16.The Bee
- Chiweruzo cha Mulungu chidzabwera, ndipo kotero musachifulumizitse. Kulemekezeka ndi kuyamikidwa kukhale kwa Iye kuposa zonse zimene akumufanizira
- Iyeamatsitsaangelondimawuakeamalamulokwaakapolo ake amene wawafuna ndikuwauza kuti muwachenjeze iwo kuti, “Kulibe Mulungu wina koma Ine ndekha. Kotero ndiopeni Ine.”
- Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi. Iye akhale kutali ndi zimene akumufanizira nazo
- Iye ndiye adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna ndi la ukazi ndipo taonani iye amatsutsa poyera
- Iye adakulengerani nyama ndipo mu izo mumapeza zofunda ndi zithandizo zina ndiponso nyamazo mumadya
- Ndipo mumanyadira pamene mumazisaka kudza nazo ku nyumba kwanu madzulo ndi pamene mumapita nazo kuubusa kukazidyetsa m’mawa
- Ndipo izo zimanyamula katundu wanu wolemera kupita kumalo kumene inu simutha kukafikako kupatula movutikira. Ndithudi Ambuye wanu ndi Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha
- Ndipo adalenga akavalo, abulu ndi mahatchi kuti muzikwera ndi kukongoletsa. Ndipo adalenganso zina zimene simuzidziwa
- Zili kwa Mulungu kusonyeza njira yoyenera, koma pali njirazinazopatukandipo Iyeakadafunaakadakutsogolerani nonse
- Iye ndiye amene amatsitsa madzi kuchokera ku mitambo omwe inu mumamwa ndipo amameretsa mitengo imene mumadyetsa ziweto
- Kudzera m’menemu, Iye amakumeretserani mbewu ndi mitengo ya mafuta, mitengo ya tende ndi mphesa ndiponso zipatso zina. Ndithudi! Mu ichi muli chizindikiro kwa anthu a maganizo abwino
- Ndipo adakupeputsirani usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, mwalamulo lake. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira
- Ndipo chilichonse chimene adakulengerani padziko lapansi adachilenga cha mitundu yosiyanasiyana. Kotero chilichonse chili ndi chisonyezo kwa anthu omwe amasangalala ndi matamando a Mulungu
- Iye ndiye amene adakupeputsirani nyanja kuti inu muzidya nyama yaiwisi kuchokera mu iyo ndi kutulutsa zovala zokongola zimene mumavala. Ndipo mumaona ngalawa zili kuyenda pa nyanja. Adalenga zonsezi kuti muzipezamo zokoma zake ndi kuti muzikhala othokoza
- Ndipo Iye adakhazikitsa mapiri padziko lapansi kuti lisagwedezeke pamodzi ndi inu, mitsinje ndi misewu kuti mutsogozedwe munjira zabwino
- Ndi zizindikiro zina zokutsogolerani, nyenyezi nazonso anthu amatsogozedwa nazo
- Kodi Iye amene amalenga angafanane ndi Iye amene salenga? Kodi inu simungakumbukire
- Ngati inu mutawerenga zokoma za Mulungu simungakwaniritse kuziwerenga. Ndithudi! Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
- Ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumabisa ndi zimene mumaonetsera
- Koma milungu yabodza imene anthu osakhulupirira amapembedza m’malo mwa Mulungu, siinalenge china chilichonse ayi chifukwa nayonso ndi yolengedwa
- Iyo ndi yakufa, si yamoyo ayi ndiponso iyo siidziwa nthawi imene idzaukitsidwe
- Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi yekha. Koma iwo amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza, mitima yawo imakana ndipo iwo ndi odzikweza
- Mosakayika, ndithudi, Mulungu amadziwa zonse zimene iwo amabisa ndi zimene amaonetsera. Ndithudi, Iye sakonda anthu odzikweza
- Pamene amafunsidwa kuti, “Kodi Ambuye wanu wavumbulutsa zotani?” Iwo amati, “Nkhani zopeka za anthu a kalekale.”
