14.Abraham
- Alif Lam Ra. Tavumbulutsa Buku lino kwa iwe kuti uwatulutse anthu kuchoka kumdima ndi kupita kowala, kunjira ya Mwini Mphamvu, ndi Mwini kuyamikidwa mwachifuniro cha Ambuye wawo
- Mulungu ndiye Mwini wa zonse zimene zili kumwamba ndi dziko lapansi. Tsoka kwa anthu osakhulupirira chifukwa cha chilango chowawa
- Iwo ameneamakondamoyounokuposamoyoumeneulinkudza ndipo amaletsa kutsatira njira ya Mulungu ndipo amafuna za chinyengo mu izo, iwo ndi wosochera kwambiri
- NdipoIfesitinatumizeMtumwikupatulam’chilankhulo cha anthu ake ndi cholinga chakuti akhoza kuwafotokozera momveka. Ndipo Mulungu amasocheretsa aliyense amene Iye wamufuna ndi kutsogolera amene wamufuna. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndiponso Mwini luntha
- Ndithudi Ife tidamutuma Mose ndi zizindikiro zathu ndi kunena kuti, “Atulutse anthu ako kuchoka ku mdima ndi kupita nawo kowala ndipo uwakumbutse za masiku a Mulungu.” Ndithudi mu izi muli zizindikiro kwa aliyense wopirira ndi wothokoza
- Ndipo pamene Mose adawauza anthu ake kuti, “Kumbukirani ubwino wa Mulungu kwa inu pamene Iye adakupulumutsani inu kwa anthu a Farawo, amene adakupatsani inu mavuto aakulu ndipo anali kupha ana anu aamuna ndi kusiya ana anu aakazi amoyo, ndithudi, zimenezi zidali mayesero aakulu kuchokera kwa Ambuye wanu.”
- Ndipo pamenepo Ambuye wanu adalengeza kuti, “Ngati inu muthokoza, Ine ndidzakupatsani zinthu zambiri koma ngati simuthokoza, ndithudi, chilango changa ndi chokhwima kwambiri.”
- Ndipo Mose adati “Ngati inu simukhulupirira, inu ndi wonse amene ali padziko lapansi, ndithudi, Mulungu ndi wolemera ndipo ndi Mwini kuyamikidwa.”
- Kodi inu simunamve nkhani za anthu a Nowa, Aad, ndi Thamoud omwe adalipo inu musanadze? Ndiponso za iwo amene adadza pambuyo pawo? Palibe adziwa za iwo kupatula Mulungu yekha. Atumwi awo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka koma iwo adatseka pakamwa pawo ndi manja awo ndipo adati, “Ndithudi ife sitikhulupirira mu zimene mwatumidwa, ndithudi ife tili ndi chikaiko pazimene mukutiitanira.”
- Atumwi awo adati, “Chiyani! Kodi pangakhale chikayiko pa Mulungu, Namalenga wa kumwamba ndi dziko lapansi? Iye akukuitanani kuti akukhululukireni machimo anu ndi kukusungani mpaka pa nthawi yomwe idaikidwa.” Iwo adati, “Inu simuli ena, koma anthu ngati ife. Inu mufuna kutiletsa zimene makolo athu anali kupembedza. Tipatseni umboni weniweni wooneka.”
- Atumwi awo adati kwa iwo, “Ife tili anthu ngati inu nomwe koma Mulungu amakhazikitsa chisomo chake pa ena mwa akapolo ake amene Iye wawasankha. Ife sitingathe kukupatsani chizindikiro pokhapokha ngati Mulungu afuna. Mwa Mulungu yekha onse okhulupirira aike chikhulupiriro chawo.”
- “Kodi ife tingalekerenji kuika chikhulupiriro chathu mwa Mulungu pamene Iye watitsogolera kunjira zathu? Ndithudi ife tidzapirira ku mazunzo amene mungatipatse ife ndipo mwa Mulungu, onse amene amakhulupirira aike chikhulupiriro chawo.”
- Ndipo anthu osakhulupirira adati kwa Atumwi awo, “Ndithudi ife tidzakuthamangitsani m’dziko lathu kapena mubwerere kuchipembedzo chathu.” Koma Ambuye wawo adawalangiza iwo nati, “Ndithudi tidzaononga anthu ochita zoipa.”
- “Ndipo, ndithudi, tidzakukhazikitsani m’dziko pambuyo pa iwo. Chimenechi ndi cha iye amene aopa kudzaima pamaso panga ndipo amaopa chenjezo langa.”
