15.The Rock
- Alif Lam Ra. Awa ndi mavesi a Buku, ndipo ndi Korani yofotokoza bwino
- Mwina iwo amene sakhulupirira adzafuna kuti akadakhala Asilamu
- Alekeni kuti adye, ndi kuti asangalale ndipo alekeni kuti atangwanike ndi chikhulupiriro chabodza. Iwo adzadziwa posachedwapa
- Ndipo Ife sitinaonongepo mzinda wina uliwonse, kupatula pamene nthawi yake itakwana
- Anthu sangathe kufulumizitsa chionongeko chawo kapena kuchichedwetsa ayi
- Iwo amati, “Iwe, amene Korani yavumbulutsidwa kwa iwe! Ndithudi ndiwe munthu wa misala.”
- “Bwanji siutibweretsera angelo ngati iweyo uli mmodzi mwa onena zoona?”
- Ife sitimatsitsa pansi angelo, kupatula ndi choonadi ndipo zitatero iwo sadzapatsidwa nthawi
- Ndithudi ndife amene tidatsitsa Korani ndipo, ndithudi, Ife ndife amene tidzaiteteza
- Ndithudi Ife tidatumizapo, iwe usanadze, Atumwi ena pakati pa mibadwo yakale
- Ndipo sikunadze kwa iwo Mtumwi, amene iwo sanamuchite chipongwe
- Kotero timalowetsa chisokonezo m’mitima ya anthu ochita zoipa
- Iwo sangakhulupirire mu uthenga wa Korani ndipo ndi chizolowezi cha anthu amene adalipo kale
- Ndipo ngati Ife tikadatsekula khomo lakumwamba, iwo ndi kumakwera kumwamba mosalekeza
- Iwo akadakanabe kuti, “Maso athu athobwa. Ndithudi ife talodzedwa.”
- Ndithudi Ife taika nyenyezi zikuluzikulu kumwamba ndipo tazikongoletsa kuti zizikondweretsa anthu oyang’ana
- Ndipo tawateteza malo a kumwamba kwa Satana wotembereredwa
- Kupatula iye amene amamvetsera mwakuba, iye amatsatiridwa ndi malawi a moto
- Ife tidatambasula dziko lapansi ndi kuikamo mapiri ndipo tameletsa mu ilo zinthu zosiyanasiyana chilichonse chili ndi muyeso wake
- Ndipo takupatsani mu ilo njira zopezela chakudya chanu ndi cha izo zimene inu simungathe kuzidyetsa
- Palibe chilichonse, chimene nkhokwe yake siili ndi Ife ndipo sititumiza kupatula m’muyeso wodziwika
- Ndipo Ife timatumiza mphepo yobereketsa ndipo timatsitsa madzi kuchokera kumwamba ndipo timakupatsani kuti mumwe; ndipo inu si ndinu osunga nkhokwe zake
- Ndipo, ndithudi, Ife ndife amene timapereka moyo ndi imfa ndipo zinthu zonse ndi zathu
- Ndipo, ndithudi, Ife timadziwa onse amene adalipo kale inu musanadze ndipo timadziwa mibadwo yanu yatsopano ndi iwo amene adzadza m’tsogolo
- Ndipo, ndithudi, Ambuye wako adzasonkhanitsa onse pamodzi. Zoonadi Iye ndi Wanzeru ndi Wodziwa chilichonse
- Ndipo, ndithudi, Ife tidamulenga munthu kuchokera ku dothi lotulutsa mawu, losinthidwa m’matope akuda osalala
- Tidapanga mtundu wa majini poyamba kuchokera ku mphepo ya moto
- Ndipo pamene Ambuye wako adati kwa angelo, “Ine ndilenga munthu kuchokera ku dothi lotulutsa mawu losinthidwa matope akuda osalala.”
- “Motero ndikatha kumukonza ndi kuuzira mpweya umene ndidalenga chifukwa cha iye ndipo nonse gwadani kumulambira iye.”