- Iwo adzanyamula katundu wawo okwanira pa tsiku la kuuka kwa akufa pamodzi ndi katundu wa iwo amene adawasocheretsa mu umbuli. Ndithudi zoipa ndi zimene akusenza
- Iwo amene adalipo kale adakonza chiwembu koma Mulungu adaphwanya nyumba zawo kuyambira pa maziko ake ndipo denga lidawagwera kuchokera pamwamba pawo ndipo chilango chidadza pa iwo kuchokera ku mbali imene iwo sanali kuganiza
- Ndipo patsiku la kuuka kwa akufa Iye adzawachititsa manyazi ndipo adzati, “Zili kuti zimene munkandifanizira nazo, zimene inu mumakangana ndi Aneneri chifukwa cha izo?” Iwo amene adapatsidwa nzeru adzati, “Ndithudi! Zochititsa manyazi ndiponso zoipa ziwagwera lero lino anthu osakhulupirira.”
- Iwo amene angelo amawatenga ali odzipondereza okha, adzagonja mwachinyengo ponena kuti, “Ife sitinali kuchitachoipa.”Angeloadzati,“Indedi! Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene munali kuchita.”
- “Kotero lowani m’zipata za Gahena, kumeneko mudzakhalako mpaka kalekale. Ndithudi ndi oipa malo a anthu odzikweza.”
- Ndipo kwa anthu oopa zidzanenedwa kuti, “Kodi Ambuye wanu adavumbulutsa zotani?” Iwo adzati, “Zabwino.” Mphotho yabwino idzakhala ya iwo amene adachita ntchito zabwino m’moyo uno. Koma nyumba yabwino kwambiri ndi mphotho ya moyo umene uli nkudza ndi mtendere wabwino ndiponso nyumba ya anthu oopa Mulungu
- Iwo adzalowa m’minda yamuyaya ndipo mitsinje idzayenda pansi pake. Iwo, kumeneko, adzapeza zonse zimene adzazifuna. Mmenemu ndi mmene Mulungu adzawalipirire anthu oopa Mulungu
- Iwo amene angelo amatenga miyoyo yawo ali kuchita zabwino, Angelo adzanena kuti, “Mtendere ukhale kwa inu. Lowani mu Paradiso, chifukwa cha ntchito zabwino zimene munkachita.”
- Kodi iwo akudikira kuti angelo adze kwa iwo kapena kuti libwere lamulo kuchokera kwa Mulungu wanu? Chomwecho ndicho adachita iwo amene adalipo kale. Mulungu sadawapondereze koma iwo adadzipondereza okha
- Ndipo mavuto adawapeza iwo chifukwa cha zimene adachita ndipo adawazungulira masautso a zinthu zimene iwo amazikana
- Ndipo anthu opembedza mafano amati, “Mulungu akadafuna, ife kapena makolo athu, sitikadapembedza milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni ayi ndiponso ife sitikadaletsa china chilichonse opanda chilolezo chake.” Mmenemo ndimo adachitira anthu amene adalipo kale iwo asanadze. Kodi Atumwi adapatsidwa china kupatula kupereka Uthenga momveka
- Ndithudi! Ife tidatumiza Mtumwi pakati pa mtundu uliwonse amene amanena kuti, “Pembedzani Mulungu ndipo mupewe milungu yabodza.” Pakati pawo padali ena amene Mulungu adawatsogolera ndi ena mwa iwo amene kusochera kwawo kudali koyenera. Yendani pa dziko lonse lapansi ndipo mukaone kuti adali bwanji mapeto a anthu osakhulupirira
- Ngati iwe ufunitsitsa kuti iwo atsogozedwe, ndithudi, Mulungu satsogolera amene wamusocheretsa. Ndipo iwo sadzapeza owathandiza
- Iwo adalumbira mwamphamvu M’dzina la Mulungu kuti, “Mulungu sadzaukitsa munthu wakufa.” Inde, ndi lonjezo la Mulungu loona ndipo lidzakwaniritsidwa, koma anthu ambiri sadziwa
- Kuti Iye adzawaonetse zoonadi zimene iwo amatsutsana ndi kuti iwo amene sakhulupirira adziwe kuti adali onama