- Ndipo iwo adafunafuna kupambana ndi chithandizo ndipo aliyense wamwano, wamtudzu ndi wolamula mwankhanza, adatayika ndi kuonongeka
- Kutsogolo kwake kuli Gahena ndipo adzamwetsedwa madzi owira ndi othukusira
- Iye, mwa unyizi, adzangopsontha koma sadzamwa ngakhale ndi pang’ono pomwe, ndipo imfa idzadza kuchokera kumbali zonse koma iye sadzafa ayi ndipo chilango chowawa chidzakhala kutsogolo kwake
- Fanizo la iwo amene sakhulupirira mwa Ambuye wawo ndi lakuti ntchito zawo zili ngati phulusa limene liulutsidwa ndi mphepo pa tsiku la mphepo ya mkuntho. Iwo sadzapeza china chilichonse kuchokera ku zinthu zimene ankachita. Ndipo kumeneku ndiko kusochera kwenikweni
- Kodi iwe siuona kuti Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi? Atafuna Iye akhoza kukuchotsani ndi kubweretsa zolengedwa zatsopano
- Kwa Mulungu zoterezo si zovuta ayi
- Ndipo onse adzaonekera pa maso pa Mulungu. Ndipo anthu ochepa mphamvu adzanena kwa iwo amene anali a mwano kuti, “Ndithudi ife tinali kutsatira inu. Kodi inu mungatiteteze ife ku chilango cha Mulungu?” Iwo adzati, “Mulungu akadatitsogolera ife tikadakutsogolerani inu. Ndi chimodzimodzi kwa ife kaya tikalipa kapena tipirira, tilibe kothawira.”
- Ndipo Satana adzanena, pamene chiweruzo chaperekedwa, kuti: “Ndithudi Mulungu adakulonjezani lonjezo loona. Inenso ndidakulonjezani koma ndidakusocheretsani. Ine ndidalibe udindo pa inu, kupatula kuti ndidangokuitanani ndipo inu mudandiyankha. Tsopano musandidzudzule ine ayi koma dzidzudzuleni nokha. Ine sindingathe kukuthandizani ndipo inu simungandithandize ine. Ndithudi ine ndakana kundisakaniza kwanu ndi Mulungu kumene munali kuchita.” Zoonadi ochita zoipa adzalangidwa zedi
- Ndipo iwo amene adakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzalowetsedwa ku minda yothiriridwa ndi madzi yam’mitsinje ndipo adzakhala komweko mpaka kalekale ndi chilolezo cha Ambuye wawo. Kulonjerana kwawo kudzakhala “Mtendere”
- Kodi simuona mmene Mulungu amaperekera chitsanzo? Liwu labwino lili ngati mtengo wabwino umene mizu yake ndi yokhazikika ndi nthambi zake zifika mlengalenga
- Umene umabereka zipatso nyengo iliyonse ndi chilolezo cha Ambuye wake ndipo Mulungu amapereka mafanizo kwa anthu ndi cholinga chakuti azikumbukira
- Ndipo chitsanzo cha liwu loipa lili ngati mtengo woipa, umene uzulidwa kuchoka ku nthaka ndipo ulibe mizu ina iliyonse
- Mulungu adzalimbikitsa anthu okhulupirira ndi liwu lokhazikika m’moyo uno ndi m’moyo umene uli nkudza. Ndipo Mulungu adzasocheretsa ochita zoipa ndipo Mulungu amachita zimene Iye afuna
- Kodi siunaone iwo amene amasinthanitsa chisomo cha Mulungu ndi kusakhulupirira ndi kuwakankhizira anthu awo kuti akhale m’nyumba ya mazunzo
- Ndipo Gahena, m’mene iwo akalowe, ndi malo oipa kukhalako
- Iwo akhazikitsa milungu yabodza kuti ikhale yofanana ndi Mulungu ndi cholinga chosokoneza anthu ku njira yake. Nena, “Basangalalani! Koma, ndithudi, kokafikira kwanu ndi ku Moto.”