- Motero Angelo onse adagwada ndi kumulambira
- Kupatula Satanaadakanakukhalammodzimwaolambira
- Mulungu adati, “oh iwe Satana! Kodi ndi chifukwa chiyani siuli pamodzi ndi olambira?”
- Satana adati, “Ine sindingagwadire munthu amene Inu mwamulenga kuchokera ku dothi lotulutsa mawu losinthidwa matope akuda osalala.”
- Mulungu adati: “Motero choka kuno chifukwa ndithudi iwe ndiwe wotembereredwa.”
- Ndipo, ndithudi, temberero lidzakhala pa iwe mpaka pa tsiku lachiweruzo.”
- Satana adati, “oh Ambuye wanga! Bandisungani mpaka patsiku louka kwa akufa.”
- Mulungu adati, “Ndithudi iwe uli m’gulu la anthu amene apatsidwa nthawi.”
- “Mpaka pa nthawi ya tsiku lotsimikizika.”
- Satana adati, “Oh Ambuye wanga! Popeza Inuyo mwandisocheretsa ine, ndithudi, ndidzawasalalitsira njira yautchimo anthu onse padziko lapansi, ndithudi onse ndidzawasocheretsa
- Kupatula akapolo anu osankhidwa amene ali pakati pawo.”
- Mulungu adati, “Imeneyi ndiyo njira imene idzalondola mwachindunji kwa Ine.”
- “Ndithudi iwe siudzakhala ndi mphamvu pa akapolo anga, kupatula anthu ochita zoipa amene amakutsatira iweyo.”
- “Ndipo, ndithudi, Gahena ndi malo olonjezedwa kwa iwo onse.”
- “Iyo ili ndi makomo asanu ndi awiri, ndipo chipata chilichonse chidzakhala ndi anthu ake olowapo.”
- “Ndithudi! Onse oopa Mulungu adzakhala m’kati mwa minda ndi m’kati mwa a kasupe.”
- “Lowanimo mwamtendere mopanda mavuto.”
- “Ndipo Ife tidzachotsa m’mitima yawo mkwiyo uliwonse kuti akhoza kukhala pachibale ndi kupumula m’mipando yawofowofo moyang’anizana.”
- “Ndipo iwo sadzatopa kumeneko ndipo sadzafunsidwa kuti achoke ku Paradiso.”
- Auze akapolo anga kuti ndithudi Ine ndimakhululukira ndipo ndine wachisoni
- Ndiponso kuti chilango changa, ndithudi, ndi chilango chowawa koposa
- Auze za alendo a Abrahamu
- Pamene iwo adadza kwa iye ndi kumuuza kuti, “Mtendere ukhale kwa iwe.’ Koma iye adawayankha kuti, “Ndili ndi mantha ndi inu.”
- Iwo adati, “Usaope! Ife tadza kwa iwe ndi nkhani yabwino ya mwana wamwamuna amene adzakhala wodziwa zambiri.”
- Iye adati, “Kodi inu muli kudzandiuza nkhani yabwino pamene ine nditakalamba kale? “Kodi nkhani yanu ndi yotani?”
- Iwo adati, “Ife tili kukuuza nkhani yabwinoyi mwachoonadi. Kotero usakhale wotaya mtima.”
- Iye adati, “Ndani amene angataye mtima ndi chifundo cha Mulungu, kupatula osochera?”
- Iye adatinso, “Kodi cholinga chanu ndi chiyani, inu otumidwa?”
- Iwo adati, “Ife tatumidwa kwa anthu oipa.”
- “onse kupatula anthu otsatira Loti okha. Ife, ndithudi, tidzawapulumutsa iwo okha.”
- “Kupatula mkazi wake amene ife talamulidwa kuti akhalire m’mbuyo pamodzi ndi iwo amene anali kukhalira m’mbuyo.”