- Ndithudi liwu lathu pa chinthu chimene tachifuna ndi lakuti timangonena, “Khala” ndipo chimakhala
- Ndi iwo amene adasamuka ndi cholinga chokondweretsa Mulungu pambuyo poponderezedwa, Ife, ndithudi, tidzawakhazika padziko mwamtendere. Koma malipiro a tsiku lachiweruzo adzakhala aakulu kwambiri iwo akadadziwa
- Iwo amene adapirira ndipo adaika chikhulupiriro mwa Ambuye wawo
- Iwe usanadze Ife sitidatumizepo, ena koma amuna amene tidawapatsa chivumbulutso chathu. Kotero afunse iwo odziwa mawu a Mulungu ngati iwe siukudziwa
- Ndi zizindikiro zooneka ndiponso mabuku opatulika, Ife tavumbulutsa kwa iwe chikumbutso kuti ulalikire anthu zonse zimene zatumizidwa kwa iwo ndi kuti akhoza kulingirira
- Kodi iwo amene amakonza chiwembu ndi odzikhulupirira kuti Mulungu sangawakwirire m’nthaka kapena kuti chilango sichingagwe pa iwo kuchokera ku mbali imene sali kuiyembekezera
- Kapena iwo ali ndi chikhulupiriro chakuti Iye sadzawagwira iwo m’maulendo awo pamene sangathe kuthawa
- Kapena kuti Iye sangawapatse chionongeko cha pang’onopang’ono? Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha
- Kodi iwo sakuziona zinthu zimene Mulungu adalenga mmene zimagwetsera mithunzi yake kumbali ya dzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere, kumulambira Mulungu modzichepetsa
- Ndipo kwa Mulungu zimagwada zinthu zonse za mlengalenga ndi za padziko lapansi ndi zonse za moyo ndi angelo, ndipo sizidzikweza
- Izo zimaopa Ambuye wawo amene ali pamwamba pawo ndipo zimachita monga momwe zalamulidwira
- Mulungu adati, “Inu musapembedze milungu iwiri ayi. Ndithudi Iyendi Mulungummodziyekha. Koterondiopeni Ine.”
- Ndipo zonse zimene zili mlengalenga ndi m’dziko lapansi ndi zake ndipo Iye yekha ayenera kupembedzedwa basi. Kodi inu mudzaopa wina wake wosati Mulungu
- Ndipo zokoma zonse zimene mumalandira zimachokera kwa Mulungu. Ndipo pamene mavuto akupezani, inu mumapempha chithandizo kwa Iye
- Koma Iye akakuchotserani inu mavuto, taonani! Ena mwa inu mumaphatikiza Ambuye wanu ndi mafano mukamapembedza
- Motero iwo amakana zimene tawapatsa! Choncho basangalalani pang’ono koma posachedwapa mudzadziwa choonadi
- Ndipo iwo amapereka gawo lina la zinthu zimene tawapatsa ku zinthu zimene iwo sazidziwa. Pali Mulungu, inu mudzafunsidwa zinthu zonse zabodza zimene mumapeka
- Ndipo iwo amamupatsa Mulungu ana aakazi. Ayeretsedwe Ambuye ndipo Iye akhale pamwamba pa zonse zimene amaziphatikiza ndi Iye ndi zimene iwo amafuna
- Ndipo pamene kubadwa kwa mwana wamkazi kumemezedwa kwa wina wa iwo, nkhope yake imada ndipo amadzadzidwa ndi chisoni
- Iye amadzibisa kuti asaonane ndi anthu ake chifukwa cha nkhani yoipa imene wauzidwa. Kodi mwanayu akhale naye ndi manyazi kapena kuti akamukwirire m’nthaka? Ndithudi chiweruzo chawo ndi choipa kwambiri
- Iwo amene sakhulupirira zatsiku lachiweruzo ali ndi mbiri yoipa pamene Mulungu ali ndi mbiri yaulemerero. Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndiponso ndi Wanzeru