- Auze akapolo anga, amene ali okhulupirira kuti apitirize mapemphero ndi kupereka zothandiza osauka kuchokera ku zimene tawapatsa mseri ndi pooneka, lisanafike tsiku limene sikudzakhala kukambirana kapena kuchita ubwenzi
- Ndi Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo amagwetsa madzi kuchokera kumwamba amene amameretsa zipatso kuti zikhale chakudya chanu. Iye adapanga zombo kuti muzizigwiritsa ntchito; kuti zikhoza kuyenda pa nyanja ndi chilolezo chake ndipo adapanga mitsinje kuti izikutumikirani
- Ndipo adalenga dzuwa ndi mwezi, zimene zimayenda mokhazikika m’misewu yawo kuti muzigwiritsa ntchito. Ndipo adalenga usiku ndi usana kuti muziugwiritsa ntchito
- Ndipo Iye adakupatsani zonse zimene mudamupempha ndipo ngati inu muwerenga zokoma za Mulungu inu simungathe kuziwerenga zonse. Zoonadi munthu ndi wosayamika ndi wosakhulupirira
- Ndipo pamenepo Abrahamu adati, “oh Ambuye wanga! Upangeni uwu kukhala Mzinda wamtendere ndipo nditetezeni ine ndi ana anga kuti tisapembedze mafano.”
- “oh Ambuye wanga! Ndithudi mafano asocheretsa anthu ambiri. Koma iye amene anditsatira ine ndithudi adzakhala wa ine. Koma aliyense amene sandimvera ine, komabe Inu ndinu okhululukira ndi wachisoni chosatha.”
- “Oh Ambuye wathu! Ine ndakhazika ena mwa ana anga m’dambo lopanda zomera limene lili pafupi ndi Nyumba yanu yoyera, Oh Ambuye wathu, kuti iwo azipemphera. Motero dzazani mitima ya anthu ndi chikondi kuti awaonetsere iwo ndipo apatseni iwo zipatso kuti akhale othokoza.”
- “Oh Ambuye wathu! Ndithudi inu mumadziwa zonse zimene timazibisa ndi zonse zimene timaulula. Palibe china pa dziko lapansi kapena kumwamba chimene chimabisika kwa Mulungu.”
- “Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu amene wandipatsa ine Ishimayeli ndi Isake ku ukalamba wanga. Ndithudi! Ambuye wanga ndiye amene amamva mapemphero onse.”
- “oh Ambuye wanga! Ndipangeni ine kukhala mmodzi wopemphera ndiponso kuchokera ku ana anga. Ambuye wathu! Landirani pempho langa.”
- “Ambuye wathu! Khululukireni ine ndi makolo anga ndi onse okhulupirira pa tsiku limene zonse zidzakhazikitsidwa.”
- Usaganize kuti Mulungu sadziwa ntchito za anthu ochita zoipa koma Iye akungowasiya mpaka patsiku limene maso awo adzaona motuzuka
- Iwo adzathamanga kupita kutsogolo, makosi osololoka, mitu yokwezedwa ndi maso awo otuzuka ndipo mitima yawo idzakhala yopanda chilichonse
- Achenjeze anthu za tsiku limene chilango chidzadza pa iwo ndipo anthu ochita zoipa adzati, “Ambuye wathu tipatseni mpumulo wa kanthawi kochepa ndipo ife tidzamvera kuitana kwanu ndi kutsatira Atumwi anu.” Koma adzati kwa iwo, “Kodi inu nthawi zina simudalumbira kuti simudzafa?”
- Inu mumakhala m’nyumba za anthu amene adachimwira miyoyo yawo pamene mumadziwa zonse zimene tidawachitira iwo. Ndipo Ife tidakuikirani chitsanzo
- Ndithudi iwo akonza chiwembu chawo ndipo chiwembu chawo chili ndi Mulungu ngakhale kuti chiwembu chawo chinali choti, chingathe kuchotsa mapiri
- Musaganize kuti Mulungu adzalephera kukwaniritsa lonjezo lake limene adapereka kwa Atumwi ake. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu ndipo amatha kulanga
- Pa tsiku limene dziko lapansi lidzasinthidwa kukhala dziko lapansi la mtundu wina, ndi kumwamba kukhala kwa tsopano, mtundu onse udzaonekera pamaso pa Mulungu, Mmodzi yekha yemwe ndi Mwini mphamvu zonse
- Pa tsiku limeneli iwe udzaona anthu osakhulupirira atamangidwa m’magoli
- Zovala zawo zidzakhala zakuda ngati phula ndi nkhope zawo zidzakutidwa ndi malawi a moto
- Kuti Mulungu alipire munthu aliyense pa zimene adachita. Ndithudi Mulungu ndi wachangu powerengera
- Uwu ndi uthenga kwa anthu onse kuti achenjezedwe nawo ndi kudziwa kuti Mulungu ndi mmodzi yekha ndi kuti anthu anzeru akumbukire