye adati, “Kodi ine sindidakuuze kuti iwe siudzatha kupirira ndi ine?”
  76. Mose adati, “Ngati ine ndikufunsanso chinthu china pambuyo pa izi, usayende nanenso chifukwa ukhala utachipeza chifukwa kuchokera mwa ine.”
  77. Ndipo onse adapitirira kuyenda mpaka pamene adapeza anthu a mu mzinda wina wake ndipo iwo adawafunsa anthu aja kuti awapatseko chakudya koma iwo adakana kuwalandira ngati alendo awo. Iwo adapeza mu mzindawo chipupa chikufuna kugwa ndipo Iye adachimanganso. Mose adati, “Iwe ukadafuna, ndithudi, ukadawauza kuti akulipire chifukwa cha ntchito imene wagwira.”
  78. Iye adati, “Uku ndiye kusiyana kwa pakati pa iwe ndi ine. Ndikuuza tanthauzo la zinthu zimene iwe umakanika kupirira nazo.”
  79. Chikakhala chombo chija eni ake adali anthu osauka amene amagwira ntchito pa nyanja. Ndipo ine ndinafuna kuti ndichiononge chifukwa kutsogolo kwawo kudali mfumu yomwe imalanda chombo chilichonse mwamphamvu
  80. Akakhala mnyamata uja, makolo ake onse adali okhulupirira mu choonadi ndipo timaopa kuti mwina iye akhoza kuwatembenuza ndi kuyamba kuchita zoipa ndi kusiya kukhulupirira
  81. Ndipo tidafuna kuti Ambuye wawo awapatse m’malo mwake, mwana wina wabwino ndi woyera mtima kuposa iye
  82. Chikakhala chipupa chija, eni ake adali ana awiri a masiye amene amakhala mu mzinda uja ndipo pansi pa chipupacho padali chuma chawo. Ndipo bambo wawo adali munthu wabwino motero Ambuye wako adafuna kuti anawo akule kuti adzatulutse okha chuma chawo ngati chifundo chochokera kwa Ambuye wako. Ine sindidachite zimenezi mwachifuniro changa ayi. Limeneli ndilo tanthauzo lake la zinthu zimene umalephera kupirira nazo
  83. Ndipo iwo akukufunsa za Dhul-Qarnain. Nena, “Ine ndikufotokozerani za mbiri ya iye.”
  84. Ndithudi Ife tidamukhazika iye padziko ndipo tidamupatsa njira yopezera chilichonse
  85. Ndipo iye adatsatira njira
  86. Mpaka pamene adafika polowera dzuwa ndipo adalipeza dzuwalo lili kulowa m’dziwe la matope akuda. Pafupi pomwepo iye adapeza anthu ena. Ife tidati, “Iwe Dhul-Qarnain! Iwe uli ndi ufulu wowalanga kapena wowachitira chisoni.”
  87. Iye adati, “Akakhala iye amene achita zoipa, tidzamulanga ndipo iye adzabwezedwa kwa Ambuye wake yemwe adzamulanga ndi chilango choipa kwambiri.”
  88. Koma iye amene wakhulupirira ndikumachita ntchito zabwino, adzakhala ndi mphotho yabwino ndipo tidzamuyankhula mawu abwino
  89. Ndipo iye adatsatira njira ina
  90. Mpaka pamene adafika kotulukira dzuwa kumene adalipeza dzuwa lili kutuluka pa anthu amene Ife sitidawaikire chotchinga ku dzuwa
  91. Kotero Ife tidadziwa zonse zokhudza iye
  92. Ndipo iye adatsatiranso njira ina
  93. Mpaka pamene iye adafika pakati pa mapiri awiri adapeza pambali pake anthu amene sanali kuzindikira chilichonse
  94. Iwo adati, “Iwe Dhul-Qarnain! Ndithudi Ya-juj ndi Majuj ali kuchita zoipa m’dziko lino. Kodi tikupatse malipiro kuti utimangire linga lotiteteza nalo pakati pa iwo ndi ife?”
  95. Iye adati, “Mphamvu zomangira linga zimene Ambuye wanga wandipatsa ndi zabwino. Choncho ndithandizeni ndi anthu amphamvu ogwira ntchito kuti ndimange linga pakati pa inu ndi iwo.”
  96. Ndipatseni zidutswa zachitsulo; mpaka pamene iye adadzadza gawo limene linali pakati pa mapiriwa. Iye adati, “Uzirani ndi livumbo lanu.” Pamene adazifiwiritsa zidutswazo ngati moto, iye adati, “Ndipatseni mtovu kuti ndiuthire pa zidutswazo.”
  97. Anthu a Ya-juj ndi Majuj sadathe kuchilumpha ndipo sadathe kuchiboola
  98. Iye adati, “Ichi ndi chifundo chochokera kwa Ambuye wanga. Koma pamene lonjezo la Ambuye wanga lidzadza, Iye adzaliononga. Ndipo lonjezo la Ambuye wanga ndi loona
  99. Ndipo pa tsikulo tidzawasiya ena mwa iwo akusakanikirana ndi ena. Lipenga lidzaimbidwa ndipo tidzawasonkhanitsa onse pamodzi
  100. Pa tsiku limeneli tidzaonetsa Gahena kwa anthu osakhulupirira, kuti adzalione lonse moonekera kwambiri
  101. Amene maso awo adali otsekeka kuchikumbutso changa, satha kumva
  102. Kodi anthu osakhulupirira akuganiza kuti akhoza kuwapanga akapolo anga kukhala atetezi awo m’malo mwa Ine? Ndithudi Ife takonza Gahena kukhala malo ofikira anthu onse osakhulupirira
  103. Nena, “Kodi tikuuzeni anthu amene ali olephera mu ntchito zawo?”
  104. Iwowo ndi amene ntchito zawo zaonongeka m’moyo uno pamene iwo anali kuganiza kuti ali kulandira zabwino chifukwa cha ntchito zawo
  105. Iwo ndi amene sadakhulupirire mawu a Ambuye wawo ndi zokumana ndi Iye. Motero ntchito zawo zaonongeka ndipo patsiku lachiweruzo Ife sitidzawakhazikira muyeso
  106. Gahena idzakhala mphotho yawo chifukwa iwo adalibe chikhulupiriro ndipo achitira chipongwe Atumwi ndiponso mawu anga
  107. Ndithudi! Iwo amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, minda ya ku Paradiso idzakhala malo awo ofikira
  108. Adzakhala komweko nthawi zonse ndipo sadzafuna kusintha malo
  109. Nena, “Ngati Nyanja ikadakhala inki yolembera mawu Ambuye wanga, ndithudi, nyanjayo ikadaphwa koma osati Mawu a Ambuye wanga ngakhale tikadabweretsa nyanja yofanana ndi imeneyo moonjezera.”
  110. Nena, “Ine ndine munthu monga inu nomwe, koma zavumbulutsidwa kwa ine kuti Mulungu wanu ndi mmodzi. Kotero aliyense amene afuna kudzakumana ndi Ambuye wake ayenera kuchita zimene zili zabwino ndipo popembedza Ambuye wake, osaphatikizamo wina wake.”