- Akadakhala kuti Mulungu anali kulanga anthu msanga chifukwa cha zoipa zawo, palibe cholengedwa ndi chimodzi chomwe chimene Iye akadachisiya ndi moyo. Koma Iye amawasunga mpaka tsiku lokhazikitsidwa, ndipo ngati nthawi yawo ikwana, ngakhale ndi kamphindi kochepa, iwo sangaichedwetse kapena kuifulumizitsa
- Iwo amamupatsa Mulungu zinthu zimene iwo amazida, ndipo malirime awo amanena bodza lakuti mphotho yabwino ili kuwayembekezera. Mosakayika kwawo ndi kumoto ndipo iwo adzakhala oyamba kuponyedwako ndipo adzasiyidwa m’menemo osasamalidwa
- Pali Mulungu, ndithudi, Ife tidatumiza Atumwi ena, ku mibadwo ina, iwe usanadze. Koma Satana adasandutsa ntchito zawo zoipa kuti zikhale zabwino kwa iwo. Motero Satana ndiye bwenzi lawo. Chawo chidzakhala chilango chowawa zedi
- Ndipo Ife sitinavumbulutse Buku kwa iwe kupatula kuti iwe uwauze anthu poyera choonadi cha zinthu zimene ali kukangana ndiponso ngati chilangizo ndi dalitso kwa anthu okhulupirira moonadi
- Mulungu amatsitsa madzi kuchokera ku mtambo ndipo Iye amadzutsira nthaka pambuyo poti idafa. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu akumva
- Ndithudi! Mu nyama muli phunziro kwa inu. Ife timakupatsani kuti muzimwa zina mwa zomwe zili m’mimba mwake kuchokera pakati pa ndowe ndi magazi. Mkaka wabwino, chakumwa chabwino kwambiri kwa iwo amene amamwa
- Ndipo kuchokera ku zipatso za mitengo ya tende ndi mitengo ya mphesa, inu mumapanga zakumwa zoledzeretsa ndiponso chakudya chabwino. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu amene ali ndi nzeru
- Ambuye wako adauza njuchi kuti, “Mangani nyumba zanu m’mapiri, m’mitengo ndi m’ming’oma imene anthu amakonza.”
- “Ndipo idyani zipatso za mitundu yonse, ndipo yendani m’njira za Ambuye wanu mosavutika.” Kuchokera m’mimba mwa njuchi, mumatuluka zakumwa zamitundu yosiyanasiyana ndipo m’menemo muli mankhwala ochiza anthu. Ndithudi mu izi muli zizindikiro kwa iwo amene amalingilira
- Mulungu ndiye amene adakulengani inu ndipo adzakuphani. Ndipo ena a inu amakalamba koti sangathe kuzidziwa zinthu zimene anali kuzidziwa kale. Ndithudi! Mulungu amadziwa chilichonse ndiponso ali ndi mphamvu zonse
- Ndipo Mulungu wawalemekeza ena a inu kuposa ena powapatsa chuma chambiri. Ndipo iwo amene apatsidwa zambiri sadzapereka ngakhale zitavuta chotani chuma chawo kwa akapolo awo kuti mwina akhoza kufanana pa chuma. Kodi iwo amakana zokoma za Mulungu
- Ndipo Mulungu wakupatsani akazi kuchoka pakati panu ndipo kudzera mwa iwo wakupatsani ana aamuna ndi zidzukulu ndipo Iye wakupatsani zinthu zabwino. Kodi iwo tsopano adzakhulupirira mu zinthu zabodza ndikukana ubwino wa Mulungu
- Ndipo iwo amapembedza mafano mowonjezera pa Mulungu amene sangathe kuwapatsa chithandizo chilichonse kuchokera kumwamba kapena padziko lapansi
- Motero musafanizire wina aliyense ndi Mulungu. Ndithudi Mulungu amadziwa pamene inu simudziwa chilichonse
- Mulungu akupereka fanizo la kapolo amene ali mu ulamuliro wa bwana wake amene sangathe kuchita chilichonse ndi munthu wina, amene tamupatsa zinthu zabwino ndipo iye amapereka kuchokera ku zimene wapatsidwa mwamseri ndiponso moonekera. Kodi iwo angafanane? Kuyamikidwa konse kukhale kwa Mulungu, koma ambiri a iwo sazindikira