- Ndipo pamene a Kazembe athu adadza ku nyumba ya Loti
- Loti adati, “Ndithudi inu ndinu anthu omwe sindikudziwani.”
- Iwo adati, “Iyayi. Ife takubweretsera iweyo zinthu zimene iwo anali kukayika.”
- “Ndipo Ife tadza ndi choonadi kwa iwe ndipo, ndithudi, ife ndife onena zoona.”
- “Motero choka ndi abale ako pakati pa usiku, iwe uziyenda pambuyo pawo ndipo usalole wina aliyense kuti atembenuke. Kapita kumene walamulidwa kupita.”
- Ndipo tidamuuza lamulo ili kuti mizu ya iwo idzazulidwa m’mawa
- Ndipo anthu a mu Mzinda adadza ali osangala
- Iye adati, “Ndithudi! Awa ndi alendo anga motero musandichititse manyazi ayi.”
- “opani Mulungu ndipo musandipangitse manyazi.”
- Iwo adati, “Kodi ife sitidakuletse kuti uzichereza alendo?”
- Iye adati, “Awa ndi ana anga a aakazi; akwatireni ngati inu mufunadi kutero.”
- Ndithudi pali moyo wako! Iwo chifukwa chakuledzera anali kuyenda mwakhungu
- Ndipo chilango chidawapeza pamene dzuwa linkatuluka
- Ndipo Ife tidaononga (mizinda yawo) zapansi kukhala pamwamba ndipo tidawagwetsera mvula ya miyala ya moto
- Ndithudi! Mu izi muli zizindikiro kwa anthu omvetsa
- Ndipo, ndithudi, iyo ili m’mphepete mwa msewu umene umapitidwa
- Ndithudi! Muizimulizizindikirokwaanthuokhulupirira
- Ngakhale anthu okhala m’nkhalango nawonso anali ochimwa
- Motero Ife tidawalanga. Ndipo iwo ali pamalo poonekera
- Ndipo, ndithudi, anthu a ku Hijr adakana Atumwi
- Ndipo Ife tidawapatsa zizindikiro zathu koma iwo adazikana
- Ndipo iwo anali kukumba mapiri kukhala nyumba zawo ndipo anali kukhala mosaopa
- Phokoso la chilango lidafika kwa iwo m’mawa
- Ndipo sizidawathandize zonse zimene anali kuchita
- Ndipo Ife sitidalenge kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo kupatula ndi choonadi. Ndithudi popanda chikayiko tsiku lachiweruzo lidzadza; kotero akhululukireni, kukhululuka kwabwino
- Ndithudi Ambuye wako ndi Namalenga ndi wodziwa zinthu zonse
- Ndipo, ndithudi, Ife tidakupatsa mavesi asanu ndi awiri amene amanenedwa kawirikawiri ndi Korani yolemekezeka
- Usamayang’ane mwanjiru zinthu zokoma zimene tawapatsa ena a iwo kapena kumamva chisoni pa izo. Ndipo onetsani chifundo kwa anthu okhulupirira
- Ndipo Nena, “Ine ndine Mchenjezi”
- Monga tidatumiza kwa amene amagawanitsa
- Amene apanga Buku la Korani kukhala magawo awiri
- Kotero, pali Ambuye wako, tidzawafunsa
- Pa zonse zimene anali kuchita
- Motero lalikira poyera zonse zimene walamulidwa, ndipo choka pakati pa osakhulupirira
- Ndithudi Ife tidzakuteteza kwa onyoza
- Iwo amene amatumikira mulungu wina kuonjezera pa Mulungu weniweni iwowo adzadziwa
- Ndithudi Ife tilikudziwakutizimakupweteka mumtima mwako zinthu zimene amanena
- Motero lemekeza Ambuye wako ndipo khala mmodzi wa iwo amene amagwada pomulemekeza Iye
- Ndipo pembedza Ambuye wako mpaka pamene ola lotsimikizidwa likupeza