- Ndipo Mulungu ali kuperekanso fanizo la anthu ena awiri, mmodzi wa iwo wosayankhula amene sangathe kuchita chilichonse, ndi wosathandiza Ambuye wake chifukwa kulikonse kumene amamutuma iye sabweretsa chabwino. Kodi iyeyu ndi wofanana ndi iye amene amalamula mwachilungamo ndipo ali m’njira yoyenera
- Zinsinsi zimene zili mlengalenga ndi pa dziko lapansi zonse ndi za Mulungu. Ntchito yokhudza ola lomaliza idzagwiridwa mu nthawi ngati kuphethira kwa diso kapena kufulumira koposerapo apa. Ndithudi Mulungu amatha kuchita chilichonse
- Ndipo Mulungu adakutulutsani kuchokera m’mimba mwa amayi anu muli osadziwa china chilichonse ndipo adakupatsani makutu, maso, ndi mitima kuti muzithokoza
- Kodi iwo saona mbalame zomwe zimauluka mlengalenga? Palibe wina amene amazigwira kuti zisagwe pansi koma Mulungu yekha. Ndithudi mu ichi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira
- Ndipo Mulungu wakupangirani nyumba zanu kuti muzikhalamo ndipo wakupangirani nyumba kuchokera kuzikopa za nyama, zomwe mumaona kuti zimakupepukirani ponyamula ndikumakhala pamodzi ndi ubweya umene mumakonzera zinthu zina zofunika
- Ndipo Mulungu wakupangirani kuchokera ku zinthu zimene adalenga mthunzi ndipo wakupangirani malo othawirako m’mapiri ndipo Iye wakupangiraninso zovala kuti zizikutetezani kukatentha ndi zovala zokutetezani ngati chishango nthawi ya nkhondo. Mmenemo ndimo mmene amakwaniritsira ubwino wake pa inu kuti mukhale odzipereka mwahifuniro chake
- Koma ngati iwo samvera, udindo wako ndi kufikitsa uthenga moonekera
- Iwo amazindikira ubwino wa Mulungu komabe amaukana ndipo ambiri a iwo ndi anthu osakhulupirira
- Ndipo patsiku limene Ife tidzadzutsa mboni kuchokerakumtunduuliwonse, iwoamenesanakhulupirire sadzapatsidwa mwayi
- Ndipo pamene ochita zoipa adzaona chilango, mavuto awo sadzachepetsedwa ndipo sadzapatsidwa mpumulo
- Ndipo anthu opembedza mafano akadzaona mafano awo, iwo adzati, “Oh Ambuye wathu! Awa ndi mafano athu amene tinali kupembedza kuonjezera pa inu.” Koma mafano awo adzayankha opembedzawo nati, “Ndithudi! Inu ndinu abodza.”
- Patsiku limeneli, iwo adzaonetsera poyera kugonja kwawo kwa Mulungu ndipo mafano awo onse adzawathawira iwo
- Kwa iwo amene sadakhulupirire ndipo adatsekereza anzawo kutsatira njira ya Mulungu, Ife tidzawaonjezera chilango kuonjezera pa chilango china, chifukwa cha ntchito zawo zoipa zimene anali kufalitsa
- Ndipo patsikulo tidzadzutsa kuchokera ku mtundu uliwonse amene adzawachitira umboni wochokera pakati pawo. Ndipo tidzakubweretsa iwe kukhala mboni ya anthu awa. Ndipo takuvumbulutsira Buku lolongosola zonse, chilangizo, madalitso ndi nkhani yabwino kwa omwe amagonjera Mulungu
- Ndithudi Mulungu amalamulira chilungamo, kupirira pogwira ntchito ya Mulungu, ubwino ndi kupereka chaulere kwa abale. Ndipo amaletsa ntchito zoipa, zonyansa ndi kuponderezana. Iye ali kukuchenjezani kuti mukhale okumbukira
- Kwaniritsani pangano la Mulungu mukalonjeza ndipo musaphwanye malonjezo anu mutatsimikiza. Ndithudi inu mwamupanga Mulungu kukhala mboni yanu yodalirika. Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
- Musakhale ngati mkazi amene wadula ulusi wa nsalu imene amasoka italimba polumbira mwachinyengo pakati panu kuti mwina gulu lina lingakhale lopambana kuposa gulu linzake. Ndithudi mu ichi Mulungu amakuyesani. Ndipo patsiku la kuuka kwa akufa, Iye adzakuululirani zoona zokhazokha za izo zimene munali kusemphana maganizo
- Ndipo Mulungu akadafuna, akadakupangani inu kuti mukhale mtundu umodzi. Koma Iye amasocheretsa amene Iye wamufuna ndipo amamutsogolera Iye amene wamufuna. Ndithudi inu mudzafunsidwa za ntchito zanu zonse zimene munali kuchita
- Musasandutse kulumbira kwanu kukhala chinyengo pakatipanuchifukwamwinaphazilingatererelitakhazikika ndipo inu mungalawe zoipa chifukwa chakutsekereza njira ya Mulungu ndipo chanu chidzakhala chilango chachikulu
- Musagulitse lonjezo la Mulungu ndi mtengo wochepa. Ndithudi zinthu zimene zili kwa Mulungu ndi zabwino inu mukadadziwa
- Zinthuzimenezilindiinundizakuthakomazimenezili kwa Mulungu ndi zosatha. Ndithudi Ife tidzalipira anthu omwe amapirira malipiro abwino kwambiri molingana ndi zimene anali kuchita
- Aliyense amene achita zabwino, mwamuna kapena mkazi, ndipo ali okhulupirira, ndithudi, tidzampatsa moyo wabwino ndipo tidzawalipira malipiro abwino kwambiri molingana ndi zimene ankachita
- Motero ukafuna kuwerenga Korani, pempha chitetezo cha Mulungu kuti akuteteze kwa Satana wotembereredwa
- Ndithudi! Satana alibe mphamvu pa anthu okhulupirira amene amaika chikhulupiliro chawo mwa Ambuye wawo
- Mphamvu zake zili pa okhawo amene amapalana naye ubwenzi, ndiponso iwo amene amapembedza milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni
- Ndipo pamene Ife tisintha Vesi m’malo mwa linzake, Mulungu yekha amadziwa kwambiri zimene akuvumbulutsa. Iwo amati, “Iwe ndiwe wabodza.” Iyayi koma ambiri mwa iwo sadziwa
- Nena, “Ndi Mzimu Woyera umene wabweretsa chivumbulutso kuchokera kwa Ambuye wako mwachoonadi, ndi cholinga choti chiwalimbikitse anthu amene amakhulupirira, ndi malangizo ndiponso nkhani yabwino kwa Asilamu.”
- Ndithudi Ife tikudziwa kuti iwo amanena kuti, “Ndi munthu amene akumuphunzitsa iye.” Koma munthu amene amamuganizira, kuti ndiye amene anamuphunzitsa amayankhula chiyankhulo cha chilendo pamene Korani iyi ndi chiyankhulo cha Chiarabu chomveka
- Ndithudi! Iwo amene sakhulupirira mawu a Mulungu, Mulungu sadzawatsogolera ndipo iwo adzapeza chilango chowawa
- Ndithudi ndi okhawo amene sakukhulupirira mavesi a Mulungu amene amapeka bodza ndipo iwo ndi abodza
- Aliyense amene sakhulupirira Mulungu pambuyo pokhulupirira kupatula amene wakakamizidwa koma mtima wake uli wokhazikika ndi chikhulupiriro, koma iwo amene ayamba kusakhulupirira mu mtima mwawo, mkwiyo wochokera kwa Mulungu udzadza pa iwo ndipo adzapeza chilango chachikulu
- Ichi ndi chifukwa chakuti anthu otero adakonda moyo wa padziko lapansi kwambiri kuposa moyo umene uli nkudza. Ndipo Mulungu satsogolera anthu osakhulupirira
- Amenewa ndiwo amene mitima yawo, makutu awo ndi maso awo atsekedwa ndi Mulungu ndipo ndi osamva ayi
- Palibe chikayiko kuti iwo, m’moyo umene uli nkudza, sadzapeza chilichonse ndipo adzakhala olephera
- Ndipo, ndithudi, Ambuye wako, kwa iwo amene adasamuka kwawo pambuyo povutitsidwa ndipo apitirira kumenya nkhondo ndi kupirira, ndithudi, Ambuye wako, pambuyo pa zimenezo ndi Wokhululukira kwambiri ndiponso wachisoni
- Pa tsiku limene munthu aliyense adzadza kudzadzidandaulira yekha, ndipo aliyense adzalandira dipo lolingana ndi ntchito zake ndipo iwo sadzaponderezedwa ayi
- Ndipo Mulungu wapereka chitsanzo cha Mzinda umene udali wabata ndi wamtendere, chakudya chake chidali chambiri chimene chimachokera kumbali zosiyanasiyana koma anthu ake adakana zokoma za Mulungu. Kotero Mulungu adaulawitsa Mzindawo vuto la njala ndi mantha chifukwa cha zimene iwo amachita
- Ndithudi! Kudadza kwa iwo Mtumwi wa mtundu wawo koma iwo adamukana. Choncho chilango chathu chidawapeza iwo ali kuchita zoipa
- Motero idyani zinthu zabwino ndi zololedwa zimene Mulungu wakupatsani inu. Ndipo thokozani chisomo cha Mulungu ngati ndiye yekha amene mumapembedza
- Iye wakuletsani kudya zinthu zofa zokha, liwende, nyama ya nkhumba, ndiponso nyama iliyonse imene yaphedwa m’dzina la mulungu wina wosati Mulungu mmodzi yekha. Koma ngati wina akakamizidwa kudya zina za izi, osati mofuna yekha kapena mofuna kuphwanya malamulo, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira ndi wachifundo chosatha
- Ndipo musanene bodza ndi malirime anu ponena kuti, “Ichi ndi chololedwa kapena ichi ndi choletsedwa” ndi cholinga chomupekera Mulungu bodza. Ndithudi amene akupekera Mulungu bodza sadzapambana
- Chisangalalo cha kanthawi kochepa kwambiri koma iwo adzapeza chilango chowawa
- Ife tidawaletsa Ayuda kudya zakudya zimene takufotokozera kale. Ife sitidawapondereze ayi koma iwo adadzipondereza okha
- Ndipo, ndithudi! Ambuye wako, kwa anthu amene amachita zoipa mosazindikira ndi kulapa pambuyo pake ndikuchita zabwino, ndithudi, Ambuye wako pambuyo pa zimenezo ndi wokhululukira ndi wachisoni
- Ndithudi! Abrahamu adali chitsanzo cha makhalidwe abwino, wokhulupirika kwa Mulungu ndiponso wangwiro. Iye sadali mmodzi wa anthu opembedza mafano
- Iye adali wothokoza chisomo cha Mulungu ndipo Iye adamusankha iye ndi kum’tsogolera ku njira yoyenera
- Ndipo Ife tidamupatsa zabwino m’moyo uno ndipo iye, m’moyo umene uli nkudza, adzakhala pakati pa anthu olungama
- Motero Ife tavumbulutsa kwa iwe kuti, “Tsatira chipembedzo cha Abrahamu amene sanali mmodzi wopembedza mafano.”
- Tsiku la sabata lidakhazikitsidwira anthu amene adali kutsutsana pa za tsikuli ndipo ndithudi Ambuye wako adzaweruza zonse zimene anali kukangana pa tsiku lachiweruzo
- Itanira anthu ku njira ya Ambuye wako mwanzeru ndi ulaliki wabwino. Tsutsana nawo m’njira yabwino. Ndithudi Ambuye wako amadziwa bwinobwino onse amene amasochera ku njira yake, ndiponso Iye amawadziwa bwino bwino iwo amene atsogozedwa
- Ngati inu muli kulanga, langani monga momwe inu mwalangidwira. Koma ngati mutapirira, zimenezo ndi zabwino kwa anthu opirira
- Khala opirira ndipo kupirira kwako ndi chifukwa cha Mulungu ndipo usadandaule za iwo ndiponso usakhale obanika chifukwa cha chiwembu chawo
- Ndithudi Mulungu ali ndi iwo amene amamuopa Iye ndipo amachita ntchito zabwino